Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tsankho—Kodi Na Imwe Muli Nalo?

Tsankho—Kodi Na Imwe Muli Nalo?

Tsankho lili ngati matenda. Limawononga munthu amene ali nalo, ndipo nthawi zina munthu watsankho sazindikila kuti ali nalo.

Anthu amaonetsa tsankho kwa anthu cifukwa cosiyana dziko, mtundu, cinenelo, kapena cipembedzo. Enanso amaonetsa tsankho kwa anthu cifukwa si amuna kapena akazi anzawo, kapenanso cifukwa si olemela kapena osauka anzawo. Palinso ena amene amaona anthu molakwika cifukwa ca zaka zawo zakubadwa, maphunzilo awo, zilema zimene ali nazo, kapena cifukwa ca maonekedwe awo. Ngakhale n’telo, anthu otelo amadziona kuti alibe tsankho.

Kodi na imwe mungakhale na tsankho? Ambili a ife timakwanitsa kuona tsankho mwa ena. Koma cingakhale covuta kuzindikila kuti na ife tili nalo. Zoona n’zakuti tonsefe tiliko na tsankho pa mlingo winawake. Katswili wa cikhalidwe ca anthu, dzina lake David Williams anakamba kuti ngati anthu amauona molakwika mtundu winawake wa anthu, akakumana na munthu wocokela mu mtundu umenewo, “amacita naye zinthu mosiyanako, koma osazindikila ngakhale pang’ono kuti aonetsa tsankho.”

Mwacitsanzo, m’dziko lina ku Europe muli mtundu wina wocepa wa anthu. Ambili m’dzikolo sawakonda anthu ocokela mu mtundu umenewo. Jovica, amene akhala m’dzikolo, anati: “N’nali kuganiza kuti anthu onse a mtundu umenewo si abwino. Koma sin’nadziŵe kuti n’nali na tsankho, cifukwa n’nali kukhulupilila kuti ni mmenedi anthuwo alili.”

Maboma ambili amapanga malamulo oletsa kusankhana mitundu na makhalidwe ena atsankho. Ngakhale n’conco, khalidwe la tsankho likupitilizabe. Cifukwa ciani? Cifukwa malamulowo amangoletsa munthu kucita tsankho. Sangalamulile za m’maganizo na mumtima mwa munthu, mmene mumayambila tsankholo. Ndiye funso n’lakuti, kodi n’zothekadi kuthetsa tsankho? Kodi mankhwala othetsela tsankho aliko?

Nkhani zotsatila zifotokoza mfundo zisanu, zimene zathandiza anthu ambili kuthetsa tsankho mumtima na m’maganizo mwawo.