Kodi N’zoona Kuti Davide Anamenyana ndi Goliyati?
Anthu ena amaganiza kuti nkhani ya Davide ndi Goliyati ni nthano cabe. Pamene munali kuŵelenga nkhani yapita, kodi inunso munali kukayikila? Ngati n’conco, onani mafunso atatu otsatila.
1 | Kodi munthu angakhale wamtali kufika mamita 2.9?
Baibulo imakamba kuti Goliyati “anali wamtali mikono 6 ndi cikhatho cimodzi.” (1 Samueli 17:4) Mkono umene Baibulo imakamba unali wautali masentimita 44.5, ndipo cikhato cinali cacitali masentimita 22.2. Popeza kuti Goliyati anali wamtali mikono 6 ndi cikhatho cimodzi, ndiye kuti anali wamtali mamita 2.9. Ena amakayikila kuti Goliyati anali wamtali conco. Koma ganizilani izi: Masiku ano, aliko munthu wamtali mamita 2.7. Ngati masiku ano kuli munthu wamtali conco, n’zosadabwitsa kuti Goliyati anali wamtali mamita 2.9 kapena kuposapo. Iye anali wocokela mumtundu wa Arefai, anthu amene anali kudziŵika kuti anali atali-atali kwambili. Cikalata ca ku Iguputo ca mu 1200 B.C.E., cinakamba kuti m’dziko la Kanani munali asilikali ena oopsa amene anali aatali mamita 2.4. Conco, n’zoona kuti Goliyati anali wamtali mamita 2.9.
2 | Kodi Davide anali munthu weni-weni?
Kale, akatswili ena anali kukamba kuti nkhani yakuti kunali Mfumu Davide ni nthano cabe. Koma zimenezi sizoona. Ofufuza zinthu zakale anapeza cikalata cimene cinachulako za “nyumba ya Davide.” Kuwonjezela apo, zimene Yesu Khiristu anakamba zokhudza Davide zionetsa kuti Davideyo anali munthu weni-weni. (Mateyu 12:3; 22:43-45) Pali mibadwo iŵili imene imaonetsa kuti Yesu anali Mesiya. Mibadwo imeneyi imaonetsanso kuti iye anali mbadwa ya Mfumu Davide. (Mateyu 1:6-16; Luka 3:23-31) N’zoonekelatu kuti Davide anali munthu weni-weni.
3 | Kodi malo ochulidwa m’nkhani imeneyi ndi eni-eni?
Baibulo imakamba kuti nkhondo imeneyi inacitikila m’Cigwa ca Ela. Imakambanso kuti Afilisiti anamanga msasa m’mbali mwa phili, pakati pa mizinda iŵili ya Soko ndi Azeka. Aisraeli anamanga msasa m’mbali mwa phili limene linali kutsidya lina la cigwa. Kodi malo amenewa analikodi?
Munthu wina amene anapita kukaona malo amenewa anakamba kuti: “Munthu amene anali kutionetsa malo anatipeleka ku Cigwa ca Ela. Iye sanali wacipembedzo. Tinayenda m’kasewu kupita pamwamba pa phili. Pamene tinali kuyang’ana cigwa, anatiuza kuti tiŵelenge 1 Samueli 17:1-3. Ndiyeno analata kutsidya la cigwa, n’kukamba kuti: ‘Apo, cakumanzele kwathu, ndiye pali mabwinja a Soko.’ Ndiyeno, anatembenuka n’kukambanso kuti, ‘Apo paja, kudzanja lanu la manja, m’pamene pali mabwinja a Azeka. Afilisiti anamanga msasa pakati pa mizinda iŵili imeneyi, m’mbali mwa phili limene mukuliona. Conco, n’kutheka kuti pano pamene taimilila ndiye pamene Aisraeli anamanga msasa.’ N’nayamba kuganiza kuti mwina Sauli ndi Davide anaimilila pa malo amene ine n’naima. Titatsika paphili, tinafika m’cigwa ndi kudutsa kamtsinje kouma kamene munali miyala yambili. Mumtima mwanga n’naganiza kuti mwina pano m’pamene Davide anatola miyala isanu yooneka bwino, kuphatikizapo umene anaphela Goliyati.” Mofanana ndi anthu ambili, munthu wokaona malo ameneyu anacita cidwi kuona kuti Baibulo limakamba zoona zokha-zokha.
Palibe zifukwa zomveka zokayikilila nkhani imeneyi. Imakamba za anthu eni-eni ndiponso malo eni-eni. Koposa zonse, nkhaniyi ndi mbali ya Mau ouzilidwa a Mulungu. Conco ndi yocokela kwa Mulungu wacoodi, “amene sanganame.”—Tito 1:2; 2 Timoteyo 3:16.