‘Khalanibe M’cikondi ca Mulungu’

Bukuli lidzakuthandizani kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo mu umoyo wanu ndi kuti mukhalebe m’cikondi ca Mulungu.

Kalata Yocokela Ku Bungwe Lolamulila

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova likulimbikitsa onse amene amakonda Yehova kutengela citsanzo ca Yesu, amene anakhalabe m’cikondi ca Atate wake.

NKHANI 1

Izi Ndi Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”

M’mau acidule, Baibulo lifotokoza mmene tingaonetsele kuti timakonda mulungu.

NKHANI 2

Mmene Mungasungile Cikumbumtima Cabwino?

Kodi n’zotheka kukhala na cikumbumtima coyela koma codetsedwa m’maso mwa Mulungu?

NKHANI 3

Kondani Anthu Amene Mulungu Amakonda

Yehova amacita kusankha anthu okhala nawo paubwenzi ifenso tifunika kucita cimodzi-modzi.

NKHANI 4

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kulemekeza Ulamulilo?

Malemba amatiuza mbali zitatu paumoyo pamene Yehova amatipempha kulemekeza ulamulilo wa ena.

NKHANI 5

Mmene Tingakhalile Olekana ndi Dziko

Mau a Mulungu amafotokoza zinthu zisanu zimene tifunika kupewa kuti tilekane ndi dziko.

NKHANI 6

Mmene Mungasankhile Zosangulutsa Zabwino

Mafunso atatu angakuthandizeni kusankha mwanzelu.

NKHANI 7

Kodi Mumalemekeza Moyo Mmene Mulungu Amaulemekezela?

Kodi pali zina zofunika kusamala nazo kupatula pa kupha munthu?

NKHANI 8

Mulungu Amakonda Anthu Oyela

Baibulo lingakuthandizeni kupewa zinthu zimene zingakudetseni m’maso mwa Yehova.

NKHANI 9

“Thaŵani dama”

Caka ciliconse, Akristu ambili amacita dama. Mungapewe bwanji kukoledwa m’msampha umenewu?

NKHANI 10

Cikwati Ndi Mphatso Yocokela kwa Mulungu Wacikondi

Mungakonzekele bwanji cikwati ca cipambano? Ngati muli kale pabanja, mungatani kuti banja lanu likhalitse?

NKHANI 11

‘Cikwati Cikhale Colemekezeka’

Kudzifunsa mafunso 6 kungakuthandizeni kulimbitsa cikwati canu.

NKHANI 12

Lankhulani Mau “Olimbikitsa”

Mau angafooketse ena kapena kuwalimbikitsa. Onani mmene mungaseŵenzetsele mphatso yolankhula mogwilizana ndi cifunilo ca Yehova.

NKHANI 13

Zikondwelelo Zimene Mulungu Amadana Nazo

Zikondwelelo ndi maholide zimene zingaoneke monga zilemekeza Mulungu m’ceni-ceni zimam’khumudwitsa.

NKHANI 14

Citani Zinthu Zonse Moona Mtima

Tisanacite zinthu moona mtima ndi ena, pali sitepu imene tiyenela kutenga.

NKHANI 15

Sangalalani Cifukwa Cogwila Nchito Yanu Mwakhama

Mayankho a mafunso asanu angakuthandizeni kudziŵa kaya kulandila kapena kukana nchito ina yake.

NKHANI 16

Tsutsani Mdyelekezi ndi Zocita Zake Zacinyengo

Timazindikila mphamvu za Satana, koma sitimuopa. Cifukwa ciani?

NKHANI 17

“Dzilimbitseni Pamaziko a Cikhulupililo Canu Coyela Kopambana”

Zinthu zitatu zimene zingakuthandizeni kulimbitsa cikhulupililo canu kuti mukhalebe m’cikondi ca Mulungu.

ZAKUMAPETO

Kodi Tiyenela Kucita Bwanji ndi Munthu Wocotsedwa?

Kodi m’pofunikiladi kupewelatu kugwilizana ndi munthu wocotsedwa?

ZAKUMAPETO

Ndi Liti Pamene Mlongo Ayenela Kuvala Cophimba Kumutu, Ndipo N’cifukwa Ciani?

Baibulo limachula zinthu zitatu zimene zingakuthandizeni kuyankha.

ZAKUMAPETO

Kucitila Saliyuti Mbendela, Kuvota ndi Kugwila Nchito Yosakhala Yausilikali

Ndi malangizo a m’Malemba ati amene angakuthandizeni kukhala na cikumbumtima coyela pa nkhanizi?

ZAKUMAPETO

Tuzigawo twa Magazi ndi Njila Zimene Amatsatila Pocita Opaleshoni

Kutenga masitepu ocepa osavuta kungatithandize kuyang’anizana ndi zovuta za mankhwala.

ZAKUMAPETO

Kugonjetsa Cizoloŵezi Coseŵeletsa Malisece

Kodi mungacigonjetse bwanji cizoloŵezi coipa cimeneci?

ZAKUMAPETO

Zimene Baibulo Limanena pa Kulekana ndi Kupatukana

Malinga ndi zimene Baibulo limanena, ndi liti pamene munthu wolekana ndi mnzake angakwatilenso kapena kukwatiwanso?

ZAKUMAPETO

Kuthetsa Mikangano pa Zamalonda

Kodi Mkristu angatengele Mkristu mnzake ku khoti?