Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Alisa

Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Turkey

Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Turkey

AKHRISTU a m’zaka 100 zoyambilila anayesetsa kulalikila “uthenga wabwino . . . wa Ufumu” kwa anthu ambili. (Mat. 24:14) Ena anacita kupita ku maiko ena kuti akalalikile. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo pa maulendo ake a umishonale anapita ku dela limene lomba timati dziko la Turkey. * Kumeneko, iye anayesetsa kulalikila anthu ambili. Mu 2014, pambuyo pa zaka 2,000, ku Turkey kunacitikanso nchito yapadela yolalikila. N’cifukwa ciani analinganiza zakuti pacitike nchito imeneyi? Nanga anagwila nchitoyi n’ndani?

“N’CIANI CIKUCITIKA?”

Ku Turkey kuli ofalitsa oposa 2,800, koma kuli anthu 79 miliyoni. Izi zitanthauza kuti wofalitsa mmodzi afunika kulalikila anthu 28,000 m’dzikoli. N’zoonekelatu kuti ofalitsa m’dzikoli amakwanitsa kulalikila anthu ocepa cabe. Colinga ca kampeni imeneyi cinali kulalikila anthu ambili m’kanthawi kocepa. Abale na alongo pafupi-fupi 550 okamba citundu ca Citeki, anapita kudziko la Turkey kuti akagwile nchito yapadela imeneyi pamodzi na ofalitsa a kumeneko. Kodi panakhala zotulukapo zanji?

Anthu ambili anamva uthenga wabwino. Mpingo wina ku Istanbul unalemba kuti: “Anthu akationa, anali kutifunsa kuti: ‘Kodi kuli msonkhano wapadela? Paliponse tingoona a Mboni za Yehova.’” Mpingo winanso mu mzinda wa Izmir unalemba kuti: “Munthu woseŵenza pa malo okwelela matakisii anafikila mkulu n’kumufunsa kuti: ‘N’ciani cikucitika?’ Mulalikila kwambili masiku ano.’” Zoonadi, anthu ambili anaona kuti nchito yapadela inali kucitika.

Steffen

Abale na alongo amene anacokela ku maiko ena anasangalala kwambili kugwila nawo nchito yolalikila imeneyi. Steffen, wocokela ku Denmark, anati: “Tsiku lililonse, n’nali kulalikila anthu amene sanamvelepo za Yehova. N’nali kudzimva kuti nikudziŵikitsadi dzina la Yehova.” Nayenso Jean-David wocokela ku France analemba kuti: “Tinalalikila kwa maola ambili mumsewu umodzi cabe. Tinali kusangalala ngako. Anthu ambili sanali kuwadziŵa a Mboni za Yehova. Pafupi-fupi pa nyumba iliyonse tinali kupeza anthu omvetsela, ndipo tinali kuwatambitsa mavidiyo yathu, ndi kuwagaŵila zofalitsa.”

Jean-David (pakati)

Ofalitsa 550 anagaŵila zofalitsa 60,000 m’mawiki aŵili cabe. Kampeniyo inathandizadi kuti anthu ambili amvele uthenga wabwino.

Khama lawo pa nchito yolalikila linawonjezeka. Nchito yapadela imeneyi inawalimbikitsa kwambili abale a m’dzikolo. Ambili anaganiza zoyamba utumiki wa nthawi zonse. Zotulukapo zake zinali zakuti ciŵelengelo ca apainiya a nthawi zonse ku Turkey cinawonjezeka. Ofalitsa 82 anayamba upainiya patangopita caka cimodzi kucokela nthawi ya kampeni.

Şirin

Ofalitsa a ku maiko ena amene anagwilako nchito yapadelayi anafotokoza mmene inakhudzila utumiki wawo atabwelela kwawo. Şirin, mlongo wa ku Germany, anati: “Abale a ku Turkey savutika kucita ulaliki wamwayi. Ine mwacibadwa nimacita manyazi kulalikila mwamwayi. Koma cifukwa ca kampeniyi, citsanzo ca abale a kumeneko, ndi mapemphelo, n’nakwanitsa kucita zimene kale n’nali kulephela. N’nakwanitsa ngakhale kulalikila na kugaŵila tumapepa twauthenga mumsewu. Lomba sinicita manyazi kwambili ngati mmene n’nali kucitila poyamba.”

Johannes

Johannes wa ku Germany anati: “N’naphunzila zambili zothandiza pa utumiki wanga. Abale a ku Turkey amakhala ofunitsitsa kulalikila coonadi kwa anthu ambili mmene angathele. Amalalikila pa mpata uliwonse umene apeza. N’tabwelela ku Germany, n’naganiza zakuti nizicita zofananazo. Ndipo lomba nimalalikila anthu ambili kuposa kale.”

Zeynep

“Nchito yapadelayi inanithandiza ngako pa utumiki wanga. Inanithandiza kukhala wolimba mtima ndi kudalila kwambili Yehova,” anatelo Zeynep wa ku France.

Cikondi na mgwilizano zinawonjezeka pakati pa ofalitsa. Zinali zocititsa cidwi kuona cikondi na mgwilizano umene unali pakati pa abale na alongo ocokela m’maiko osiyana-siyana. Jean-David, amene tam’chula kale, anati: “Tinaona mzimu woceleza umene abale ali nawo. Anatilandila monga mabwenzi awo ndi acibululu awo. Anatilandila bwino ku nyumba zawo. N’nali kudziŵa kuti tili paubale wa padziko lonse. N’naŵelengako kambili-mbili m’zofalitsa zathu za ubale umenewu. Koma pa cocitikaci, n’nadzionela nekha za ubalewu. Nimanyadila kukhala m’gulu la anthu a Yehova, ndipo nimamuyamikila cifukwa ca mwayi umenewu.”

Claire (pakati)

“Ngakhale kuti tinali ocokela kumaiko osiyana-siyana monga Denmark, France, Germany, ndi Turkey, tonse tinali ogwilizana monga banja limodzi. Zinali ngati kuti Mulungu wafufuta malile a maiko na cilaba cacikulu,” anatelo Claire wa ku France.

Stéphanie (pakati)

Nayenso Stéphanie wocokela ku France anati: “Nchito yapadelayi inatiphunzitsa kuti cimene cimatigwilizanitsa si cikhalidwe kapena citundu, koma ndi kukonda kwathu Yehova.”

ANAPEZA MAPINDU OKHALITSA

Ofalitsa ambili ocokela ku maiko ena amene anacitako nchito yapadelayi anaganiza zokukila ku Turkey kuti akathandize pa nchito yaikulu yolalikila imene ili kumeneko. Ena mwa iwo anapita kale. Ofalitsa otumikila kosoŵa amenewa timawayamikila kwambili.

Mwacitsanzo, ganizilani za kagulu ka ofalitsa 25, kamene kali m’dela lina lakutali m’dzikolo. Kwa zaka zambili, kagulu kameneka kanali na mkulu mmodzi. Mosakayikila, abale na alongo a m’kaguluko anakondwela ngako pamene ofalitsa ena 6 ocokela ku Germany ndi ku Netherlands anasamukila kudela limeneli mu 2015, kuti akatumikile pamodzi ndi ofalitsa a kudelali.

KUTUMIKILA KOSOŴA

Kodi abale na alongo amene akutumikila ku Turkey anakamba ciani cokhudza umoyo wawo kumeneko? N’zoona kuti nthawi zina zimakhala zovuta, koma kutumikila kosoŵa kumabweletsa madalitso oculuka. Onani zimene ena mwa iwo anakamba:

Federico

“Kukhala na umoyo wosalila zambili kwanithandiza kukhala womasuka ndi kuika maganizo anga pa zinthu zofunika kwambili,” anatelo Federico, m’bale wokwatila wa zaka za m’ma 40, amene ni wocokela ku Spain. Kodi iye amaona kuti utumiki umenewu ni wabwino? Iye anati: “Inde, ni wabwino ngako. Ukapita ku dziko lina n’colinga cokathandiza anthu kudziŵa Yehova, umaonetsa kuti umadalila Mulungu. Ndipo m’pamene umaona bwino kuti Yehova akukusamalila kwambili.”

Rudy

Rudy, m’bale wokwatila wa zaka za m’ma 50 wocokela ku Netherlands, anati: “Kutumikila kosoŵa na kuuzako coonadi anthu ambili amene sanacimveleko, kumaticititsa kukhala wokhutila. Tikaona cimwemwe cimene anthu amakhala naco akalandila coonadi, timakhala osangalala ngako.”

Sascha

Sascha, m’bale wokwatila wa zaka za m’ma 40 wocokela ku Germany, anati: “Nthawi zonse nikapita mu ulaliki, nimakumana ndi anthu amene n’koyamba kumvelako coonadi. Kukhala na mwayi wothandiza anthu aconco kudziŵa Yehova, kumanicititsa kukhala na cimwemwe coculuka.”

Atsuko

Atsuko, mlongo wokwatiwa wa zaka za m’ma 30 wocokela ku Japan, anati: “Kale, n’nali kungofuna Aramagedo itabwela mwamsanga. Koma kucokela pamene n’nabwela kuno ku Turkey, nimayamikila Yehova cifukwa ca kuleza mtima kwake. Nikaona mmene Yehova akuyendetsela zinthu, cikondi canga pa iye cimakulila-kulila.”

Alisa, mlongo wocokela ku Russia wa zaka za m’ma 30, anakamba kuti: “Kutumikila Yehova mwanjila imeneyi kwanithandiza kuona ubwino wonse wa Yehova.” (Sal. 34:8) Anakambanso kuti: “Yehova ni Tate wanga komanso Mnzanga wapamtima, ndipo umoyo wanga watsopano wanithandiza kum’dziŵa bwino kwambili. Umoyo wanga ni wodzala na cimwemwe ndi madalitso osaneneka.”

‘ONANI M’MINDAMO’

Nchito yapadela imene inacitika ku Turkey, inathandiza kuti anthu ambili amvele uthenga wabwino. Ngakhale n’conco, kukali gawo lalikulu losalalikidwa. Ofalitsa amene anapita kukatumikila ku Turkey, tsiku lililonse amapeza anthu amene sanamveleko za Yehova. Kodi mungakonde kukatumikilako ku gawo laconco? Ngati mungakonde, tikulimbikitsani kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Inde, ngati mufuna kukatumikila kudela kumene minda ‘ni yoyela ndipo ni yofunika kukolola,’ yambani lomba kukonzekela kuti mudzakwanilitse colinga canu. Ndipo dziŵani kuti ngati mugwila nawo mokwanila nchito yolalikila “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi,” mudzalandila madalitso osaneneka.—Mac. 1:8.

^ par. 2 Onani kabuku kakuti, ‘Onani Dziko Lokoma’ mapeji 32-33.