Kodi Inu Mudzatsatila Malangizo a Ndani?
Zimene timasankha kucita pali pano n’zimene zingapangitse kuti tikakhale na cimwemwe mtsogolo kapena ayi. Ndipo Yehova Mulungu adziŵa zimenezi. Ndiye cifukwa cake amafuna tizitsatila mfundo zake za makhalidwe abwino.
Yehova afuna kuti tikhale na umoyo wamtendele komanso wacimwemwe.
“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakutsogolelani mʼnjila imene mukuyenela kuyenda. Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje ndipo cilungamo canu cidzakhala ngati mafunde a mʼnyanja.”—Yesaya 48:17, 18.
Pokhala Mlengi wathu, Mulungu amadziŵa bwino mmene tiyenela kukhalila kuti zinthu zitiyendele bwino. Amafuna kuti tizitsatila malangizo ake cifukwa angatithandize. Tikamatsatila malamulo a Mulungu, sitingakayikile kuti zosankha zathu zidzakhala na zotulukapo zabwino. Koma nthawi zonse tidzayamba kupanga zisankho zabwino zimene zidzatibweletsela mtendele na cimwemwe.
Yehova satipempha kucita zimene sitingakwanitse.
“Lamulo limene ndikukupatsani leloli si lovuta kwa inu kulitsatila, ndipo silili poti simungathe kulipeza.”—Deuteronomo 30:11.
Kuti titsatile mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino tiyenela kusintha maganizo athu na makhalidwe athu. Koma zimene Yehova amatiuza kucita si zovuta. Tikutelo cifukwa pokhala Mlengi wathu, iye amadziŵa zimene tingakwanitse kucita. Tikafika pom’dziwa bwino Yehova, tidzaona kuti “malamulo akewo si ovuta kuwatsatila.”—1 Yohane 5:3.
Yehova analonjeza kuti adzatithandiza tikamatsatila mfundo zake.
“Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwila dzanja lako lamanja, ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—Yesaya 41:13.
N’zotheka kutsatila mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino, cifukwa iye adzatithandiza. Angatithandize kupitila m’Mawu ake, Baibo, amene amatilimbikitsa na kutipatsa ciyembekezo.
Anthu mamiliyoni padziko lonse aona kuti kutsatila malangizo a m’Baibo kwawathandiza kukhala na umoyo wabwino. Bwanji osaphunzila Baibo kuti mudziwe malangizo abwino amene limapeleka? Mungayambe kuphunzila mwa kuŵelenga bulosha yofotokoza mfundo za m’Baibo yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Ni yaulele, ndipo ipezeka pa jw.org. Ili na nkhani izi:
-
Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
-
Baibo Imatilonjeza Moyo wa Cimwemwe Kutsogolo
-
Kodi Muyenela Kuikhulupilila Baibo?
Mukamaphunzila Mawu a Mulungu, Baibo, mudzaona kuti mfundo zake n’zothandizabe masiku ano. Mawu ake ni “odalilika nthawi zonse, kuyambila panopa mpaka kalekale.” (Salimo 111:8) Tingakhale na umoyo wabwino kwambili tikamatsatila mfundo za m’Baibo za makhalidwe abwino. Koma Mulungu satikakamiza kucita zimenezo. (Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:15) Ni cisankho ca aliyense payekha.