Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

1 Thandizo pa Kupewa Mavuto

1 Thandizo pa Kupewa Mavuto

Baibo imakamba kuti uphungu wake ni wouzilidwa, komanso ni “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu.” (2 Timoteyo 3:16) Kodi zimenezi n’zoona? Onani mmene malangizo anzelu a m’Baibo athandizila anthu kupewa mavuto aakulu zinthu zikalibe kufika poipilatu.

KUMWA MOŴA MOPITILILA MALILE

Delphine, amene tam’chula m’nkhani yapita anati nkhawa ndiye zinalengetsa kuti azimwa moŵa kwambili. Baibo siiletsa kumwa moŵa mwacikati-kati, koma imati: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambili.” (Miyambo 23:20) Kumwa moŵa mopitilila malile kumawononga thanzi la munthu, vikwati vimagwedezeka na kutha, ndipo anthu mamiliyoni amafa mwamsanga caka ciliconse cifukwa ca moŵa. Anthu akhoza kupewa mavuto onsewa ngati atsatila malangizo anzelu a m’Baibo.

N’zimene Delphine anacita. Iye anati: “N’nazindikila kuti moŵa sunali kuthetsa nkhawa zanga. N’natsatila malangizo anzelu opezeka pa Afilipi 4:6, 7, amene amati: ‘Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.’ Usiku ulionse nikayamba kuvutika maganizo, na nkhawa zikanipanikiza, n’nali kum’condelela Yehova m’pemphelo. N’nali kumufotokozela nkhawa zanga, mkwiyo, kukhumudwa, na kudziimba mlandu. Ndipo n’nali kum’condelela kuti anithandize kuti niyambe kukhala na maganizo abwino. Kukaca m’maŵa n’nali kucita zonse zotheka kuti nicotse maganizo olakwika amenewo. Kupemphela kunan’thandiza kuti niziika maganizo anga pa zinthu zimene nili nazo osati zimene nilibe. N’nasankha kulekelatu moŵa. N’nacita zimenezi kuti n’satayenso mtendele wamtengo wapatali umene n’naupeza.”

ZA CIWELEWELE

Ciwelewele cimacititsa mavuto aakulu ndi ozunza kwambili. Koma mfundo za m’Baibo zingatithandize kupewa mavuto amenewo mwa kudziŵa zimene zimaayambitsa, monga kuceza kokopana na kutamba zamalisece. Mnyamata wina dzina lake Samuel anati: “Cinali cosavuta kuyamba cizoloŵezi cokopana. Zinali kucitika kuti sin’nali kukopeka naye mtsikana, koma n’nali kuona kuti iye amanikonda. Basi n’nali kuyamba kumaceza naye.” Nthawi zambili Samuel anali kudabwa kuti anthu akumuuza kuti amakonda kuceza mokopana ndi atsikana, ngakhale pamene sanafune kutelo. Pothela pake, anayamba kucita zimenezo mwadala. Koma khalidwe limeneli linali kum’vutitsa maganizo. Iye anati: “Khalidwe limeneli n’loipa cifukwa umakhala na mzimu wadyela kwambili.”

Samuel anaŵelenga nkhani ya acicepele imene anapeza pa webusaiti ya jw.org. Iye anaganizila lemba la Miyambo 20:11 imene imati: “Ngakhale mnyamata amadziwika ndi nchito zake, ngati zocita zake zili zoyela ndiponso zowongoka.” Kodi lembali linam’thandiza bwanji? Samuel anazindikila kuti kukopana si khalidwe loyela kapena loongoka. Iye anati: “N’nazindikila kuti ngati wacicepele ali na khalidwe lokonda zokopana adzakhala ndi mavuto akadzaloŵa m’banja. N’naganizila za mmene mkazi wanga angadzamvelele pondiona nikuceza mokopana na mkazi wina. Izi zinan’thandiza kuzindikila kuti ni khalidwe loipa. Ngakhale kuti n’cosavuta kuyamba khalidwe limeneli, sizitanthauza kuti n’labwino.” Samuel anasintha. Kuleka khalidwe limeneli kwam’thandizanso kupewa ciwelewele.

Antonio anali paciopsezo cacikulu cokhudza zaciwelewele. Anali atatengekeka ndi khalidwe lotamba zamalisece. Olo kuti anali kukonda mkazi wake kwambili, anali kugonjabe ku cizoloŵezi cimeneci nthawi ndi nthawi. Iye anati kuganizila lemba la 1 Petulo 5:8 kunamuthandiza kwambili. Lembali limati: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyelekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” Antonio anakamba kuti: “Zithunzi zamalisece zili paliponse m’dzikoli, ndipo zikhoza kukhazikika m’maganizo. Lembali linan’thandiza kuganizila amene amabweletsa mayeselo amenewa. N’nali kukumbukila mwamsanga uyo anali kuseli kwa zithunzi zonyansazo. Lomba n’nazindikila kuti Yehova yekha ndiye angan’thandize ‘kukhalabe woganiza bwino na kukhala maso,’ kuti nikwanitse kulimbana na zimene zingawononge maganizo anga, mtima wanga, na cikwati canga.” Antonio anapeza thandizo lofunikila, ndipo tsopano analeka khalidwe lake loipalo. Izi zinam’thandiza kuti vuto lake lisafike poipilatu.

Taona bwino lomwe kuti Baibo ili na uphungu wothandiza pa kupewa mavuto aakulu. Nanga bwanji za mavuto amene anazika kale mizu, ndipo aoneka kuti sadzatha? Tiyeni tione mmene Mau a Mulungu angatithandizile kuthetsa mavuto amenewo.

Uphungu wa m’Baibo ungatithandize kupewa mavuto