Ciyembekezo—Cimathandizadi?
Ciyembekezo—Cimathandizadi?
DANIEL anali na zaka 10 basi, koma anali atatha caka cathunthu akuvutika na matenda a kansa. Madokotala ndiponso anzake anali atataya kale mtima. Koma Daniel sanataye mtima ayi. Iye ankakhulupilila kuti akadzakula adzakhala wofufuza ndipo adzathandiza kupeza mankhwala ocilitsa matenda a kansa. Cinamulimbitsanso mtima makamaka cinali cakuti ankayembekezela kubwela kwa dokotala wodziŵa bwino za kansa yakeyo. Komano tsiku lake litakwana, dokotalayo analephela kubwela cifukwa kunja sikunace bwino. Zimenezi Daniel zinamulefula. Kwa nthaŵi yoyamba, iye anatayilatu mtima. Kenaka patangotha masiku angapo anamwalila.
Amene anasimba nkhani ya Daniel ndi munthu wina wa zaumoyo yemwe anafufuza mmene ciyembekezo na kutaya mtima zimakhudzila thanzi lathu. N’kutheka kuti nkhani zotelezi munazimvapo. Mwacitsanzo, mwina munamvapo za agogo enaake amene ankadwala mwakayakaya komano ankafunitsitsa ataona cinthu cinacake comwe acidikilila kwa nthaŵi yaitali; cinthu monga kufika kwa wokondedwa wawo winawake kapena cabe cikondwelelo cinacake ca pacaka. Ndiye cinthuco citangocitika, basi agogowo anafa. Kodi n’ciani cimacititsa zotelezi? Kodi kukhala n’ciyembekezo n’kothandizadi kwambili monga mmene anthu ena amaganizila?
Anthu ambili ofufuza za matenda amati kusataya mtima, kukhala n’ciyembekezo, komanso maganizo ena otele, kumathandizadi pa moyo ndiponso thanzi la munthu. Komanso si onse amagwilizana na mfundoyi. Ofufuza ena amati zimenezi n’zikhulupililo cabe ndipo zilibe umboni wasayansi. Iwo amaona kuti matenda amayambitsidwa na zinthu zenizeni osati za m’maganizo cabe ayi.
Inde, kuyambila kale anthu akhala asakukhulupilila kuti ciyembekezo n’cothandizadi. Zaka masauzande zapitazo, Aristotle, yemwe anali wafilosofi wa ku Greece anafunsidwapo kuti anene tanthauzo la ciyembekezo, ndiyeno iye anayankha kuti ciyembekezo “n’kulota uli maso.” Ndipo osati kale kwenikweni, mtsogoleli wa dziko la America, Benjamin Franklin ananena monyoza kuti: “Wodalila ciyembekezo amangotaya nthaŵi pacabe.”
Motelo kodi zoona zake zenizeni za ciyembekezo n’zotani? Kodi nthaŵi zonse munthu akakhala n’ciyembekezo amakhala akungodzinamiza yekha kuti akwanitsa kucita zinthu zomwe kwenikweni zili zosatheka? Kapena kodi pali zifukwa zomveka zoganizila kuti ciyembekezo n’cinthu cofunikiladi kwa tonsefe kuti tikhale athanzi ndi osangalala, komanso kuti ciyembekezo n’cinthu cotsimikizika ndiponso copindulitsadi?