Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 47

Kodi Ndinu Wokonzeka Kubatizika?

Kodi Ndinu Wokonzeka Kubatizika?

Pa kuphunzila kwanu Baibo, mwadziŵa zinthu zambili zokhudza Yehova. Ngakhale n’conco, pangakhale cinthu cina cimene cikukudodometsani kuti musadzipatulile kwa Yehova na kubatizika. Nkhani ino idzafotokoza zimene zimapinga anthu ambili kuti asabatizike, na mmene mungazigonjetsele zopingazo.

1. Kodi muyenela kudziŵa zoculuka motani kuti mubatizike?

Kuti mubatizike, muyenela ‘kudziŵa coonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Izi sizitanthauza kuti muyenela kudziŵa mayankho onse pa mafunso onse a m’Baibo kuti mubatizike, ayi. Ngakhale Akhristu amene anabatizika zaka zambili kumbuyoku akali kuphunzilabe zinthu zambili m’Baibo. (Akolose 1:9, 10) Mungofunikila kudziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. Ndipo akulu mu mpingo wanu adzakuthandizani kuona ngati mwadziŵa zokwanila kuti mukabatizike.

2. Kodi muyenela kutenga masitepe ati kuti mubatizike?

Kuti mubatizike, Baibo imati “lapani ndi kutembenuka.” (Ŵelengani Machitidwe 3:19.) Izi zimatanthauza kumva cisoni kwambili pa macimo alionse amene munacita kumbuyoku, na kupempha Yehova kuti akukhululukileni. Muyenelanso kusiyilatu khalidwe loipa lililonse, komanso kukhala na umoyo wokondweletsa Mulungu. Pamwamba pa izi, muyenela kutengapo gawo pa zocitika za mpingo, mwa kupezeka pa misonkhano komanso kugwila nchito yolalikila monga wofalitsa wosabatizika.

3. N’cifukwa ciyani simuyenela kucita mantha kuti mubatizike?

Ena amaopa kuti angadzalephele kucita zimene anamulonjeza Yehova. N’zoona kuti nthawi zina mungalakwitse zinthu, monga mmene zinali kucitikila kwa amuna na akazi okhulupilika ochulidwa m’Baibo. Koma Yehova amadziŵa kuti olambila ake si anthu angwilo. (Ŵelengani Salimo 103:13, 14.) Cimene iye amafuna n’kuona kuti mumacita zimene mungakwanitse! Mukatelo adzakudalitsani. Ndipo Yehova amatitsimikizila kuti “ciliconse, sicidzatha kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu.”—Ŵelengani Aroma 8:38, 39.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani mmene mungagonjetsele ciliconse cokupingani kuti musabatizike, mwa kum’dziŵa bwino Yehova komanso kulandila thandizo lake.

4. Fikani pomudziŵa bwino Yehova

Kodi muyenela kudziŵa Yehova pa mlingo wotani kuti mubatizike? Muyenela kumudziŵa pa mlingo wakuti mwayamba kumukonda, na kucita zinthu zom’kondweletsa. Tambani VIDIYO kuti muone mmene ophunzila Baibo padziko lonse acitila zimenezi. Kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, kodi n’ciyani cinathandiza anthu ena kukonzekela ubatizo?

Ŵelengani Aroma 12:2, na kukambilanana mafunso aya:

  • Kodi muliko na cikayikilo ciliconse pa zimene Baibo imaphunzitsa, kapena zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa?

  • Ngati n’telo, kodi muyenela kucitapo ciyani?

5. Gonjetsani zimene zingakupingeni kuti musabatizike

Tikadzipatulila kwa Yehova na kubatizika, tonse timakumana na zovuta zosiyana-siyana. Kuti muone citsanzo, tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, kodi Narangerel anafunikila kugonjetsa zopinga zotani kuti atumikile Yehova?

  • Kodi kukonda kwake Yehova kunam’thandiza bwanji kugonjetsa zopingazo?

Ŵelengani Miyambo 29:25, komanso 2 Timoteyo 1:7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi n’ciyani cimatilimbikitsa kuti tigonjetse zopinga?

6. Dalilani thandizo la Yehova

Yehova adzakuthandizani kuti mupambane. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

  • Mu vidiyo imeneyi, kodi n’ciyani cinali kudodometsa wophunzila Baibo kuti abatizike?

  • Koma anaphunzila ciyani cimene cinam’limbikitsa kudalila Yehova?

Ŵelengani Yesaya 41:10, 13, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani muyenela kukhala na cidalilo kuti mukhoza kukwanilitsa lonjezo limene munapanga pa kudzipatulila kwanu?

7. Muziyamikiladi cikondi ca Yehova pa inu

Mukamaganizila kwambili za mmene Yehova amakukondelani, ciyamikilo canu cidzawonjezeleka, ndipo mudzakhala wofunitsitsa kum’tumikila kwamuyaya. Ŵelengani Salimo 40:5, na kukambilana funso ili:

  • Kodi ni madalitso a Yehova ati amene mumayamikila kwambili?

Mneneli Yeremiya anali kukonda kwambili Yehova komanso mawu ake. Ndipo anayamikila kwambili mwayi umene anali nawo wokhala mtumiki wake. Iye ananena kuti: “Mawu anu amandikondweletsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimachedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu.” (Yeremiya 15:16) Yankhani mafunso aya:

  • N’cifukwa ciyani uli mwayi wapadela kukhala Mboni ya Yehova?

  • Kodi mukufunadi kubatizika na kukhala Mboni ya Yehova?

  • Kodi pali cimene cikukulepheletsani kucita zimenezi?

  • Muganiza kuti muyenela kucita ciyani kuti mukakwanilitse colinga canu ca kubatizika?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nikayikila ngati ningakwanitse zonse zofunikila nikabatizika.”

  • Kodi inunso muona conco?

CIDULE CAKE

Yehova angakuthandizeni kugonjetsa ciliconse cokupingani kuti musabatizike.

Mafunso Obweleza

  • Kodi muyenela kudziŵa zoculuka motani za m’Baibo kuti mubatizike?

  • Kodi muyenela kupanga masinthidwe otani kuti mubatizike?

  • N’cifukwa ciyani simuyenela kulola mantha kukubwezani m’mbuyo?

Colinga

FUFUZANI

Onani zifukwa zimene muyenela kupangila cisankho cakuti mukabatizike.

“Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?” (Nsanja ya Mlonda, March 2020)

Onani mmene mungagonjetsele zopinga zimene zingakubwezeni m’mbuyo.

“Cikuniletsa Kubatizika N’ciani?” (Nsanja ya Mlonda, March 2019)

Onani mmene mwamuna wina anagonjetsela zopinga zazikulu kuti abatizike.

N’cifukwa Ciani Mucedwa Kubatizika?’ (1:10)

Poyamba mwamuna wina dzina lake Ataa anali kuzengeleza kuti abatizike. Onani cimene cinam’khutilitsa maganizo kuti atenge sitepe yofunika imeneyi.

Kodi N’nali Woyeneleladi Madalitso Onsewa? (7:21)