N’zotheka Kusiya Fodya
N’zotheka Kusiya Fodya
TINENE kuti tsopano ‘mwalimba mtima’ kuti musiye kusuta fodya, kodi ni mfundo ziti zomwe mungatsatile kuti zimenezo zitheke?—1 Mbiri 28:10.
Sankhani tsiku. Dipatimenti ya zaumoyo ku United States inanena kuti munthu akaganiza zosiya kusuta, ayenela kuonetsetsa kuti waziikila malile osiya kusuta mkati mwa milungu iŵili. Kucita zimenezi kungakuthandizeni kuti musasinthe maganizo. Lembani tsiku lomwe mwasankhalo pakalendala, dziŵitsani anzanu ndipo tsikulo likafika musalisinthe, zivute zitani.
Muziyenda ni pepala lolembedwa kuti “Nasiya kusuta.” Papepalapo mungalembe zinthu zomwe zingakuthandizeni kutsatila zomwe mwasankha monga:
● Zifukwa zosiyila.
● Manambala a foni a anthu amene mungawaimbile panthawi yomwe cibaba ca fodya cakubwelelani.
● Mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni, ngati zomwe zili pa Agalatiya 5:22, 23.
Nthawi zonse muziyenda ni pepala limene mwalemba kuti “Nasiya kusuta” kuti lizikukumbutsani zomwe mwasankhazo. Ngakhale mutafika poti mwasiya kusuta, muziyenda nalobe kuti muziliŵelenga mukaona kuti cibaba coti musute cayambilanso.
Siyani zinthu zina zimene mumakonda kucita. Tsiku lomwe mwasankha kusiya kusuta lisanafike, muyenela kusiya kaye zizolowezi zina zimene mumacita. Mwacitsanzo, ngati muli na cizolowezi cosuta mukangodzuka m’mawa, yesani kusintha kuti muzitha ola limodzi musanasute. Ngati mumasuta panthawi ya cakudya kapena mukangomaliza kudya, siyani kusuta panthawi imeneyi. Pewani malo amene anthu amakonda kusutilako fodya. Ndipo mukakhala nokha muziyesa kunena mokuwa kuti: “Pepani, nasiya kusuta.” Zimenezi zingakuthandizeni kwambili kuti musadzavutike kusiya tsiku limene mwasankha kusiya kusuta likafika. Komanso zimenezi zingakuthandizeni kuona kuti kusuta fodya ikhala mbili yakale kwa inu.
Konzekani. Tsiku limene mwasankha kuti musiye kusuta likayandikila, pezani zinthu zomwe mungamadye, m’malo mosuta. Mwacitsanzo, mungagule kaloti, cingamu, mtedza na zina zotelo. Kumbutsani anzanu komanso anthu am’banja lanu za tsiku limene mukufuna kusiya komanso mmene angakuthandizileni. Tsikulo lisanafike, muyenela kutaya zotsalila zonse za fodya, macesi na zina zimene zingakukopeni kuti muyambilenso kusuta. Mwacitsanzo, muyenela kutaya ndudu zimene zili m’nyumba, m’galimoto, m’matumba a zovala kapena ku ofesi. Kunena zoona, n’zovuta kwambili kupempha mnzanu kuti akupatseni fodya kapena kugula paketi ya fodya kusiyana na kungopita m’nyumba n’kutenga. Ndiponso, pitilizani kupempha Mulungu kuti akuthandizeni, ndipo muyenela kuyesetsa kwambili kucita zimenezi pamene mwasiya kusuta.—Luka 11:13.
Anthu ambili akwanitsa kusiya kusuta, ndipo inunso mungakwanitse. Dziŵani kuti fodya ni woipa. Kusiya kusuta kungakuthandizeni kukhala na thanzi labwino ndiponso kukhala wosangalala kwambili.
Nthawi zonse muziyenda na pepala limene mwalemba kuti, “Nasiya kusuta” kuti lizikukumbutsani zomwe mwasankhazo