PHUNZILO 57
Kodi Muyenela Kutani Mukacita Chimo Lalikulu?
Ngakhale kuti Yehova mumam’konda kwambili, ndipo mumayesetsa kupewa kucita zinthu zomukhumudwitsa, nthawi zina mudzapangabe zolakwa. Ndipo macimo ena amakhala aakulu kuposa ena. (1 Akorinto 6:9, 10) Koma mukagwela mu chimo lalikulu, kumbukilani kuti Yehova sanaleke kukukondani; iye amakhala wofunitsitsa kukukhululukilani na kukuthandizani.
1. Kodi tiyenela kucita ciyani kuti Yehova atikhululukile?
Aja amene amamukondadi Yehova, akazindikila kuti acita chimo lalikulu, amacita cisoni kwambili. Ngakhale n’conco, iwo amapeza citonthozo mu lonjezo la Yehova kwa anthu ake lakuti: “Ngakhale macimo anu atakhala ofiila kwambili, adzayela kwambili.” (Yesaya 1:18) Ngati tilapa moona mtima, Yehova adzatikhululukila na mtima wonse. Kodi timalapa bwanji? Cifukwa ca kumva cisoni cacikulu, timalekelatu kucita coipaco na kumucondelela Yehova kuti atikhululukile. Kenako, timalimbikila kusintha maganizo athu olakwika, kapena cizolowezi coipa cimene cinatifikitsa ku chimolo. Ndiyeno timayesetsa kutsatila malamulo oyela a Yehova.—Ŵelengani Yesaya 55:6, 7.
2. Kodi tikacimwa Yehova amaseŵenzetsa bwanji akulu kuti atithandize?
Tikagwela mu chimo lalikulu, Yehova amatiuza kuti ‘tiitane akulu a mpingo.’ (Ŵelengani Yakobo 5:14, 15.) Amuna oikidwa amenewa amam’konda kwambili Yehova pamodzi na nkhosa zake. Iwo amadziŵa bwino mmene angatithandizile kukonzanso ubale wathu na Yehova.—Agalatiya 6:1.
Kodi akulu amenewa amatithandiza bwanji tikacita chimo lalikulu? Akulu aŵili kapena atatu amasankhidwa kuti atithandize potipatsa uphungu wa m’Malemba. Iwo amatiuzanso zocita kuti tisakabwelezenso chimo limenelo, ndiponso amatipatsa cilimbikitso. Iwo angatiimitse kwa kanthawi pa zocitika zina zacikhristu kufikila pamene tidzakhalanso athanzi kuuzimu. Aliyense amene anacita chimo lalikulu, ndipo ni wosalapa, amam’cotsa mumpingo kuti asawononge ena.
KUMBANI MOZAMILAPO
Yesani kumvetsetsa mmene Yehova amatithandizila tikagwela m’chimo lalikulu.
3. Kuulula macimo athu kumatithandiza kucila kuuzimu
Chimo lililonse limene tingacite limamukhudza Yehova. Conco, tiyenela kuulula kwa iye. Ŵelengani Salimo 32:1-5, na kukambilana funso ili:
-
N’cifukwa ciyani n’cinthu canzelu kuulula macimo athu kwa Yehova, m’malo moyesa kuwabisa?
Tikaulula macimo athu kwa Yehova, tiyenelanso kupempha akulu kuti atithandize. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
-
Mu vidiyo imeneyi, kodi akulu anamuthandiza bwanji Canon kuti abwelele kwa Yehova?
Tiyenela kulankhula momasuka komanso moona mtima kwa akulu; iwo alipo kuti atithandize. Ŵelengani Yakobo 5:16, na kukambilana funso ili:
-
Tikalankhula moona mtima kwa akulu, n’cifukwa ciyani cimawapepukila kuti atithandize?
4. Mmene kucotsa munthu mumpingo kumathandizila
Munthu akacita chimo lalikulu, ndipo akukana kutsatila malangizo a Yehova, sayenelanso kukhala mumpingo. Munthu ameneyo amacotsedwa mumpingo, ndipo timaleka kuyanjana naye kapena kulankhula naye. Ŵelengani 1 Akorinto 5:6, 11, komanso 2 Yohane 9-11, kenako kambilanani funso ili:
-
Monga mmene yisiti amafufumitsila fulawulo wokanda, kodi kuyanjana na munthu wosalapa kungakhudze bwanji mpingo?
Ambili amene anacotsedwapo, pambuyo pake anabwelela mumpingo. Ngakhale kuti cilango cimene analandila cinali coŵaŵa, cinawathandiza kuganizanso mwanzelu. (Salimo 141:5) Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
-
Mu vidiyo imeneyi, kodi kucotsedwa mumpingo kunamuthandiza bwanji Sonja?
Kodi kucotsa munthu mumpingo . . .
-
kumalemekeza bwanji dzina la Yehova?
-
kumaonetsa motani kuti Yehova ni wacilungamo komanso wacikondi?
5. Yehova amatikhululukila tikalapa
Yesu anapeleka fanizo lotithandiza kumvetsa mmene Yehova amamvela munthu akalapa. Ŵelengani Luka 15:1-7, na kukambilana funso ili:
-
Kodi zimenezi zimakuphunzitsani ciyani za Yehova?
Ŵelengani Ezekieli 33:11, na kukambilana funso ili:
-
Kodi kulapa kwenikweni kumafuna kuti ticite ciyani?
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Nimaopa kuti, nikawauza akulu za chimo langa, adzanicotsa mumpingo.”
-
Kodi inu mungamuuze ciyani munthu amene amaganiza conco?
CIDULE CAKE
Ngati tacita chimo lalikulu, koma ndife acisoni mocokela pansi pa mtima, ndipo tatsimikiza mumtima mwathu kuti sitidzacitanso coipaco, Yehova adzatikhululukila.
Mafunso Obweleza
-
N’cifukwa ciyani n’cinthu canzelu kuulula macimo athu kwa Yehova?
-
Kodi tiyenela kucita ciyani kuti macimo athu akhululukidwe?
-
Tikacita chimo lalikulu, n’cifukwa ciyani tiyenela kupempha thandizo kwa akulu?
FUFUZANI
Onani mmene mwamuna wina anapindulila na cifundo ca Yehova cofotokozedwa pa Yesaya 1:18.
Kodi kucotsa munthu mumpingo kugawapindulile bwanji onse okhudzidwa?
“Cifukwa Cake Kucotsa Munthu Mumpingo Ndi Makonzedwe Acikondi” (Nsanja ya Mlonda, April 15, 2015)
Onani mmene mungafotokozele munthu amene si Mboni ubwino wocotsa munthu mumpingo.
“Kodi a Mboni za Yehova Amapewa Anthu Amene Kale Anali M’cipembedzo Cao?” (Nkhani ya pawebusaiti)
Mu nkhani yakuti “Ndinazindikira Kuti Ndiyenera Kubwerera kwa Yehova,” onani mmene mwamuna wina amene anatayika pa coonadi anaonela kuti Yehova ndiye anamukokelanso kwa Iye.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2012)