Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Masisitele Anakhala Paubale Weniweni Wakuuzimu

Masisitele Anakhala Paubale Weniweni Wakuuzimu

ZAKA zambili zapitazo, mng’ono wanga, Araceli anakwiya kwambili ndipo anandinyoza. Iye anati: “Osakamba ndi ine. Sindifuna kumva ciliconse cokhudza cipembedzo canu. Mumandinyansa ndi cipembedzo canuci.” Mau amenewa anandikhumudwitsa kwambili. Ngakhale kuti tsopano ndili ndi zaka 91, ndikali kuwakumbukila bwino mau amenewa. Koma monga mmene lemba la Mlaliki 7:8 limakambila, “mapeto a cinthu amakhala bwino kuposa ciyambi cake.”—Felisa.

Felisa: Ndinakulila m’banja lina losauka ku Spain. Banja lathu linali la Katolika ndipo tinali kukonda kwambili kupemphela. Acibale anga okwana 13 anali kugwila nchito pa chalichi ndipo ena pakati pao anali ansembe. Msuweni wa amai anga anali wansembe ndiponso mphunzitsi pa sukulu ya Katolika. Iye atamwalila, Papa John Paul waciŵili, anamulemekeza mwa kumudzodza kukhala woyela mtima. Atate anga anali mmisili wazitsulo, ndipo amai anga anali mlimi. M’banja lathu tinabadwa okwanila 8, ndipo ine ndine woyamba.

Nditafika zaka 12, ku Spain kunabuka nkhondo yapaciŵeniŵeni. Nkhondo itatha, atate anga anaikidwa m’ndende cifukwa boma linali kudana ndi maganizo ao pa zandale. Zinali zovuta kwa amai kupezela zakudya banja lonse. Conco, anapeleka ang’ono anga, Araceli, Lauri, ndi Ramoni kunyumba ya masisitele mumzinda wa Bilbao kuti azikakhala ndi masisitele. Kumeneko, ang’ono anga anali kudya bwino.

Araceli: Panthawi imeneyo, ndinali ndi zaka 14, Lauri anali ndi zaka 12, ndipo Ramoni anali ndi zaka 10. Tinali kuyewa banja lathu kwambili. Kunyumba ya masisitele, tinali kugwila nchito yoyeletsa. Patapita zaka ziŵili, masisitele anatitumiza kunyumba ina yaikulu ya masisitele ku Zaragoza, kumenenso anali kusungila okalamba. Tinali kugwila nchito yoyeletsa m’khicheni, ndipo tinali kulema kwambili.

Felisa: Ang’ono anga atapita kunyumba ya masisitele ku Zaragoza, amai ndi amalume anga, amene anali wansembe, anaganiza zonditumizanso kumeneko. Anafuna kuti ndileke kuceza ndi mnyamata winawake amene anali kundikonda. Ndinali kuyembekezela mwacidwi kukhala kunyumba ya masisitele cifukwa ndinali kukonda Mulungu kwambili. Ndinali kupita ku chechi nthawi zonse, ndipo ndinali kufuna kudzakhala mmishonale wa Katolika monga msuweni wanga amene anali ku Africa.

Malo okhala masisitele ku Zaragoza, ku Spain (kumanzele) Baibulo la Cináka-kolunga (kulamanja)

Koma, kunyumba imeneyi, ndinayamba kuona kuti sindidzakwanitsa kucita zonse zimene ndinali kufuna. Masisitele sanandilimbikitse kukatumikila Mulungu ku dziko lina monga mmene ndinali kufunila. Conco, patapita caka, ndinabwelela kunyumba kukasamalila amalume anga, amene anali wansembe. Ndinali kugwila nchito za panyumba, ndipo madzulo alionse tinali kupemphela pamodzi pemphelo la Korona. Ndinali kukonda kuika maluŵa m’chalichi ndi kukongoletsa cithunzi ca Mariya ndi zithunzi za “oyela mtima.”

Araceli: Ndili ku Zaragoza, ndinacita malumbilo oyamba kuti ndikhale sisitele. Ndiyeno masisitele anaganiza zondilekanitsa ndi abale anga. Conco, ananditumiza kunyumba ya masisitele ku Madrid ndipo Lauri anamutumiza ku Valencia. Koma Ramoni anatsala ku Zaragoza. Ndili ku Madrid, ndinalumbila kaciŵili kuti ndikhale sisitele. Kunyumba imeneyi, kunali kukhala anthu ambili monga okalamba ndi ena obwela kudzaphunzila. Cifukwa ca ici, kunali kukhala nchito yambili. Ndinali kuseŵenzela ku cipatala.

Ndinali kuyembekezela kuti ndizisangalala ndi umoyo wa usisitele. Ndinali kuganiza kuti tidzayamba kuthela nthawi yaitali kuŵelenga ndi kuphunzila Baibulo. Koma zimene zinali kucitika zinandikhumudwitsa. Palibe aliyense amene anali kuseŵenzetsa Baibulo, ngakhale kukambako za Mulungu kapena za Yesu. Ndinaphunzila Cilatini, ndi za umoyo wa “oyela mtima” a Cikatolika, ndiponso ndinali kulambila Mariya. Koma nthawi zambili, tinali kungogwila nchito.

Ndinayamba kuda nkhawa kwambili. Ndinaona kuti cili bwino kucoka kuti ndizikagwila nchito yothandiza banja langa m’malo molemeletsa anthu ena. Conco, ndinapita kukauza sisitele wamkulu kuti ndifuna kucoka. Koma atamva zimenezo, ananditsekela m’cipinda. Anaona monga kucita zimenezi kungandicititse kusintha maganizo.

Ndiyeno, ananditulutsa, koma atazindikila kuti ndikali ndi maganizo ofuna kucoka, ananditsekelanso m’cipinda. Atanditsekela kacitatu, anandiuza kuti ndingacoke ngati ndalemba mau awa: “Ndikucoka cifukwa cakuti ndifuna kutumikila Satana osati Mulungu.” Ndinasoŵa zocita. Ndinali kufunitsitsa kucoka, koma sindikanalemba mau amenewo. Pomalizila pake, ndinapempha kuti ndikambe ndi wansembe. Ndinamuuza zonse zimene zinacitika. Iye anapempha cilolezo kwa a bishopu kuti andibweze kunyumba ya masisitele ya ku Zaragoza. Nditakhalako kwa miyezi yocepa, ndinaloledwa kucoka. Posakhalitsa, Lauri ndi Ramoni nawonso anacoka.

BUKU LIMENE LINATIGAŴANITSA

Felisa

Felisa: Patapita nthawi, ndinakwatiwa ndipo tinasamukila mumzinda wa Cantabria ku Spain. Ndinali kupitabe ku chechi nthawi zonse. Tili m’chechi pa Sondo, mokwiya wansembe anati: “Mwaliona buku ili!” Anationetsa buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolela ku Moyo Wamuyaya. Kenako anati, “Ngati winawake anakupatsani bukuli, mundipatse kapena mulitaye!”

Ndinalibe buku limenelo, koma ndinali kulifuna. Patapita masiku ocepa, azimai aŵili anabwela kunyumba kwathu. Iwo anali a Mboni za Yehova, ndipo anandipatsa buku lija limene wansembe analetsa. Usiku wa tsiku limenelo, ndinaliŵelenga. Azimai amenewa atabwelanso, anandipempha kuti ndiziphunzila nao Baibulo, ndipo ndinavomela.

Buku la Coonadi

Nthawi zonse ndinali kufuna kukondweletsa Mulungu. Ndiyeno, ndinaphunzila coonadi ponena za Yehova, ndipo ndinayamba kum’konda kwambili. Ndinali kufuna kuuza aliyense za iye. Mu 1973, ndinabatizidwa. Ndinali kuyesetsa kuuzako anthu a m’banja langa coonadi. Koma a m’banja langa, makamaka mng’ono wanga Araceli, anali kukamba kuti ndinali kukhulupilila zinthu zabodza.

Araceli: Cifukwa cakuti anali kundivutitsa kunyumba ya masisitele, ndinakhumudwa ndi cipembedzo canga. Ngakhale n’telo, ndinapitiliza kupita ku chechi pa Sondo ndi kupemphela pemphelo la Korona tsiku lililonse. Ndinali kufunabe kumvetsetsa Baibulo ndipo ndinapempha Mulungu kuti andithandize. Kenako, Felisa anandiuza zimene anaphunzila. Iye anali wosangalala kwambili ndi zimene anali kuphunzila cakuti ndinaona monga wayamba kufuntha. Sindinakhulupilile zimene anali kukamba.

Araceli

Patapita nthawi, ndinabwelela ku Madrid cifukwa ndinapeza nchito, kenako ndinakwatiwa. Kwa zaka zambili, ndinaona kuti anthu amene anali kupita ku chalichi nthawi zonse, sanali kucita zimene Yesu anaphunzitsa. Cotelo, ndinaleka kupita ku chechi. Ndinaleka kukhulupilila “oyela mtima” komanso moto wa helo ndipo sindinali kuona kuti wansembe angakhululukile macimo. Ndinacotsanso mafano onse a cipembedzo amene ndinali nao. Koma sindinali kudziŵa ngati ndinali kucita zinthu zoyenela. Ndinakhumudwa kwambili, koma ndinapitiliza kupemphela kwa Mulungu kuti: “Ndifuna kukudziŵani, ndithandizeni.” Ndikumbukila kuti Mboni za Yehova zinagogoda pacitseko maulendo ambilimbili, koma sindinatseguleko. Sindinali kukhulupilila cipembedzo ciliconse.

Mng’ono wanga Lauri anali kukhala ku France, ndipo Ramoni anali kukhala ku Spain. Ca m’ma 1980, anayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinali kuona kuti anali kuphunzila zinthu zabodza monga Felisa. Patapita nthawi, ndinakumana ndi Angelines, amene tinali kukhala naye pafupi, ndipo anakhala mnzanga. Iyenso anali wa Mboni za Yehova. Angelines ndi mwamuna wake anandipempha mobwelezabweleza kuti ndiziphunzila nao Baibulo. Iwo anazindikila kuti ndinali kufuna kumvetsetsa Baibulo ngakhale ndinali kukamba kuti sindikonda za cipembedzo. Pamapeto pake, ndinawauza kuti: “Cabwino, tingayambe kuphunzila ngati mundilola kuseŵenzetsa Baibulo langa.” Ndinali ndi Baibulo lomasulidwa m’Cinaka-Kolunga.

BAIBULO LINATIGWILIZANITSA

Felisa: Nditabatizidwa mu 1973, ku Santander, likulu la cigawo ca Cantabria, kunali Mboni za Yehova pafupifupi 70. Tinali kuyenda maulendo ataliatali kukalalikila kwa anthu onse amene anali kukhala m’midzi yambili ya m’cigawoco. Conco, tinali kuyenda pa basi ndipo kenako pa galimoto yaing’ono kucoka mudzi wina kupita ku wina.

Kwa zaka zambili, ndinaphunzila Baibulo ndi anthu oculuka, ndipo 11 mwa io anabatizidwa. Ambili anali Akatolika. Ndinafunika kukhala woleza mtima. Monga mmene zinalili kwa ine, panafunika nthawi kuti azindikile kuti zimene anali kukhulupilila zinali zabodza. Ndinali kudziŵa kuti Baibulo ndiponso mzimu woyela wa Yehova n’zimene zingathandize munthu kusintha maganizo ake ndi kuyamba kumvetsetsa coonadi. (Aheberi 4:12) Amuna anga, a Bienvenido, amene anali wapolisi, anabatizidwa mu 1979. Ndipo amai anga anamwalila atangoyamba kumene kuphunzila Baibulo.

Araceli: Nditangoyamba kuphunzila Baibulo ndi a Mboni za Yehova, ndinali kuwakaikila. Koma, m’kupita kwa nthawi, ndinayamba kuwakhulupilila. A Mboni amaphunzitsa Baibulo komanso amacita zimene limaphunzitsa. Ndinayamba kukhulupilila kwambili Yehova ndi Baibulo ndipo ndinali kukhala wosangalala. Ena mwa anthu amene tinali kukhala nao pafupi, anaona kuti nayamba kusintha. Iwo anati: “Araceli, pitiliza kucita zimene ukucita.”

Ndikumbukila tsiku lina ndinapemphela kuti, “Yehova, ndiyamikila kwambili cifukwa simunandisiye, ndipo nthawi zambili munali kundipatsa mwai wopeza cidziŵitso colondola ca m’Baibulo cimene ndinali kufuna.” Ndinapepesa kwa mkulu wanga Felisa cifukwa comunyoza. Kucokela nthawi imeneyo, m’malo moyambana, timasangalala kukambilana nkhani za m’Baibulo. Ndinabatizidwa mu 1989, ndili ndi zaka 61.

Felisa: Tsopano, ndili ndi zaka 91. Mwamuna wanga anamwalila ndipo sindikwanitsa kucita zonse zimene ndinali kucita kale. Koma ndimakwanitsa kuŵelenga Baibulo tsiku lililonse, kupita kumisonkhano, ndi mu ulaliki.

Araceli: Ndimakonda kulalikila kwa ansembe ndi masisitele amene ndimakumana nao, mwina cifukwa cakuti ndinali sisitele. Makambilano ena anali opindulitsa kwambili, ndipo ambili anatenga mabuku athu ndi magazini. Sindidzaiŵala zimene ndinakambilana ndi wansembe wina. Pambuyo pokambilana naye maulendo angapo, anavomeleza kuti ndinali kukamba zoona. Ndiyeno, anandifunsa kuti: “Ndakalamba, ndiye ndikasiya cipembedzoci ndizicita ciani? Nanga anthu a m’banja langa ndi mamembala a chalichi canga adzandiona bwanji?” Ndinam’yankha kuti: “Nanga muganiza kuti Mulungu adzamvela bwanji?” Nditamufunsa funso limeneli, anazindikila kuti ndinali kukamba zoona cifukwa nkhope yake inagwa. Koma zioneka kuti sanalimbe mtima kuti asinthe.

Ndinasangalala kwambili tsiku lina pamene amuna anga anandiuza kuti afuna tipitile pamodzi kumisonkhano. Tsiku loyamba kupezeka pa misonkhano, anali ndi zaka zoposa 80, ndipo kuyambila pamenepo sanaphonyepo misonkhano. Anaphunzila Baibulo ndi kuyamba kulalikila. Ndimakondwela kwambili ndikakumbukila nthawi imene tinali kulalikila pamodzi. Iwo anamwalila kutatsala miyezi iŵili kuti abatizidwe.

Felisa: Pamene ndinayamba kutumikila Yehova, ang’ono anga anakhumudwa kwambili. Koma patapita nthawi, iwonso anaphunzila coonadi. Izi zinandisangalalatsa kwambili. Kuyambila nthawi imeneyo, tinali kusangalala poceza pamodzi ndi kukambilana za Mulungu wathu wokondedwa, Yehova, ndi Mau ake. N’zosangalalatsa kwambili kuti patapita nthawi, tonse tinayamba kulambila Yehova. *

^ par. 29 Araceli ali ndi zaka 87, Felisa 91, ndipo Ramoni 83. Onse akali kutumikila Yehova mokhulupilika. Lauri anamwalila mu 1990, ndipo nayenso anali wokhulupilika kwa Yehova.