Yehova Amapeleka Mphoto kwa Anthu Omufuna-funa na Mtima Wonse
“Aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi, ndi kuti amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.”—AHEB. 11:6.
1, 2. (a) Kodi cikondi na cikhulupililo n’zogwilizana bwanji?(b) Ni mafunso ati amene tidzakambilana?
TIMAKONDA Yehova “cifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yoh. 4:19) Yehova amaonetsela cikondi cake mwa kupeleka mphoto kwa atumiki ake okhulupilika. Pamene tikonda kwambili Mulungu wathu, m’pamenenso cikhulupililo cathu cimalimba kwambili. Timakhulupilila kuti Iye aliko ndi kuti salephela kupeleka mphoto kwa amene amawakonda.—Ŵelengani Aheberi 11:6.
2 Yehova amakondwela kwambili ndi kupeleka mphoto. Kuti tikhale na cikhulupililo cokwanila, tifunika cidalilo cakuti Mulungu amapeleka mphoto kwa amene amam’funa-funa mwakhama. N’cifukwa cake Baibo imati “cikhulupililo ndico ciyembekezo cotsimikizika ca zinthu zoyembekezeledwa.” (Aheb. 11:1) Inde, cikhulupililo cimaphatikizapo kuyembekezela madalitso amene Mulungu analonjeza. Kodi ciyembekezo codzalandila mphoto cimatithandiza bwanji? Kodi Yehova anadalitsa bwanji atumiki ake akale? Nanga masiku ano? Tiyeni tione.
YEHOVA ANALONJEZA KUTI ADZADALITSA ATUMIKI AKE
3. Kodi pa Malaki 3:10 pali lonjelo lanji?
3 Yehova Mulungu analonjeza kuti adzadalitsa atumiki ake Mal. 3:10) Timaonetsa ciyamikilo cathu ca mtima wonse ngati tilabadila ciitano ca Yehova cimeneci.
okhulupilika. Conco, amatipempha kuti tizicita zinthu zom’kondweletsa kuti tikalandile madalitso ake. M’Baibo timaŵelenga kuti: “‘Ndiyeseni conde, . . . kuti muone ngati sindidzakutsegulilani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulilani madalitso oti mudzasoŵa powalandilila,’ watelo Yehova wa makamu.” (4. N’cifukwa ciani tifunika kudalila mau a Yesu a pa Mateyu 6:33?
4 Yesu anatsimikizila ophunzila ake kuti ngati adzaika Ufumu patsogolo, Mulungu adzawathandiza. (Ŵelengani Mateyu 6:33.) Lonjezo la Yesu limeneli linazikidwa pa malonjezo a Yehova, amene ni odalilika kuyambila kale. Yesu anadziŵa kuti malonjezo a Mulungu salephela. (Yes. 55:11) Ifenso tiyenela kukhulupilila kuti Yehova adzakwanilitsa lonjezo lake lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Tingagwilizanitse mau ouzilidwa amenewa na mau a Yesu olimbikitsa kufuna-funa Ufumu wa Mulungu coyamba na cilungamo cake.
5. N’cifukwa ciani zimene Yesu anayankha Petulo n’zolimbitsa cikhulupililo?
5 Mtumwi Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatilani, kodi tidzapeza ciani?” (Mat. 19:27) Yesu sanam’dzudzule Petulo cifukwa ca funso limeneli. M’malomwake, anauza ophunzila ake kuti adzalandila madalitso cifukwa codzimana zinthu zina. Atumwi okhulupilikawo ndi ena adzalamulila naye kumwamba. Koma ngakhale pali pano ife timapeza madalitso. Yesu anati: “Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda cifukwa ca dzina langa adzalandila zoculuka kwambili kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.” (Mat. 19:29) Yesu anati ophunzila ake adzalandila madalitso oposa zimene anasiya kaamba ka Ufumu. Kodi zimenezo si zoona poyelekezela ndi atate auzimu, amayi, abale, alongo ndi ana amene timapeza?
“NANGULA WA MIYOYO YATHU”
6. N’cifukwa ciani Yehova analonjeza olambila ake mphoto?
6 Yehova analonjeza olambila ake mphoto. Zimenezi zimawathandiza kupilila pamene cikhulupililo cawo ciyetsedwa. Kuwonjezela pa madalitso auzimu amene akusangalala nawo tsopano, atumiki a Yehova Mulungu okhulupilika akuyembekezela mwacidwi kudzalandila madalitso aakulu m’tsogolo. (1 Tim. 4:8) Zoona, kukhala na cidalilo colimba cakuti Yehova “amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse,” kudzatithandiza kukhala olimba m’cikhulupililo.—Aheb. 11:6.
7. Kodi ciyembekezo cingakhale bwanji ngati nangula?
7 Pa Ulaliki wa pa Phili, Yesu anati: “Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:12) Atumiki ena a Mulungu adzalandila mphoto yakumwamba. Ndipo ena adzalandila mphoto ya moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. Cimeneci ni cifukwa cabwino cokhalila ‘okondwela, na kudumpha ndi cimwemwe.’ (Sal. 37:11; Luka 18:30) Kaya ciyembekezo cathu n’cakumwamba kapena ca padziko lapansi, ico cili ngati “nangula wa miyoyo yathu ndipo n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.” (Aheb. 6:17-20) Monga mmene nangula amacilikizila ngalawa ku mphepo yamkuntho, ciyembekezo cathu codzalandila mphoto cingatithandize kukhala osagwedezeka m’maganizo ndi mwauzimu. Cingatithandizenso kupilila mavuto.
8. Kodi ciyembekezo cimatithandiza bwanji kucepetsa nkhawa?
8 Ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cingatithandize kucepetsa nkhawa. Malonjezo a Mulungu ali monga mankhwala ozizilitsa ululu wa nkhawa zathu. Ndithudi, kodi si zotonthoza ‘kutulila Yehova nkhawa zathu’ podziŵa kuti ‘adzaticilikiza’? (Sal. 55:22) Inde, tiyeni tikhale na cidalilo cakuti Mulungu angathe “kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza, malinga ndi mphamvu yake imene ikugwila nchito mwa ife.” (Aef. 3:20) Tangoganizani! Mulungu angacite “zazikulu kwambili,” osati cabe zazikulu.
9. Tingatsimikize bwanji kuti Yehova adzatidalitsa?
9 Kuti tikalandile mphoto, tifunika kukhala na cikhulupililo conse mwa Yehova ndi kulabadila malangizo ake. Mose anauza mtundu wa Isiraeli kuti: “Yehova adzakudalitsa ndithu m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale colowa cako. Adzakudalitsa ngati udzamveladi mau a Yehova Mulungu wako ndi kutsatiladi malamulo onsewa amene ndikukupatsa lelo. Yehova Mulungu wako adzakudalitsa ndithu monga mmene anakulonjezela.” (Deut. 15:4-6) Kodi mumakhulupilila na mtima wonse kuti Yehova adzakudalitsani mukapitiliza kum’tumikila mokhulupilika? Ngati yakho lanu ni inde, simudzagwila mwala.
YEHOVA ANALI KUWADALITSA
10, 11. Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji Yosefe?
10 Baibo inalembewa kuti itipindulitse. Timaŵelengamo nkhani zambili pamene Mulungu anadalitsila atumiki ake okhulupilika. (Aroma 15:4) Citsanzo cabwino ni nkhani ya Yosefe. Cifukwa ca ciwembu ca abale ŵake, ndiponso pambuyo pake kunamizilidwa ndi mkazi wa mbuye wake, Yosefe anapezeka kuti ali m’ndende ku Iguputo. Kodi Mulungu anamusiya? Kutali-tali! Baibo imati: “Yehova anapitilizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha . . . Yehova anali ndi Yosefe, ndipo ciliconse cimene iye anali kucita Yehova anali kucidalitsa.” (Gen. 39:21-23) Panthawi yovuta imeneyo, Yosefe anayembekezela moleza mtima kwa Mulungu wake.
11 Patapita zaka, Farao anamasula Yosefe m’ndende ndi kuika kapolo wodzicepetsayu kukhala wolamulila waciŵili mu Iguputo. (Gen. 41:1, 37-43) Pamene Yosefe anabala ana aŵili amuna, “mwana woyambayo . . . anamucha dzina lakuti Manase, cifukwa anati, ‘Mulungu wandiiŵalitsa mavuto anga onse, ndi nyumba yonse ya bambo anga.’ Waciŵiliyo anamucha Efuraimu, cifukwa anati, ‘Mulungu wandipatsa ana m’dziko la masautso anga.’” (Gen. 41:51, 52) Cifukwa cakuti Yosefe anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu, anadalitsidwa kwambili. Cifukwa ca madalitsowo, iye anapulumutsa Aisiraeli ndi Aiguputo. Mfundo ni yakuti, Yosefe anazindikila kuti Yehova ndiye anam’patsa mphoto na kum’dalitsa.—Gen. 45:5-9.
12. N’ciani cinathandiza Yesu kukhalabe wokhulupilika pamayeselo?
12 Yesu Khiristu nayenso anadalitsidwa cifukwa cokhalabe womvela Mulungu pokumana ndi mayeselo osiyana-siyana. N’ciani cinam’thandiza kupilila? Mau a Mulungu amati: “Cifukwa ca cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake, anapilila mtengo wozunzikilapo. Iye sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila.” (Aheb. 12:2) Yesu anakondwela kwambili kuti anakwanitsa kuyeletsa dzina la Mulungu. Komanso, Atate wake anamuyanja na kumuonjezela maudindo osililika. Baibo imatiuza kuti ‘anakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu.’ Imakambanso kuti: “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomela mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.”—Afil. 2:9.
YEHOVA SAIŴALA ZIMENE TIMACITA
13, 14. Kodi Yehova amamvela bwanji pa zimene timacita kaamba ka iye?
13 Dziŵani kuti Yehova amayamikila zoyesetsa zathu pomutumikila. Amamvetsetsa nkhawa iliyonse imene tingakhale nayo. Amatimvelelanso cifundo ngati tikumana ndi mavuto a zacuma, kapena tikalephela kucita zambili mu utumiki cifukwa ca thanzi lathu kapena kuvutika maganizo. Ndithudi, Yehova amayamikila kwambili zonse zimene atumiki ake amacita kuti akhalebe okhulupilika.—Ŵelengani Aheberi 6:10, 11.
14 Kumbukilaninso kuti tikhoza kufikila “Wakumva pemphelo,” tili na cidalilo cakuti adzamvetsela mavuto athu. (Sal. 65:2) “Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse,” adzapeleka mosaumila thandizo lakuthupi ndi lauzimu limene tingafunikile. Angacite zimenezo ngakhale kupitila mwa Akhiristu anzathu. (2 Akor. 1:3) Yehova amakhudzika mtima pamene ticitila ena cifundo. “Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezela zimene anacitazo.” (Miy. 19:17; Mat.6:3, 4) Conco, tikathandiza anthu amene akuvutika, Yehova amaona zimenezo ngati nkhongole imene tamukongoza. Ndipo walonjeza kuti adzatifupa cifukwa ca kukoma mtima kwathu.
MADALITSO A PANTHAWI INO NA M’TSOGOLO
15. Ni madalitso ati amene muyembekezela mwacidwi? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)
15 Akhiristu odzozedwa amalimbikitsidwa na ciyembekezo cakuti adzalandila ‘cisoti cacifumu cacilungamo. Ambuye, 2 Tim. 4:7, 8) Komabe, ngati Mulungu wakupatsani ciyembekezo cina, sindiye kuti wacita zinthu mopanda cilungamo. Mamiliyoni a “nkhosa zina” za Yesu akuyembekezela mwacidwi mphoto ya mtsogolo ya moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. Mmenemo “adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Yoh. 10:16; Sal. 37:11
woweluza wolungama, adzapeleka mphotoyo m’tsikulo.’ (16. Kodi timapeza citonthozo canji pa 1 Yohane 3:19, 20?
16 Nthawi zina, tingaone kuti siticita zambili mu utumiki wa Mulungu kapena tingakaikile ngati Yehova amakhutila na zimene timacita. Tingakaikilenso kuti ndife oyenelela kudzalandila mphoto iliyonse. Koma tisaiŵale kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziŵa zonse.” (Ŵelengani 1 Yohane 3:19, 20.) Ngakhale ngati zimene timacita pom’tumikila zingaoneke zocepa, Mulungu amayamikilabe na kutidalitsa, malinga ngati timazicita na mtima wonse, komanso cifukwa comukonda.—Maliko 12:41-44.
17. Ni madalitso ena ati amene tili nawo kale?
17 Ngakhale m’masiku ano otsiliza a dongosolo la Satana, Yehova amadalitsabe anthu ake. Amatsimikiza kuti olambila oona akukhala na cakudya cauzimu ca mwana alilenji m’paradaiso wauzimu. (Yes. 54:13) Monga mmene Yesu analonjezela, Yehova watidalitsa pali pano pokhala m’banja lokondana la padziko lonse, banja lauzimu, inde banja la abale na alongo. (Maliko 10:29, 30) Komanso, awo amene amacita khama kufuna-funa Mulungu, amalandila madalitso osaneneka, monga mtendele wa maganizo, kukhala okhutila, na cimwemwe.—Afil. 4:4-7.
18, 19. Kodi atumiki a Yehova amamvela bwanji na madalitso amene amalandila?
18 Zungulile dziko lonse, atumiki a Yehova akhoza kudzikambila okha madalitso amene alandila kwa iye. Mwacitsanzo, Bianca wa ku Germany anati: “Nicita kusoŵa mau oyamikilila Yehova ponithandiza pa nkhawa zanga, na kunicilikiza tsiku ndi tsiku. Kunja kuli msokonezeko wokha-wokha m’dziko. Koma potumikila moyandikana na Yehova, nimamva kukhala wotetezeka m’manja mwake. Pamene nidzimana zinthu pom’tumikila, m’pamenenso iye amaniwonjezela madalitso.”
19 Ganizilaninso za mlongo Paula wa zaka 70 ku Canada, amene sakwanitsa kuyenda cifukwa ca matenda a msana. Iye anati: “Kuleka kuyenda si kutha kwa ulaliki wanga. Nimalalikilabe m’njila zosiyana-siyana, monga pafoni na ulaliki wa mwamwayi. Kuti nizikumbukila mfundo zonilimbikitsa, nimalemba m’kabuku malemba na mfundo za m’zofalitsa zathu kuti niziyang’anamo. Nimakaitana kuti ‘Cithandizo ca Panthawi Yake.’ Tikasumika maganizo pa malonjezo a Yehova, mavuto amaoneka kuti ni a kanthawi cabe. Yehova ni wokonzeka kutithandiza nthawi zonse, olo tikumane na mavuto abwanji.” N’zoona kuti mavuto anu angakhale osiyana ndi a mlongo Bianca ndi a m’bale Paula. Komabe, mukhoza kuganizila njila zimene Yehova wakudalitsilani imwe na anthu ena. N’cinthu colimbikitsa ngako kuganizila mmene Yehova amakudalitsilani pali pano, na mmene adzakudalitsilani m’tsogolo.
20. Kodi tingayembekezele ciani m’tsogolo ngati titumikila Yehova na moyo wathu wonse?
20 Musaiŵale kuti mapemphelo anu ocokela pansi pamtima na ufulu wanu wokamba na Mulungu ‘zidzabweletsa mphoto yaikulu kwambili.’ Dziŵani kuti “mutacita cifunilo ca Mulungu, [mudzalandila] zimene Mulungu walonjeza.” (Aheb. 10:35, 36) Conco, tiyeni tipitilize kulimbitsa cikhulupililo cathu na kutumikila Yehova ndi moyo wathu wonse. Ticite zimenezi podziŵa kuti Yehova adzatipatsa mphoto pa nthawi yake.—Ŵelengani Akolose 3:23, 24.