Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga
Kodi kuika munthu cizindikilo kofotokozedwa pa 2 Atesalonika 3:14, kuyenela kucitika na akulu kapena wofalitsa aliyense payekha mumpingo?
Mtumwi Paulo analembela Akhristu a ku Tesalonika kuti: “Ngati wina sakumvela mawu athu amene ali mʼkalatayi, muikeni cizindikilo.” (2 Ates. 3:14) Kumbuyoku tinali kunena kuti malangizowa anali kupita kwa akulu. Kale, akulu anali kukamba nkhani ku mpingo ngati mu mpingomo muli munthu amene sasintha khalidwe lake loipa ngakhale kuti akulu amuthandiza mobweleza-bweleza. Zikatelo, ofalitsa anali kuleka kuceza naye munthu woteloyo.
Komabe, payenela kukhala masinthidwe pa nkhaniyi. Malangizo a Paulo amenewa amakamba zimene Mkhristu aliyense payekha ayenela kucita pa mkhalidwe wina wake. Conco palibe cifukwa cakuti akulu apeleke nkhani yocenjeza mpingo. N’cifukwa ciyani pakhala masinthidwe amenewa? Ganizilani zimene Paulo anali kukambapo pomwe anali kupeleka malangizowa.
Paulo anakamba kuti anthu ena mu mpingomo anali ‘kuyenda mosalongosoka.’ Iwo sanali kutsatila malangizo ocokela kwa Mulungu. Paulendo wake wa m’mbuyomo, iye anakamba kuti: “Ngati wina sakufuna kugwila nchito, asadye.” Ngakhale n’telo, ena anali kukana kugwila nchito kuti adzipezele zofunika za paumoyo. Anthuwo anali kukana kugwila nchito ngakhale kuti anali na mphamvu zocitila zimenezi. Cina, anali kuloŵelela m’nkhani za eni. Kodi Akhristu anali kufunika kucita nawo motani anthu amene anali kuyenda mosalongosoka amenewo?—2 Ates. 3:6, 10-12.
Paulo anakamba kuti “muikeni cizindikilo.” Mu Cigiriki, mawu amenewa apeleka lingalilo loika cizindikilo munthu woteloyo. Paulo anali kupeleka malangizo amenewa ku mpingo wonse osati cabe kwa akulu. (2 Ates. 1:1; 3:6) Conco, Mkhristu aliyense amene anaona Mkhristu mnzake sakumvela malangizo ouzilidwa, akanasankha ‘kusiya kucitila naye zinthu limodzi’ munthu ameneyo.
Kodi izi zinatanthauza kuti iwo anayenela kucita naye zinthu munthuyo monga wocotsedwa? Ayi. Tikutelo cifukwa Paulo anawonjezela kuti: “Pitilizani kumulangiza monga mʼbale.” Conco, Mkhristu aliyense anali kuceza na munthuyo pa misonkhano kapena mu ulaliki. Koma anali kusankha kusakhala na munthuyo pa zina monga pa zosangalatsa kapena pa maceza. N’cifukwa ciyani? Paulo anati, kuti munthuyo “acite manyazi.” Tikasiya kuceza na m’bale mwa njila imeneyi, iye angacite manyazi. Izi zingacititse kuti asinthe khalidwe lake na kacitidwe kake ka zinthu.—2 Ates. 3:14, 15.
Kodi Akhristu masiku ano angaseŵenzetse bwanji malangizo amenewa? Coyamba, tiyenela kutsimikiza kuti munthuyo “akuyenda mosalongosoka” monga mmene Paulo anafotokozela. Iye sanali kunena za anthu amene timasiyana nawo zisankho pa nkhani zimene zimafuna cikumbumtima kapena amene timasiyana nawo makonda. Ndipo sanali kukambanso za anthu amene atikhumudwitsa. M’malomwake, Paulo anali kukamba za anthu amene mwadala amasankha kusamvela malangizo omveka bwino amene Mulungu wapeleka.
Ngati taona Mkhristu mnzathu akuonetsa mzimu wosamvela umenewu, a tingapange cisankho cakuti tileke kukhala naye pa zosangalatsa kapena pa maceza. Popeza ici ni cisankho ca munthu mwini, sitiyenela kukambilana za cisankho cathu pa nkhaniyi na anthu ena amene si a m’banja lathu, amenenso sitikhala nawo panyumba. Ndipo tingapitilize kuceza naye munthuyo pa misonkhano komanso mu ulaliki. Munthuyo akasintha khalidwe lake, tingayambilenso kucita naye zinthu monga kale.
a Mwacitsanzo, Mkhristu mnzathu angasankhe kusagwila nchito kuti apeze zomuthandiza paumoyo ngakhale kuti angakwanitse kucita zimenezo. Mwina angasankhenso kukhala pa cibwenzi na munthu wosakhulupilila, kapena angayambe kufalitsa nkhani zotsutsa ziphunzitso zathu kapena kufalitsa mijedo yovulaza. (1 Akor. 7:39; 2 Akor. 6:14; 2 Ates. 3:11, 12; 1 Tim. 5:13) Mkhristu amene amacita zimenezi ndiye kuti “akuyenda mosalongosoka.”