Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Anacita Zinthu Molimba Mtima, Modzipeleka, Komanso Mokangalika

Anacita Zinthu Molimba Mtima, Modzipeleka, Komanso Mokangalika

Yehova analamula Yehu kuti akawononge anthu onse a m’nyumba ya mfumu yoipa Ahabu (2 Maf. 9:6, 7; w11 11/15 3 ¶2)

Mosazengeleza, Yehu anapha Mfumu Yehoramu (mwana wa Ahabu) na Mfumukazi Yezebeli (mkazi wa Ahabu) (2 Maf. 9:22-24, 30-33; w11 11/15 4 ¶2-3; onani chati yakuti “‘Nyumba Yonse ya Ahabu Idzafafanizidwa’—2 Maf. 9:8”)

Yehu anatsiliza nchito imene anapatsidwa, ndipo anaicita molimba mtima, modzipeleka, komanso mokangalika (2 Maf. 10:17; w11 11/15 5 ¶3-4)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Ningatengele bwanji citsanzo ca Yehu pogwila nchito imene tinapatsidwa yochulidwa pa Mateyu 28:19, 20?’