1 | Pemphelo—“Mutulileni Nkhawa Zanu Zonse”
BAIBO IMATI: ‘Mutulileni Mulungu, nkhawa zanu zonse. Pakuti amakudelani nkhawa.’—1 PETULO 5:7.
Tanthauzo Lake
Yehova Mulungu akutipempha kuti tizimuuza nkhawa zilizonse zimene tili nazo. (Salimo 55:22) Palibe vuto lalikulu kwambili kapena laling’ono kwambili limene sitingamuuze m’pemphelo. Ngati ife tiona kuti ni vuto, ndiye kuti nayenso Yehova amaona kuti ni vuto cifukwa amasamala za ife. Kupemphela kwa iye n’kofunika cifukwa kumatithandiza kukhala na mtendele wa mumtima.—Afilipi 4:6, 7.
Mmene Kucita Zimenezi Kungatithandizile
Tikamadwala matenda a maganizo, tingaone monga kuti palibe aliyense amene akuona zimene tikupitamo. Zili conco cifukwa nthawi zina anthu sangamvetse vuto lathu. (Miyambo 14:10) Koma tikamuuza Mulungu mocokela pansi pa mtima mmene tikumvela, iye adzatimvetsela mokoma mtima. Yehova amationa. Amadziŵa zimene zimatipweteka mtima komanso mavuto amene timakumana nawo. Ndipo amafuna kuti tizimuuza m’pemphelo zilizonse zimene zimatidetsa nkhawa.—2 Mbiri 6:29, 30.
Kupemphela kwa Yehova kungalimbitse cidalilo cathu cakuti iye amasamala za ife. Tingamve mmene wamasalimo anamvela pamene anapemphela kuti: “Mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwela.” (Salimo 31:7) Kungodziŵa kuti Yehova amaona mavuto amene timapitamo, kungatithandize kupitiliza kupilila mavutowo. Koma sikuti Mulungu amangowaona mavutowo. Amacitapo kanthu. Kuposa munthu wina aliyense, Yehova amamvetsetsa mavuto amene timakumana nawo, ndipo amatithandiza kupeza cilimbikitso m’Baibo.