Zimene Mungacite Kuti Kuŵelenga Baibo Kwanu Kukhale Kopindulitsa Komanso Kokondweletsa
YOSWA anapatsidwa nchito yaikulu kwambili. Anafunika kutsogolela mtundu wa Aisiraeli kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, ndipo anali kuyembekezela kukumana na adani oopsa. Koma Yehova anamulimbikitsa na kumutsimikizila kuti adzapambana. Anamuuza kuti: ‘Khala wolimba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Uzitsatila malamulo anga onse. Uziwaŵelenga usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatila zonse zolembedwamo. Ukatelo, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzacita zinthu mwanzelu.’—Yos. 1:7, 8.
Popeza tikukhala m’masiku otsiliza komanso ovuta, nafenso timakumana na mavuto aakulu. (2 Tim. 3:1) Mofanana ndi Yoswa, tingapambane ngati titsatila malangizo amene Yehova anam’patsa. Tifunika kumaŵelenga Baibo tsiku lililonse, na kuseŵenzetsa mosamala mfundo zimene taŵelengazo pamene takumana na ciyeso.
Ambili a ise tingavomeleze kuti zoŵelenga-ŵelenga sitizikonda komanso kuphunzila kumativuta. Komabe, popeza kuti kuŵelenga Baibo n’kofunika ngako, onani pa kamutu kakuti “ Yesani Kucita Izi,” pamene pali malangizo abwino amene angakuthandizeni kuti kuŵelenga Baibo kwanu kukhale kopindulitsa na kokondweletsa.
Wamasalimo anaimba kuti: “Ndiyendetseni m’njila ya malamulo anu, pakuti ndikukondwela ndi njila imeneyi.” (Sal. 119:35) Na imwe mungapeze cimwemwe coculuka poŵelenga Mau a Mulungu. Pamene mupitiliza kuphunzila Baibo mwakhama, mudzapeza mfundo zambili zothandiza.
N’zoona kuti sitinapatsidwe udindo wotsogolela mtundu wa anthu monga umene Yoswa anapatsidwa. Koma na ise timakumana na mavuto. Conco, mofanana ndi Yoswa, tifunika kumaŵelenga Mau a Mulungu na kuwaseŵenzetsa. Ngati ticita zimenezi, ifenso tidzakhala na umoyo wopambana, komanso tidzacita zinthu mwanzelu.