Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Elias Hutter na Mabaibo Ake a Ciheberi Ocititsa Cidwi

Elias Hutter na Mabaibo Ake a Ciheberi Ocititsa Cidwi

KODI mungakwanitse kuŵelenga Baibo ya Ciheberi? Mwina simungakwanitse, ndipo n’kutheka kuti simunaionepo. Komabe, mukhoza kuyamikila ngako Baibo yanu ya Malemba Oyela mukaphunzilako zina zake zokhudza Elias Hutter, katswili amene anakhalako zaka za m’ma 1500. Iye anafalitsa Mabaibo aŵili a Ciheberi.

Elias Hutter anabadwa mu 1553, m’tauni yaing’ono yochedwa Görlitz m’dziko la Germany. Tauni imeneyi ili kufupi ndi malile a maiko a Poland na Czech Republic. Hutter anaphunzila vitundu va kumaiko a kum’mawa kwa Asia pa Yunivesite ya Lutheran m’tauni ya Jena. Ali pafupi kufika zaka 24, anasankhidwa kukhala pulofesa wa Ciheberi ku Leipzig. Popeza anali katswili wa zamaphunzilo, iye anayambitsa sukulu ku Nuremberg, ndipo ana a sukulu anali kuphunzila Ciheberi, Cigiriki, Cilatini, na Cijeremani kwa zaka zinayi cabe. Panthawiyo, izi zinali zosatheka m’masukulu kapena m’mayunivisite ena.

“BUKU YOCITITSA CIDWI”

Peji imene pali mutu wa Baibo ya Ciheberi yomasulidwa na Hutter mu 1587

Mu 1587, Hutter anatulutsa Baibo ya Ciheberi imene imadziŵika kwambili kuti Cipangano Cakale. Baibo imeneyo inali kuchedwa kuti Derekh ha-Kodesh, kutanthauza “Msewu wa Ciyelo.” Mau amenewo anacokela pa Yesaya 35:8. Mtundu wa zilembo zake zokongola unapangitsa ena kukamba kuti “zonse zionetsa kuti ni buku yocititsa cidwi.” Koma cimene cinapangitsa Baibo imeneyi kukhala yofunika kwambili, n’cakuti inali kuthandiza kwambili ana a sukulu kuphunzila Ciheberi.

Kuti timvetse cifukwa cake Baibo ya Ciheberi ya Hutter inali yothandiza kwambili, ganizilani mavuto aŵili amene ophunzila analupeza poŵelenga Mabaibo ena a Ciheberi. Coyamba, anali na alifabeti yacilendo, ndipo caciŵili mau ake anali na mphatikila kutsogolo ndi kumbuyo. Mphatikila zimenezi zinali kupangitsa kuti zikhale zovuta kuti azindikile liu lake lenileni. Mwacitsanzo, ganizilani liu la Ciheberi lakuti נפשׁ (limene kachulidwe kake ni ne’phesh), kutanthauza “moyo.” Pa Ezekieli 18:4, m’Cihebeli liu limeneli ili na mphatikila ya ה (ha) kumbuyo kwake, imene ipangitsa liu limenelo kukhala liu limodzi lakuti הנפשׁ (han·ne’phesh). Kwa munthu wosaphunzila, liu lakuti הנפשׁ (han·ne’phesh) lingaoneke losiyana kwambili ndi liu lakuti נפשׁ (ne’phesh).

Kuti athandize ophunzila ake, Hutter anaseŵenzetsa njila yaluso yolembela zilembo. Iye analemba zilembo zina za Ciheberi m’mau akuda kwambili. Mau amene amaonetsa liu lake lenileni anawalemba m’zilembo zakuda kwambili. Mphatikila ya kumbuyo ndi ya kutsogolo anailemba m’zilembo zanthawi zonse (zosada kwambili). Njila imeneyi inathandiza ophunzila kuzindikila liu lake lenileni la Ciheberi, na kuphunzila cineneloco mosavuta. Baibo ya New World Translation of the Holy Scriptures—With References limaseŵenzetsa njila yolinganako pa mau ake amunsi. * Liu lake lenileni lili m’zilembo zakuda, ndipo mphatikila zake zinalembewa m’zilembo zanthawi zonse. Zimene takambazo zionetsa mtundu wa zilembo zimene Hutter anaseŵenzetsa m’Baibo yake ya Ciheberi pa Ezekieli 18:4, zimene zipezekanso m’mau amunsi mu Reference Bible pa vesi imodzi-modziyo.

BAIBO YA CIHEBERI YA “CIPANGANO CATSOPANO”

Hutter anafalitsanso Baibo yochedwa Cipangano Catsopano, ndipo inali na zitundu 12. Baibo imeneyo anaipulintila ku Nuremberg mu 1599, ndipo anthu ambili amaicha Nuremberg Polyglot. Hutter anafuna kuwonjezelapo Malemba Acigiriki Acikhristu omasulidwa m’Ciheberi. Koma iye anakamba kuti ngakhale kuti “anali wofunitsitsa kupeleka cuma cake” kuti cithandizile pa nchito yomasulila Ciheberi, kufufuza kwake kukanangopita pacabe. * Conco, iye anaganiza zomasulila yekha Baibo ya Cipangano Catsopano kucoka m’Cigiriki kupita m’Ciheberi. Hutter anaika nchito yake yomasulila Baibo patsogolo, ndipo anaitsiliza m’caka cimodzi cabe!

Hutter anamasulila bwino kwambili Malemba Acigiriki Acikhristu m’Ciheberi. Motani? M’caka ca 1891, katswili wina wa Ciheberi dzina lake Franz Delitzsch analemba kuti: “Baibo ya Ciheberi imene anamasulila inali ndi mau ambili amene Akhristu sanali kuwaseŵenzetsa, ndipo ikali yothandiza pofufuza zinthu. Iye anali kuonetsetsa kuti wasankha mau oyenelela.”

INATHANDIZA KWAMBILI

Hutter sanalemele cifukwa ca nchito yake yomasulila, ndipo mwacionekele Mabaibo ake sanagulidwe kwambili. Komabe, nchito yake inathandiza kwambili. Mwacitsanzo, Baibo yake ya Cipangano Catsopano ya Ciheberi inakonzedwanso na kupulintiwa mu 1661 ndi William Robertson, komanso mu 1789 ndi Richard Caddick. Pomasulila kucokela ku Cigiriki coyambilila, Hutter anaseŵenzetsa dzina lakuti “Yehova” (יהוה, JHVH) pa maina audindo akuti Kyʹri·os (Ambuye), ndi The·osʹ (Mulungu). Anali kucita izi pa mavesi aliwonse ogwila mau Malemba a Ciheberi, kapena akaona kuti vesilo ikukamba za Yehova. Izi n’zocititsa cidwi cifukwa Mabaibo ambili a Cipangano Catsopano mulibe dzina leni-leni la Mulungu. Koma Baibo imene Hutter anamasulila iye anaikamo dzina la Mulungu. Izi zipeleka umboni woonjezeleka wobwezeletsa dzina la Mulungu m’Malemba Acigiriki Acikhristu.

Pamene mudzaonanso dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Malemba Acigiriki Acikhristu kapena m’mau a munsi mu Reference Bible, mukakumbukile za Elias Hutter na Mabaibo ake a Ciheberi ocititsa cidwi.

^ par. 7 Onani mau a munsi aciŵili pa lemba la Ezekieli 18:4 ndi Zakumapeto 3B mu Reference Bible.

^ par. 9 Mwacionekele, akatswili ena anali atafalitsapo kale Baibo ya Cipangano Catsopano yomasulidwa m’Ciheberi. Mmodzi wa iwo anali Simon Atoumanos, wansembe amene anakhalako mu ulamulilo wa Byzantine m’zaka za m’ma 1360. Wina anali Oswald Schreckenfuchs, katswili wa ku German wa m’zaka za m’ma 1565. Mabaibo amenewa sanafalitsidwe ndipo sangapezeke.