PHUNZILO 7
Kodi Yehova ni Mulungu Wotani?
Mukamva kuti Yehova Mulungu, n’ciyani cimabwela m’maganizo mwanu? Kodi mumaganiza kuti Mulungu ni wapamwamba kwambili, komanso wocititsa mantha, cakuti n’zosatheka ife anthu kukambilana naye? Kapena mumaganiza kuti Mulungu ni wamphamvu kwambili ndiponso ali paliponse monga mphepo? Kodi Yehovayo ali bwanji maka-maka? Mawu ake Baibo amatifotokozela za makhalidwe ake. Amatiuzanso zakuti amasamala za ife.
1. N’cifukwa ciyani sitikhoza kumuona Mulungu?
“Mulungu ndiye Mzimu.” (Yohane 4:24) Yehova alibe thupi la nyama na magazi monga lathu. Iye ni Mzimu ndipo amakhala kumwamba, ku malo amene sitingaone.
2. Kodi Yehova ali na makhalidwe abwanji?
Ngakhale kuti Yehova sitingamuone, iye ali na makhalidwe amene amakopa aja amene amam’dziŵa. Baibo imati: “Yehova amakonda cilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupilika.” (Salimo 37:28) Komanso iye “ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo,” maka-maka kwa anthu amene ali pa mavuto. (Yakobo 5:11) “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Salimo 34:18) Kodi mudziŵa kuti zocita zathu zingam’sangalatse kapena kum’khumudwitsa Yehova? Munthu amene amasankha kucita zoipa amam’khumudwitsa na kum’mvetsa cisoni. (Salimo 78:40, 41) Koma munthu wocita zabwino amam’kondweletsa.—Ŵelengani Miyambo 27:11.
3. Kodi Yehova amaonetsa bwanji kuti amatikonda?
Khalidwe lalikulu la Yehova ni cikondi. Ndiiko komwe, “Mulungu ndiye cikondi” (1 Yohane 4:8) Yehova amationetsa cikondi cake kupitila m’Baibo, komanso kupitila m’zinthu zimene analenga. (Ŵelengani Machitidwe 14:17) Mwacitsanzo, ganizilani mmene anatilengela. Anatilenga m’njila yakuti tizitha kuona kukongola kwa zinthu, kusangalala na nyimbo zabwino, komanso kumva kukoma kwa zakudya. Amafuna kuti tizikondwela nawo moyo.
KUMBANI MOZAMILAPO
Dziŵani cimene Yehova amaseŵenzetsa pocita zinthu zodabwitsa. Onaninso mmene Yehova amaonetsela makhalidwe ake abwino.
4. Mzimu woyela—mphamvu ya Mulungu yogwila nchito
Monga mmene timaseŵenzetsela manja pogwila nchito, Yehova naye amaseŵenzetsa mzimu woyela. Baibo imaonetsa kuti mzimu woyela si Mulungu ayi, koma mphamvu imene Mulungu amaiseŵenzetsa pocita zinthu. Ŵelengani Luka 11:13 komanso Machitidwe 2:17, na kukambilana mafunso aya:
-
Mulungu ‘adzatsanulila,’ kutanthauza kupungulila mzimu wake woyela pa aja amene amaupempha. Conco, kodi muganiza mzimu woyela ni Mulungu, kapena ni mphamvu ya Mulungu yogwila nchito? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?
Yehova amaseŵenzetsa mzimu woyela kuti acite zinthu zodabwitsa. Ŵelengani Salimo 33:6 komanso 2 Petulo 1:20, 21, na kukambilana funso ili:
-
Kodi mungachuleko njila ziti zimene Yehova wagwilitsa nchito mzimu wake woyela?
5. Yehova ali na makhalidwe abwino kwambili
Mose anali mtumiki wokhulupilika wa Mulungu. Ngakhale n’telo, iye anafunabe kum’dziŵa bwino Mlengi wake. Conco Mose anapempha Mulungu kuti: “Ndidziŵitseni njila zanu, kuti ndikudziŵeni.” (Ekisodo 33:13) Poyankha, Yehova anavumbulila Mose ena a makhalidwe Ake. Ŵelengani Ekisodo 34:4-6, na kukambilana mafunso aya:
-
Ni makhalidwe ake ati amene Yehova anachulila Mose?
-
Ndipo ni makhalidwe ati a Yehova amene akukopani mtima kwenikweni?
6. Yehova amasamala za anthu
Anthu a Mulungu, Aheberi, anali akapolo ku Iguputo. Kodi Yehova anali kumva bwanji poona anthu ake akuvutika? Mvetselani ODIYO na kutsatila m’Baibo yanu, apo ayi ŵelengani Ekisodo 3:1-10. Pambuyo pake kambilanani mafunso aya.
-
Kodi nkhani iyi ionetsa kuti Yehova amamva bwanji poona anthu akukumana na mavuto?—Onani vesi 7 na 8.
-
Kodi muona kuti Yehova amafunadi kuthandiza anthu, ndipo amakwanitsa kutelo? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?
7. Zacilengedwe zimaonetsa makhalidwe a Yehova
Yehova amaonetsa makhalidwe ake abwino kupitila m’zinthu zimene analenga. Tambani VIDIYO. Kenako ŵelengani Aroma 1:20, na kukambilana funso ili.
-
Ni makhalidwe ati a Yehova amene mumaona m’zinthu zimene analenga?
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Mulungu ali monga mphepo imene imapezeka pena paliponse.”
-
Nanga inu muganiza bwanji?
-
N’cifukwa ciyani mwayankha conco?
CIDULE CAKE
Yehova ni Mzimu wosaoneka. Ndipo ali na makhalidwe abwino ambili, maka-maka cikondi.
Mafunso Obweleza
-
N’cifukwa ciyani sitimatha kumuona Yehova?
-
Nanga mzimu woyela n’ciyani?
-
Kodi mungachuleko makhalidwe ati a Yehova?
FUFUZANI
Fikani pomudziŵa bwino Yehova mwa kuphunzila makhalidwe ake anayi apadela.
“Kodi Mulungu Ali na Makhalidwe Abwanji?” (Nsanja ya Mlonda Na. 1 2019)
Onani umboni woonetsa kuti Yehova sali pena paliponse.
“Kodi Mulungu Amapezeka Pena Paliponse?” (Nkhani ya pawebusaiti)
Onani cifukwa cake Baibo imachula mzimu woyela kuti ni manja a Mulungu.
Munthu wina wosaona (wakhungu) sanali kukhulupilila kuti Mulungu amasamala za iye. Onani cinapangitsa kuti asinthe maganizo ake.
“Panopa ndimaona kuti ndingathe kuthandiza ena” (Nsanja ya Mlonda, October 1, 2015)