Ziphunzitso za m’Baibo N’zothandiza Nthawi Zonse
GANIZILANI IZI: Muli ku malo osungilako zinthu zakale, ndipo kuli zoumba zakale-kale. Zambili n’zogamphuka-gamphuka, zophwanyika, komanso zosaoneka bwino. Ndipo zina mbali yaikulu kulibe. Koma coumba cimodzi cili bwino-bwino mmene anacipangila. Ndiyeno imwe mufunsa wokuonetsani malo kuti, “Kodi ici n’canyowaniko?” Iye ayankha kuti, “Ndiye cakale kwambili kuposa zonsezi, ndipo sanacikonzeko.” Mufunsanso kuti, “Koma kodi cakhala cikutetezedwa?” Iye akuuzani kuti, “Iyayi, ici calimbana na mphepo na mvula za mphamvu. Komanso, anthu oipa ambili ayesa-yesa kuciwononga.” Mwacidziŵikile, podabwa mungafunse kuti, ‘Kodi cinapangiwa na ciani?’
Mofananamo, Baibo ili ngati coumba cocititsa cidwi cimeneco. Ni buku lakale kwambili kuposa ena oculuka. N’zoona kuti pali mabuku ena akale. Koma mofanana ndi zoumba zakale zogomoka-gomoka, mabuku ambili anaonongeka m’kupita kwa nthawi. Mwacitsanzo, mfundo za m’mabuku a sayansi zimasutsidwa na cidziŵitso catsopano na mfundo zokhala na maumboni ake. Malangizo a m’mabuku a zamankhwala, amene kale anali kudziŵika kuti ni othandiza, m’kupita kwa nthawi anapezeka kuti ni oopsa. Ndipo masiku ano mabuku ambili akale anatsala ni zidutswa-zidutswa cabe, mbali zina zinataika, zina zinathelatu.
Baibo ni yosiyana kwambili na mabuku ena. Inayamba kulembedwa zaka 3500 zapitazo, koma ikali yathunthu ndipo mfundo zake sizinasinthe. Kwa zaka mahandiledi ambili, Baibo yapita m’zovuta zosiyana-siyana. Ena ayesa kuiocha, kuletsa kuifalitsa, na kuisutsa. Ngakhale kuti Baibo yacitilidwa nkhanza zonsezi, siinasinthe. Mfundo zake siziloŵedwa m’malo na cidziŵitso catsopano. Komanso, Baibo ni yocititsa cidwi pa nkhani yokambilatu za mtsogolo.—Onani Kodi inatha nchito kapena imakambilatu zinthu zimene anthu akalibe kuzitulukila?”
bokosi yakuti, “MFUNDO ZOTHANDIZA MASIKU ANO
Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi mfundo za m’Baibo zingakhale zothandiza masiku ano?’ Kuti mupeze yankho dzifunseni kuti: ‘Ni mavuto aakulu ati amene anthu amakumana nawo masiku ano? Nanga oopsa kwambili ni ati?’ Mwina mungaganizile za nkhondo, kuonongeka kwa zacilengedwe, ciwawa, kapena ziphuphu. Ndiyeno ganizilani mfundo zimene Baibo imaphunzitsa. Pamene mucita zimenezo dzifunseni kuti, ‘Sembe anthu amatsatila mfundo zimenezi, kodi dziko siikanakhala malo abwino?’
KUKONDA MTENDELE
“Odala ndi anthu amene amabweletsa mtendele, cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.” (Mateyu 5:9) “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendele ndi anthu onse, monga mmene mungathele.”—Aroma 12:18.
CIFUNDO, KUKHULULUKA
“Odala ndi anthu acifundo, cifukwa adzacitilidwa cifundo.” (Mateyu 5:7) “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova * anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.”—Akolose 3:13.
MGWILIZANO WA ANTHU AMITUNDU YOSIYANA-SIYANA
“Kucokela mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.” (Machitidwe 17:26) “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
KUSAMALILA ZACILENGEDWE
“Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja n’kumuika m’munda wa Edeni kuti aziulima ndi kuusamalila.” (Genesis 2:15) Mulungu adzaononga “amene akuononga dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:18.
KUDANA NDI UMBOMBO NDI ZACIWELEWELE
“Cenjelani ndi kusilila kwa nsanje kwamtundu uliwonse, cifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zoculuka cotani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) “Dama ndi conyansa camtundu uliwonse kapena umbombo zisachulidwe n’komwe pakati panu, monga mmene anthu oyela amayenela kucitila.”—Aefeso 5:3.
KUONA MTIMA, KULIMBIKA PA NCHITO
“Tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) “Wakubayo asabenso, koma agwile nchito molimbikila.”—Aefeso 4:28.
KUTHANDIZA OSOŴA
“Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wacisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Atesalonika 5:14) “Kusamalila ana amasiye ndi akazi amasiye m’masautso awo.”—Yakobo 1:27.
Baibo siimachula cabe mfundo zimenezo. Koma imatilangizanso kuzikonda na kuziseŵenzetsa mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku. Kukanakhala kuti anthu ambili amatsatila mfundo zimene tachulazo, sembe mavuto a anthu padziko anacepa. Zoonadi, mfundo za m’Baibo n’zothandiza kwambili maka-maka masiku ano. Nanga zimene Baibo imaphunzitsa zingakuthandizeni bwanji masiku ano?
MMENE BAIBO INGAKUTHANDIZILENI MASIKU ANO
Munthu wanzelu kupambana onse anati: “Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.” (Mateyu 11:19) Kodi simukuvomeleza zimenezi? Nzelu yeni-yeni imaoneka mukaiseŵenzetsa. Ndiye mungafunse kuti: ‘Ngati Baibo ni yothandizadi, kodi thandizo lake silifunikila kuonekela mu umoyo wanga? Inganithandize bwanji pa mavuto amene nimakumana nawo?’ Ganizilani citsanzo ici.
Delphine * poyamba, zonse zinali kumuyendela bwino. Koma mwadzidzidzi umoyo wake unasinthilatu pamene masoka anatsatizana. Mwana wake wacitsikana anamwalila. Cikwati cake cinasokonezeka. Ndalama zake zinamuthela. Iye anati: “N’nadzimva kukhala munthu wopanda pake, n’nalibenso mwana, n’nalibenso nyumba, n’nalibenso mwamuna. N’nadzimva kukhala wacabe-cabe, n’nalibe mphamvu, n’nalibenso tsogolo.”
Tsopano, Delphine anamvetsa kuti mau awa ndi oona, akuti: “Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadela amakwana zaka 80. Koma ngakhale zili conco, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka. Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timacoka mofulumila.”—Salimo 90:10.
Delphine anapeza thandizo m’Baibo pa nthawi 1 Atesalonika 2:13.
yovuta imeneyi. Inamuthandiza maningi. Monga mmene tionele m’nkhani zitatu zotsatila, ambili apeza kuti kuseŵenzetsa malangizo a m’Baibo kwaŵathandiza kwambili kulimbana na mavuto mu umoyo. Iwo afika poona Baibo monga coumba cija cimene cafotokozedwa kuciyambi. Baibo ni yosiyana na mabuku ambili amene amatha nchito. Kodi kungakhale kuti Baibo inapangiwa mosiyana na mabuku ena? Kodi n’kuthekadi kuti maganizo ali m’Baibo ni a Mulungu, osati a anthu?—Mwina na imwe mwafika povomeleza kuti moyo ni waufupi, wodzala na mavuto. Nanga mavuto akakukulilani msinkhu, kodi mumapeza kuti citonthozo, cilimbikitso, na malangizo odalilika?
Tiyeni tione njila zitatu zikulu-zikulu za mmene Baibo ingakhalile yothandiza mu umoyo wanu. Ingakuthandizeni kudziŵa mmene
-
mungapewele mavuto ngati n’kotheka.
-
mungathetsele mavuto akabuka.
-
mungapililile mukakumana na mavuto amene simungawathetse.
Nkhani zotsatila zidzafotokoza mbali zitatu zimenezi.