PHUNZILO 4
Ni Cifukwa Ciani Timafalitsa Baibulo la Dziko Latsopano?
Kwa zaka zambili, Mboni za Yehova zinali kugwilitsila nchito Mabaibo osiyana-siyana. Zinalinso kusindikiza ena ndi kuwafalitsa. Koma tinaona kuti panafunika Baibo yotembenuzidwa bwino imene ikanathandiza anthu ‘kudziŵa coonadi molondola.’ Ici ndiye cifunilo ca Mulungu kwa anthu onse. (1 Timoteyo 2:3, 4) Conco mu 1950, tinayamba kufalitsa zigao za Baibo yathu yochedwa Baibulo la Dziko la Tsopano m’cinenelo ca makono. Pano Baibo imeneyi yatembenuzidwa mokhulupilika ndi molondola m’zinenelo zopitilila 130.
Panafunika Baibo losavuta kumva. Zinenelo zimasintha m’kupita kwa nthawi, ndipo Mabaibo amakhala ndi mau oiŵalika kapena acikale amene ni ovuta kumva. Ndiponso mipukutu yolondola yakale imene sisiyana kwambili ndi mipukutu yoyambilila yapezeka. Imeneyi yathandiza kumvetsetsa Ciheberi, Ciaramu ndi Cigiriki ca m’Baibo.
Panafunika Baibo imene imafotokoza mau a Mulungu mokhulupilika. Otembenuza Baibo alibe ufulu wosintha malemba ouzilidwa a Mulungu. Iwo afunika kutsatila mokhulupilika zimene zinalembedwa m’mipukutu yoyambilila. Ngakhale ni conco, otembenuza ambili sagwilitsila nchito dzina la Mulungu, lakuti Yehova, m’Malemba Opatulika.
Panafunika Baibo imene imalemekeza Mlembi wake. (2 Samueli 23:2) M’mipukutu ya Baibo yakale kwambili, dzina la Yehova limapezeka pafupi-fupi 7,000, malinga ndi citsanzo cimene cili pansi apa. Conco, dzina la Yehova analibwezeletsa m’malo ake onsewa mu Baibulo la Dziko Latsopano. (Salimo 83:18) Baibo imeneyi imasangalatsa kuŵelenga cifukwa imafotokoza momveka bwino maganizo a Mulungu. Izi zili conco cifukwa cakuti kwa zaka zambili panacitika nchito yaikulu yofuna-funa maumboni osiyana-siyana. Kaya muli ndi Baibulo la Dziko Latsopano kapena mulibe, tikulimbikitsani kukhala ndi cizoloŵezi coŵelenga Mau a Yehova tsiku ndi tsiku.—Yoswa 1:8; Salimo 1:2, 3.
-
N’cifukwa ciani tinaona kuti panali kufunika Baibo yotembenuzidwa m’njila yatsopano?
-
Kodi n’cizoloŵezi cotani cimene munthu afunika kukhala naco kuti aphunzile cifunilo ca Mulungu?