Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 19

Kodi Mboni za Yehova ni Akhristu Enieni?

Kodi Mboni za Yehova ni Akhristu Enieni?

Ife monga Mboni za Yehova timakhulupililadi kuti ndife Akhristu enieni. Cifukwa ciyani? Tiyeni tikambilane maziko a zimene timakhulupilila, dzina limene limatipatula padela, komanso cikondi cathu kwa wina na munthu mnzake.

1. Kodi zimene a Mboni za Yehova amakhulupilila zimatsamila pa ciyani?

Yesu anati: “Mawu [a Mulungu] ndiwo coonadi.” (Yohane 17:17) Mofanana na Yesu, nthawi zonse zimene a Mboni za Yehova amakhulupilila zimatsamila pa Mawu a Mulungu. Mwacitsanzo, onani mmene acitila zimenezi kucokela kumayambililo kwa mbili yawo yamakono. M’ma 1870, kagulu ka ophunzila Baibo kanayamba kuiphunzila mozama Baibo. Iwo anakhulupililabe mfundo za m’Baibo ngakhale zinasiyana na zimene machalichi anali kuphunzitsa. Pambuyo pake, anayamba kuuzako anthu ena mfundo za m’Baibo zimenezo. a

2. N’cifukwa ciyani timanena kuti ndife Mboni za Yehova?

Yehova amacha anthu omulambila kuti ni mboni zake cifukwa iwo amakamba zoona ponena za iye. (Aheberi 11:4–12:1) Mwacitsanzo, m’nthawi zamakedzana, Mulungu anauza anthu ake kuti: “Inu ndinu mboni zanga.” (Ŵelengani Yesaya 43:10.) Yesu nayenso amachedwa “Mboni Yokhulupilika.” (Chivumbulutso 1:5) Ndiye cifukwa cake mu 1931, tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova. Ndipo timanyadila ngako kuchedwa na dzina limeneli.

3. Kodi Mboni za Yehova zimaonetsa bwanji cikondi potengela citsanzo ca Yesu?

Yesu anali kuwakonda kwambili ophunzila ake moti anakhala monga acibale ake. (Ŵelengani Maliko 3:35.) Mofananamo, Mboni za Yehova n’zogwilizana monga banja la padziko lonse. Ndiye cifukwa cake timachulana kuti m’bale kapena mlongo. (Filimoni 1, 2) Timamvelanso lamulo lakuti: “Kondani gulu lonse la abale.” (1 Petulo 2:17) Mboni za Yehova zimaonetsa cikondi cimeneci m’njila zambili, monga kuthandiza abale na alongo awo padziko lonse m’nthawi zovuta.

KUMBANI MOZAMILAPO

Phunzilani zambili zokhudza Mboni za Yehova zamakono kuti muone umboni wakuti tilidi Akhristu enieni.

Zimene Akhristu enieni amakhulupilila zimatsamila pa Baibo, ndipo iwo amauzakonso anthu ena

4. Zimene timakhulupilila zimacokela m’Baibo

Yehova ananenelatu kuti kumvetsetsa kwathu Baibo kudzawonjezeleka. Ŵelengani Danieli 12:4, na kukambilana funso ili:

  • Kodi anthu a Mulungu “adzadziŵa zinthu zambili” zotani pamene apitiliza kuphunzila Baibo?

Onani mmene kagulu ka ophunzila Baibo, kuphatikizapo Charles Russell, anafufuzila Mawu a Mulungu. Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

  • Mu vidiyo iyi, kodi Charles Russell na ophunzila Baibo anzake anali kuiŵelenga motani Baibo?

Kodi mudziŵa?

Nthawi zina, kwakhala kofunikila kuti tiwongolele zimene timakhulupilila. Cifukwa ciyani? Mwacitsanzo, dzuŵa likamatuluka zinthu zimayamba kuonekela bwino pang’ono-pang’ono. Mulungu nayenso amatithandiza pang’ono-pang’ono kumvetsa bwino Mawu ake. (Ŵelengani Miyambo 4:18.) Conco, ngakhale kuti Baibo siisintha, tikaimvetsetsa bwino timawongolela zimene timakhulupilila.

5. Timalalikila zoona ponena za Yehova

N’cifukwa ciyani tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso ili.

  • N’cifukwa ciyani dzina lakuti Mboni za Yehova n’lotiyenela?

N’cifukwa ciyani Yehova anasankha anthu kukhala mboni zake? Anatelo kuti athandize anthu kudziŵa za Mulungu woona, cifukwa pakukambidwa mabodza ambili onena za iye. Onan’koni aŵili okha a mabodza amenewo.

Zipembedzo zina zimaphunzitsa anthu awo zakuti Mulungu amafuna kuti iwo aziseŵenzetsa zifanizilo pomulambila. Kodi zimenezi n’zoona? Ŵelengani Levitiko 26:1, na kukambilana mafunso aya:

  • Malinga n’kunena kwa lemba ili, kodi Yehova amawaona bwanji mafano?

Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti Yesu ndiye Mulungu. Kodi zimenezi n’zoona? Ŵelengani Yohane 20:17, na kukambilana mafunso aya:

  • Malinga n’kunena kwa lemba ili, kodi Yesu ndiye Mulungu?

  • Kodi mukumva bwanji podziŵa kuti Yehova anatumiza Mboni zake kuti zilalikile coonadi ponena za iye na Mwana wake?

6. Timakondana wina na mnzake

Baibo imayelekezela Akhristu monga ziwalo zosiyana-siyana za thupi la munthu. Ŵelengani 1 Akorinto 12:25, 26, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Akhristu enieni ayenela kucita ciyani pamene Akhristu anzawo ali pamavuto?

  • Pa nkhani ya cikondi, kodi mwaona ciyani pakati pa Mboni za Yehova?

A Mboni za Yehova akakhala pamavuto kudela lina, a Mboni anzawo padziko lonse lapansi amagwapo mofulumila kuti athandize. Kuti muone citsanzo cimodzi, tambani VIDIYO. Pambuyo pake kambilanani funso lotsatila.

  • Poonetsana cikondi, kodi Mboni za Yehova zinathandizana bwanji kutacitika cimphepo camkuntho?

Akhristu enieni amaonetsa cikondi pothandiza ena ofunikila thandizo

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Mboni za Yehova zimasokoneza ŵanthu.”

  • Kodi muganiza izi n’zoona kapena iyai?

CIDULE CAKE

Mboni za Yehova ndizo Akhristu enieni. Lathu ni banja la olambila a padziko lonse, amene ziphunzitso zawo zimatsamila pa Baibo, ndipo timathandiza anthu kumudziŵa bwino Yehova.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova?

  • Timaonetsa bwanji kuti timakondana wina na mnzake?

  • Inu muganiza bwanji, kodi Mboni za Yehova ni Akhristu enieni?

Colinga

FUFUZANI

Onani citsanzo ca mmene Mboni za Yehova zavumbulila ziphunzitso zonyenga.

Anthu a Mulungu Amalemekeza Dzina Lake (7:08)

Pezani mayankho pa mafunso amene mungakhale nawo okhudza Mboni za Yehova.

“Mafunso Amene Amafunsidwa Kawili-kaŵili Ponena za Mboni za Yehova” (tsamba la pawebusaiti)

Stephen anatengako mbali m’zaciwawa cifukwa codana na mitundu ina. Pezani zomwe iye anaona pakati pa Mboni za Yehova zimene zinamuthandiza kusintha.

“Umoyo Wanga Unali Kuipilaipilabe” (Nsanja ya Mlonda, July 1, 2015)

a Magazini yathu yaikulu, Nsanja ya Mlonda, yakhala ikufalitsa coonadi ca m’Baibo mosasintha ciyambile m’caka ca 1879.