Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 3

Rahabi Anakhulupilila Yehova

Rahabi Anakhulupilila Yehova

Tiyelekezele kuti tinali kukhala mu mzinda wa Yeriko. Mzinda umenewu unali m’dziko la Kanani, ndipo anthu a kumeneko sanali kukhulupilila Yehova. Mkazi wina dzina lake Rahabi anali kukhala kumeneko.

Ali kamtsikana, Rahabi anamva nkhani ya mmene Mose anapatutsila madzi pa Nyanja Yofiila, ndi kutsogolela Aisiraeli kuti atuluke mu Iguputo. Iye anamvanso mmene Yehova anathandizila Aisiraeli kupambana nkhondo pomenyana ndi adani ao. Tsopano iye akumva kuti Aisiraeli amanga misasa ya nkhondo pafupi ndi Yeriko.

Rahabi anabisa azondi cifukwa anakhulupilila Yehova

Tsiku lina madzulo, Aisiraeli aŵili analoŵa mu mzinda wa Yeriko kuti aone mmene ulili. Iwo anafika kunyumba ya Rahabi, ndipo iye anawalandila ndi kukhala nao. Usiku umenewo, mfumu ya mzinda umenewo inamva kuti azondi aciisiraeli aloŵa mu mzinda ndipo ali ku nyumba ya Rahabi. Conco, mfumu inatuma amuna kuti akabweletse anthu amenewo. Koma Rahabi anabisa anthuwo pa tsindwi la [mtenje wa] nyumba yake, ndi kuuza amuna otumidwa ndi mfumu kuti: ‘Inde, amunawo anabweladi kwa ine, koma io acoka kale-kale mu mzinda uno. Fulumilani! Athamangileni! Muwapeza!’ Kodi udziŵa cifukwa cake Rahabi anachinjiliza amuna amenewo?— Cifukwa iye anakhulupilila Yehova ndipo anadziŵa kuti Yehova adzapeleka dziko la Kanani kwa Aisiraeli.

Azondi amenewo asanacoke, analonjeza Rahabi kuti iye pamodzi ndi banja lake adzapulumuka pamene Yeriko adzaonongedwa. Kodi udziŵa zimene io anauza Rahabi kucita?— Iwo anati: ‘Cingwe cofiila ici ucimangilile panja pawindo. Ukadzacita zimenezo onse a m’nyumba yako adzapulumuka.’ Ndipo Rahabi anacitadi zimene azondi amenewo anamuuza. Kodi udziŵa zimene zinacitika Rahabi atacita zimenezo?—

Yehova anapulumutsa Rahabi ndi banja lake

Patapita masiku ocepa cabe, Aisiraeli mwakacete-cete anazungulila mzinda. Kwa masiku 6 io anali kuzungulila mzinda kamodzi patsiku. Koma patsiku la 7 io anazungulila mzinda nthawi 7. Kenako io pamodzi anafuula mokweza. Yehova anacititsa mpanda wonse wa mzinda kugwa mbwee. Koma nyumba yokhala ndi cingwe cofiila panja pawindo siinagwe. Kodi waiona pacithunzi-thunzi apa?— Rahabi ndi banja lake anapulumutsidwa.

Kodi uphunzilapo ciani pa citsanzo ca Rahabi?— Rahabi anakhulupilila Yehova cifukwa ca zinthu zosangalatsa zimene anaphunzila ponena za iye. Iwenso ukuphunzila zinthu zambili zocititsa cidwi ponena za Yehova. Kodi iwe umakhulupilila Yehova monga mmene Rahabi anacitila?— Tidziŵa kuti umatelo.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • Yoswa 2:1-24; 6:1-5, 14, 15, 20-25

  • Aheberi 11:31