Ndise Anthu a Yehova
“Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala colowa cake.”—SAL. 33:12.
1. N’cifukwa ciani tikamba kuti Yehova ndiye mwini zonse? (Onani pikica pamwambapa.)
ZINTHU ZONSE ni za Yehova! Baibo imakamba kuti “kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu . . ., kumwambamwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi zake zonsezo.” (Deut. 10:14; Chiv. 4:11) Popeza kuti Yehova ndiye anatilenga, tonse ndise anthu ake. (Sal. 100:3) Komabe, kuyambila kalekale, Yehova wakhala akusankha anthu ena, kuti akhale anthu ake apadela.
2. N’ndani amene Baibo imakamba kuti ni anthu a Yehova apadela?
2 Mwacitsanzo, Salimo 135 imakamba za olambila Yehova okhulupilika a m’nthawi ya Isiraeli kuti anali “cuma cake capadela.” (Sal. 135:4) Komanso buku la Hoseya linakambilatu kuti m’tsogolo anthu ena amene si Aisiraeli adzakhala anthu a Yehova. (Hos. 2:23) Ulosi umenewu unakwanilitsika pamene Yehova anayamba kusankha anthu a mitundu ina kuti nawonso akhale m’gulu la okalamulila pamodzi na Khristu kumwamba. (Mac. 10:45; Aroma 9:23-26) “Mtundu woyela” umenewu ni “cuma capadela” ca Yehova. Anthu a mu mtundu umenewu anadzozedwa na mzimu woyela komanso anasankhidwa kuti akakhale na moyo kumwamba. (1 Pet. 2:9, 10) Nanga bwanji za Akhristu ambili okhulupilika amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya pa dziko lapansi? Amenewa Yehova amawaonanso kuti ndi ‘anthu ake osankhidwa mwapadela.’—Yes. 65:22.
3. (a) N’ndani amene ali pa ubwenzi wapadela na Yehova masiku ano? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?
3 Masiku ano, a “kagulu ka nkhosa” amene ali na ciyembekezo copita kumwamba, ndi a “nkhosa zina” amene ali na ciyembekezo codzakhala pa dziko lapansi, ni “gulu limodzi” la anthu a Yehova amene iye amawakonda. (Luka 12:32; Yoh. 10:16) Kukamba zoona, tiyenela kumuyamikila kwambili Yehova cifukwa cotipatsa mwayi wokhala naye paubwenzi wapadela. M’nkhani ino, tidzakambilana njila zosiyana-siyana zimene tingaonetsele kuti timamuyamikila Yehova potipatsa mwayi wapadela umenewu.
TINADZIPATULILA KWA YEHOVA
4. Chulani njila imodzi imene tingaonetsele kuti timamuyamikila Yehova potilola kukhala naye pa ubwenzi. Nanga Yesu anacita bwanji zofanana ndi zimenezi?
4 Timaonetsa kuti timamuyamikila Yehova mwa kudzipatulila kwa iye na mtima wonse. Pamene tinabatizika, tinaonetsa poyela kuti tsopano ndise a Yehova komanso kuti ndise ofunitsitsa kumumvela. (Aheb. 12:9) Izi n’zimene Yesu anacita. Pamene anali kubatizika, zinali ngati kuti akuuza Yehova kuti: “Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga.” (Sal. 40:7, 8) Yesu anadzipatulila kuti acite cifunilo ca Yehova, olo kuti anali wobadwila mu mtundu wodzipatulila kale kwa Mulungu.
5, 6. (a) Kodi Yehova anamvela bwanji Yesu atabatizika? (b) Fotokozani citsanzo coonetsa mmene Yehova amamvelela tikadzipatulila kwa iye.
5 Kodi Yehova anamvela bwanji Yesu atabatizika? Baibo imakamba kuti: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutela. Panamvekanso mau ocokela kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.’” (Mat. 3:16, 17) Ngakhale kuti Yesu ni Mwana wa Mulungu, Yehova anakondwela poona kuti iye wasankha kudzipatulila kuti acite cifunilo cake. Mofananamo, Yehova amakondwela tikadzipatulila kwa iye, ndipo adzatidalitsa.—Sal. 149:4.
6 Kuti timvetsetse mfundo imeneyi, tiyelekezele motele: Tinene kuti tate anashanga maluŵa ambili okongola pa nyumba. Ndiyeno, tsiku lina mwana wake wamng’ono wathyola duŵa limodzi na kum’patsa monga mphatso. N’zoona kuti maluŵawo ni ake kale tateyo. Koma kodi iye angayambe kudzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciani mwanayu wanipatsa duŵa limene n’langa kale?’ Ayi, tate wacikondi sangaganizileko zimenezo. Koma angalandile mokondwela mphatsoyo cifukwa ionetsa kuti mwanayo amam’konda. Angaone duŵalo kukhala lapadela poyelekezela na maluŵa ena onse pa nyumbapo. Nayenso Yehova amakondwela kwambili tikadzipatulila kwa iye na mtima wonse.—Eks. 34:14.
7. Malinga n’zimene Malaki analemba, kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene amam’tumikila na mtima wonse?
7 Ŵelengani Malaki 3:16. Ngati simunadzipatulile na kubatizika, mungacite bwino kuganizila kufunika kocita zimenezi. N’zoona kuti kungocokela pamene tinalengedwa, tinakhala anthu a Yehova, mofanana ndi anthu ena onse. Komabe, Yehova angakondwele kwambili ngati mungadzipatulile kwa iye kuti mucite cifunilo cake kaamba kozindikila ubwino wa ulamulilo wake. (Miy. 23:15) Ndipo Yehova amawadziwa bwino anthu amene amam’tumikila na mtima wonse moti amalemba maina awo ‘m’buku la cikumbutso.’
8, 9. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene maina awo analembedwa ‘m’buku lacikumbutso’ azicita ciani?
Eks. 32:33; Sal. 69:28.
8 Kulembedwa dzina ‘m’buku la cikumbutso’ la Yehova monga anthu ake kumabwela na udindo wake. Malaki anakamba kuti tiyenela ‘kuopa Yehova ndi kuganizila za dzina lake.’ Koma ngati tingayambe kulambila munthu kapena cinthu cina ciliconse, ndiye kuti dzina lathu lingacotsedwe m’buku la moyo lophiphilitsila la Yehova.—9 Conco, kudzipatulila kwa Yehova kumaphatikizapo zambili, osati kungolonjeza kuti tidzacita cifunilo cake na kubatizika. Zinthu zimenezi zimakhala za kanthawi kocepa, ndipo posapita nthawi zikhoza kuiŵalika. Koma kuti tionetse kuti tili ku mbali ya Yehova, tifunika kukhala omvela nthawi zonse, kwa moyo wathu wonse.—1 Pet. 4:1, 2.
TIMAKANA ZILAKOLAKO ZA DZIKO
10. Kodi pafunika kukhala kusiyana kotani pakati pa anthu amene amatumikila Yehova na amene sam’tumikila?
10 M’nkhani yapita, tinakambilana za Kaini, Solomo, ndi Aisiraeli. Onse anali kudzinenela kuti anali kulambila Yehova, koma sanali okhulupilika kwa iye. Zitsanzo zimenezi zionetsa bwino kuti anthu a Yehova afunika kugwilitsitsa colungama na kudana ndi coipa. (Aroma 12:9) Mpake kuti Malaki atakamba za “buku la cikumbutso,” Yehova anakamba kuti padzakhala “kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikila Mulungu ndi amene sanatumikilepo Mulungu.”—Mal. 3:18.
11. N’cifukwa ciani anthu ena afunika kuona kuti tinadzipatulila kwa Yehova?
11 Pamenepa tikupezapo njila ina imene tingaonetsele kuti timamuyamikila Yehova potisankha kukhala anthu ake. Tifunika kuonetsetsa kuti kupita kwathu patsogolo mwauzimu kukuwonekela kwa “anthu onse.” (1 Tim. 4:15; Mat. 5:16) Dzifunseni kuti, ‘Kodi anthu ena amaona kuti ndine wokhulupilika kwa Yehova? Kodi nimayesetsa kusakila mipata yodzidziŵikitsa kuti ndine wa Mboni za Yehova?’ Yehova angakhumudwe kwambili ngati ise amene watisankha kukhala anthu ake, timayopa kudzidziŵikitsa kwa ena kuti ndise Mboni zake.—Sal. 119:46; ŵelengani Maliko 8:38.
12, 13. Kodi Akhristu ena amacita zotani zimene zapangitsa kuti asamasiyane kweni-kweni ndi anthu a ku dziko?
1 Akor. 2:12) Mzimu wa dziko umalimbikitsa munthu ‘kutsatila zilakolako za thupi lake.’ (Aef. 2:3) Mwacitsanzo, ngakhale kuti timalandila malangizo mobweleza-bweleza pa nkhani ya kavalidwe, ena akupitilizabe kuvala mosadzilemekeza komanso kudzikonza mosayenela. Iwo amavala zovala zothina ndi zoonetsa thupi, ngakhale popita ku misonkhano. Ena amatengela masitayelo a kudziko a kageledwe na kamangidwe ka tsitsi. (1 Tim. 2:9, 10) Conco akakhala pa gulu, cimakhala covuta kusiyanitsa pakati pa munthu amene ali ku mbali ya Yehova ndi amene ni ‘bwenzi la dziko.’—Yak. 4:4.
12 N’zomvetsa cisoni kuti anthu ena a Mulungu ayamba kutengela “mzimu wa dziko.” Mwa ici, iwo sasiyana kweni-kweni ndi anthu ‘amene satumikila Mulungu.’ (13 Pali zinthu zina zimene Akhristu ena amacita, zoonetsa kuti sanasiiletu khalidwe la kudziko. Kavinidwe kawo komanso zocita zawo pa maphwando, zimakhala zosayenela kwa Akhristu. Palinso Akhristu ena amene amaika mapikica osayenela pa intaneti kapena kulembapo zinthu zina zosayenela. Iwo angakhale kuti sanacite chimo lalikulu moti n’kupatsidwa cilango mu mpingo. Koma zocita zawo zingasokoneze ena amene akuyesetsa kukhala na khalidwe labwino pakati pa anthu a Yehova.—Ŵelengani 1 Petulo 2:11, 12.
14. N’ciani cimene tiyenela kucita kuti titeteze ubwenzi wathu wapadela na Yehova?
14 Dzikoli limalimbikitsa kwambili “cilakolako ca thupi, cilakolako ca maso ndi kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Koma ise anthu a Yehova, timalimbikitsidwa kuti tiyenela “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, acilungamo ndi odzipeleka kwa Mulungu m’nthawi ino.” (Tito 2:12) Kakambidwe kathu, kadyedwe ndi kamwedwe, kavalidwe na kudzikonza kwathu, ngakhale mmene timaseŵenzela ku nchito, zonse ziyenela kuonetsa kuti ndise anthu odzipatulila kwa Yehova.—Ŵelengani 1 Akorinto 10:31, 32.
TIMAKONDANA KWAMBILI
15. N’cifukwa ciani tifunika kucita zinthu mokoma mtima ndi mwacikondi na Akhristu anzathu?
15 Njila ina imene timaonetsela kuti timayamikila Yehova potipatsa mwayi wokhala naye pa ubwenzi wapadela, ni mmene timacitila zinthu na Akhristu anzathu. Nawonso ni anthu a Yehova. Ngati sitiiŵala mfundo imeneyi, ndiye kuti nthawi zonse tidzayamba kucita zinthu mokoma mtima ndi mwacikondi na abale na alongo athu. (1 Ates. 5:15) Yesu anauza otsatila ake kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:35.
16. N’citsanzo citi ca m’Cilamulo ca Mose coonetsa mmene Yehova amaonela anthu ake?
16 Kuti timvetsetse mmene tifunika kucitila zinthu na Akhristu anzathu mumpingo, ganizilani izi: M’nthawi ya Aisiraeli, ziwiya za m’kacisi wa Yehova zinali kukhala zopatulika. Zinali kugwilitsidwa nchito cabe pa kulambila koona. Cilamulo ca Mose cinali na malangizo omveka bwino a mmene Aisiraeli anafunika kusamalila ziwiyazo, ndipo aliyense wophwanya malangizowo anali kuphedwa. (Num. 1:50, 51) Ngati Yehova anali kuteteza mwamphamvu conco zipangizo za pa kacisi, kuli bwanji atumiki ake odzipatulila ndi okhulupilika amene wawasankha kukhala anthu ake? N’zosacita kufunsa kuti iye amawateteza kwambili. Pokamba na anthu ake, Yehova anati: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.”—Zek. 2:8.
17. Kodi Yehova ‘amachela khutu ndi kumvetsela’ ciani?
17 N’zocititsa cidwi kuti Malaki anakamba kuti Yehova ‘amachela khutu ndi kumvetsela’ pamene anthu ake akukambilana wina na mnzake. (Mal. 3:16) Zoonadi, “Yehova amadziŵa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Iye amaona ciliconse cimene timacita na kukamba. (Aheb. 4:13) Ngati tacita zinthu mosakomela mtima Akhristu anzathu, Yehova ‘amachela khutu ndi kumvetsela.’ Ndipo ngati timacelezana, kupatsana zinthu mowoloŵa manja, kukhululukilana, ndi kukomelana mtima, Yehova amaonanso zimenezo.—Aheb. 13:16; 1 Pet. 4:8, 9.
“YEHOVA SADZATAYA ANTHU AKE”
18. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwayi wathu wokhala anthu a Yehova?
18 Mwacionekele, ise tonse timafunitsitsa kuonetsa kuti timamuyamikila Yehova potipatsa mwayi wokhala anthu ake. Timadziŵa kuti kudzipatulila kwa iye ndiye cinthu canzelu kwambili cimene tinacita mu umoyo wathu. Olo kuti tikukhala “pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota,” timafuna kuti anthu aone kuti ndise ‘opanda cifukwa cotineneza naco ndiponso osalakwa,’ owala ‘pakati pawo monga zounikila m’dzikoli.’ (Afil. 2:15) Timayesetsa kukana zoipa. (Yak. 4:7) Komanso, timakonda na kulemekeza olambila anzathu, podziŵa kuti nawonso ni anthu a Yehova.—Aroma 12:10.
19. Kodi Yehova amawadalitsa bwanji anthu ake?
19 Baibo inalonjeza kuti: “Yehova sadzataya anthu ake.” (Sal. 94:14) Iye sangatitaye olo titakumana na mavuto aakulu bwanji. Ngakhale imfa siingathe kutilekanitsa na cikondi ca Yehova. (Aroma 8:38, 39) “Tikakhala ndi moyo, timakhalila moyo Yehova, ndipo tikafa, timafela Yehova. Cotelo kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Ndipo tikuyembekezela mwacidwi nthawi imene Yehova adzaukitsa mabwenzi ake onse okhulupilika amene anafa. (Mat. 22:32) Ngakhale lomba, tikulandila madalitso ambili. Mpake kuti Baibo imati, “wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala colowa cake.”—Sal. 33:12.