Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Inatha Nchito Kapena Imakambilatu Zinthu Zimene Anthu Akalibe Kuzitulukila?

Kodi Inatha Nchito Kapena Imakambilatu Zinthu Zimene Anthu Akalibe Kuzitulukila?

NKHANI ZA SAYANSI

BAIBO SI BUKU LA SAYANSI, KOMA PALI ZINTHU ZOONA ZIMENE INAKAMBILATU KALE-KALE ANTHU AKALIBE KUZITULUKILA. GANIZILANI ZITSANZO ZOCEPA IZI.

Kodi cilengedwe cinali na ciyambi?

Asayansi ochuka poyamba anali kukana kwa mutu wagalu kuti iyai. Koma masiku ano iwo amavomeleza kuti cilengedwe cinali na ciyambi. Baibo inakambilatu momveka bwino zimenezi.—Genesis 1:1.

Kodi dziko limaoneka bwanji?

M’nthawi zamakedzana, anthu ambili anali kukhulupilila kuti dziko ni lafulati. M’zaka za m’ma 400 B.C.E., asayansi acigiriki anakamba kuti dziko ni lozungulila. Koma zaka zimenezi zikalibe kufika, ca m’ma 700 B.C.E, wolemba Baibo Yesaya analemba kuti: ‘Dziko lapansi ni lozungulila.’—Yesaya 40:22.

Kodi zinthu za kuthambo zimawonongeka m’kupita kwa nthawi?

Katswili wina wa sayansi wacigiriki dzina lake Aristotle, wa m’zaka za m’ma 300 B.C.E., anali kuphunzitsa kuti zinthu zimene zimawonongeka ni za padziko cabe, koma zinthu za ku thambo sizisintha kapena kuwonongeka. Ciphunzitso cimeneci cinali cofala kwa zaka mahandiledi ambili. Koma ca m’ma 1800, asayansi anakhazikitsa ciphunzitso cina. Ciphunzitso cimeneci cimati, zinthu zonse za kuthambo kapena zapadziko, m’kupita kwa nthawi zimawonongeka. Mmodzi mwa asayansi amene analimbikitsa ciphunzitso cimeneci ni Lord Kelvin. Iye anazindikila zimene Baibo imakamba ponena za kuthambo na dziko lapansi. Imati: “Ndipo zonsezi zidzatha ngati covala.” (Salimo 102:25, 26) Kelvin anakhulupilila zimene Baibo imaphunzitsa zakuti Mulungu angaletse kuti zolengedwa zake zisawonongeke.—Mlaliki 1:4.

N’ciani cimagwila mapulaneti monga dziko lapansi?

Aristotle anali kuphunzitsa kuti zinthu zonse za kuthambo zili mkati mwa zinthu zooneka monga mabola agilasi, ndipo dziko lapansi ndilo lili pakati peni-peni. Kudzafika ca m’ma 1700.C.E., asayansi anayamba kukhulupilila kuti nyenyezi na mapulaneti onse, zioneka kuti zinangolenjekeka m’malele. Koma Yobu, amene anakhalako kale-kale m’ma 1400 B.C.E., anati za Mlengi, “anakoloŵeka dziko lapansi m’malele.”—Yobu 26:7.

CITETEZO KU MATENDA

BAIBO SI BUKU LOPHUNZITSA ZA MATENDA, KOMA ILI NA MALANGIZO OTSOGOLA PA ZA UMOYO.

Kupatula anthu odwala matenda oyambukila.

Cilamulo ca Mose cinakamba kuti anthu odwala matenda a khate ayenela kukhala kwaokha. Madokota anadziŵa kufunika koseŵenzetsa mfundo imeneyi pambuyo pa milili ya matenda a m’zaka za pakati pa 500 C.E. na 1500 C.E. Mpaka pano mfundo imeneyi yakhala yothandiza.—Levitiko, caputa 13 na 14.

Kusamba m’manja pambuyo pogwila mtembo.

Mpaka kumapeto kwa zaka za m’ma 1800, madokota nthawi zambili anali kusamalila mitembo kenako n’kusamalila anthu odwala, cosasamba m’manja. Mcitidwe umenewo unabweletsa imfa zambili. Koma Cilamulo ca Mose cinakamba kuti aliyense wogwila mtembo anali wodetsedwa. Cinapeleka malangizo akuti zimenezi zikacitika, munthu anali kufunika kuyeletsedwa na madzi, motsatila mwambo wa m’cilamulo. Zimenezi zinalinso ndi maubwino pa nkhani ya umoyo na thanzi.—Numeri 19:11, 19.

Kutaya zonyansa za munthu.

Caka ciliconse, ana opitilila 500,000 amafa cifukwa ca matenda othulula. Nthawi zambili zimakhala cifukwa ca kusataya moyenelela zonyansa za anthu. Cilamulo ca Mose cinakamba kuti zonyansa za munthu ziyenela kufoceledwa kutali na malo okhala anthu.—Deuteronomo 23:13.

Nthawi yabwino yocita mdulidwe.

Malinga ni Cilamulo ca Mulungu, mwana wa mwamuna anali kudulidwa pa tsiku la namba 8 kucokela pamene anabadwa. (Levitiko 12:3) Capezeka kuti magazi a makanda amatha kuundana mosavuta pakapita wiki imodzi kucokela pamene anabadwa. M’nthawi za m’Baibo kunalibe njila zamakono zotsogola zacipatala. Koma kucita mdulidwe pambuyo pa wiki imodzi kunali citetezo cabwino.

Mgwilizano umene ulipo pakati pa maganizo na thanzi la munthu.

Ofufuza za mankhwala ndi asayansi amakamba kuti kusangalala, kukhala na ciyembekezo, kuyamikila, na kukhululukila ena ndi mtima wonse, kuli na maubwino ake pa thanzi la munthu. Baibo imati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—Miyambo 17:22.