Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 2

Rabeka Anafuna Kukondweletsa Yehova

Rabeka Anafuna Kukondweletsa Yehova

Rabeka anali mkazi wokonda Yehova. Dzina la mwamuna wake linali Isaki. Nayenso anali kukonda Yehova. Kodi Rabeka ndi Isaki anakumana bwanji? Nanga anacita ciani kuti aonetse kuti anali kufuna kukondweletsa Yehova? Tsopano tiye tiphunzile zambili ponena za iye.

Abulahamu ndi Sara anali makolo a Isaki. Anali kukhala m’dziko la Kanani, limene anthu ake sanali kulambila Yehova. Koma Abulahamu anafuna kuti mwana wake akwatile mkazi wolambila Yehova. Conco, anatuma wanchito wake, mwina Eliezere, kuti akapeze mkazi wa Isaki kumalo ochedwa Harana, kumene acibale ena a Abulahamu anali kukhala.

Rabeka anali wofunitsitsa kutungila madzi ngamila

Pa ulendowu Eliezere anapita limodzi ndi anchito ena a Abulahamu. Ulendo umenewo unali wautali. Anatenga ngamila 10 zimene zinanyamula zakudya ndi mphatso. Kodi Eliezere akanadziŵa bwanji mkazi woyenelela Isaki? Eliezere ndi anzake atafika ku Harana, anaimilila pacitsime cifukwa Eliezere anadziŵa kuti posapita nthawi anthu adzayamba kubwela kudzatunga, kapena kuti kutapa madzi. Iye anapemphela kwa Yehova kuti: ‘Ndikapempha mtsikana kundipatsa madzi,’ ndipo andipatsa ndi kupatsanso ngamila, ndidzadziŵa kuti ndiye mkazi amene mwasankha.’

Pamenepo mtsikana wa dzina lakuti Rabeka anafika pacitsime. Baibulo limanena kuti anali wokongola kwambili. Eliezere anam’pempha madzi akumwa, ndipo iye anati: ‘Palibe vuto ndikutungilani madzi ndipo nditungilanso ngamila zanu.’ Ganizila cabe! Popeza kuti ngamila zimamwa madzi ambili, Rabeka anafunika kuthamanga mobweleza-bweleza kukatunga madzi. Kodi waona mmene akugwilila nchito zolimba pa cithunzi-thunzi apa?— Eliezere anadabwa ndi mmene Yehova anayankhila pemphelo lake.

Eliezere anapatsa Rabeka mphatso zambili zabwino. Conco, Rabeka anatenga Eliezere ndi atumiki anzake kunyumba kwao. Eliezere anawauza cifukwa cimene Abulahamu anam’tumizila kumeneko ndi mmene Yehova anayankhila pemphelo lake. Banja la Rabeka linakondwela kuti iye akwatiwe ndi Isaki.

Rabeka anapita ku Kanani ndi Eliezere ndipo anakwatiwa ndi Isaki

Koma, kodi uganiza kuti Rabeka anafuna kukwatiwa ndi Isaki?— Rabeka anadziŵa kuti Eliezere watumidwa ndi Yehova. Motelo, pamene banja la Rabeka linamufunsa ngati afuna kupita ku Kanani kuti akakwatiwe ndi Isaki iye anati: ‘Inde ndifuna kupita.’ Nthawi imeneyo iye anapita ndi Eliezere. Pamene anafika ku Kanani iye anakwatiwa ndi Isaki.

Yehova anadalitsa Rabeka cifukwa iye anacita zimene anali kufuna. Patapita zaka zambili, Yesu anadzabadwila m’banja limenelo. Ngati ukhala monga Rabeka ndi kukondweletsa Yehova, iwenso adzakudalitsa.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • Genesis 12:4, 5; 24:1-58, 67