Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

“N’cifukwa Ciyani Akhristu Ayenela Kuyesetsa Kuwonjezela Utumiki Wawo?”

“N’cifukwa Ciyani Akhristu Ayenela Kuyesetsa Kuwonjezela Utumiki Wawo?”

Abale na alongo amayesetsa kupita patsogolo kuti akwanilitse zolinga zawo zauzimu, monga kucitako upainiya, utumiki wa pa Beteli, komanso kumanga nawo Nyumba za Ufumu. Kuwonjezela apo, abale amayesetsa kuti akhale oyang’anila. (1 Tim. 3:1) Koma kodi izi zitanthauza kuti Akhristu ayenela kufunitsitsa udindo kapena utumiki winawake n’colinga cakuti ena aziwalemekeza?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI N’CIFUKWA CIYANI TIYENELA KUYESETSA KUWONJEZELA UTUMIKI WATHU? (1 TIM. 3:1), KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

Kodi malemba awa aonetsa kuti ni zifukwa zitatu ziti zimatisonkhezela kuwonjezela utumiki wathu?