Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi
Ezekieli caputala 37 imafotokoza ndodo ziŵili zimene zinakhala ndodo imodzi. Kodi izi zitanthauza ciani?
Kupitila mwa mneneli wake Ezekieli, Yehova analosela kuti anthu adzabwelela ku Dziko Lolonjezedwa ndi kugwilizananso kuti akhale mtundu umodzi. Ulosiwo unakambanso kuti anthu amene amalambila Mulungu m’masiku ano otsiliza adzagwilizana ndi kukhala mtundu umodzi.
Yehova anauza mneneli Ezekieli kulemba pa ndondo ziŵili. Pa ndodo yoyamba anafunika kulembapo kuti “Ndodo ya Yuda ndi anzake, ana a Isiraeli.” Ndipo pa ndodo ina anafunika kulembapo kuti, “Ndodo ya Yosefe yoimila Efuraimu komanso anzawo onse a nyumba ya Isiraeli.” Ndodo zimenezi zinafunika kukhala “ndodo imodzi” m’manja mwa Ezekieli.—Ezek. 37:15-17.
Kodi fuko la “Efuraimu” linali kuimila ciani? Fuko la Efuraimu ndiye inali fuko la mphamvu kwambili pa mafuko 10 a ufumu wa Deut. 33:13, 17; 1 Maf. 11:26) Fuko limenelo linacokela kwa Efuraimu mwana wa Yosefe. (Num. 1:32, 33) Yosefe analandila madalitso apadela kucokela kwa Yakobo, atate ake. Conco, m’pomveka kuti “ndodo ya Efuraimu” inaimila mafuko 10 a ufumu wakumpoto. Mu 740 B.C.E. kutatsala zaka zambili kuti Ezekieli alosele, Asuri anagonjetsa ufumu wa Isiraeli wakumpoto ndi kutenga anthu kupita nawo ku ukapolo. (2 Maf. 17:6) Patapita zaka zambili, Ababulo anagonjetsa Asuri. Conco panthawi imeneyo, Aisiraeli ambili amene anatengedwa ukapolo anali atamwazikana mu ufumu wonse wa Babulo.
Isiraeli wakumpoto. Ndipo ngakhale Yerobowamu mfumu yoyamba kulamulila ufumu umenewo anacokela ku fuko la Efuraimu. (Mu 607 B.C.E., Ababulo anagonjetsa mafuko aŵili a ufumu wa Yuda wakumwela ndi kutenga anthu kupita nawo ku Babulo. Ayenela kuti anatenganso anthu ena amene anatsala mu ufumu wa Isiraeli wakumpoto. Mafumu ocokela mu mfuko la Yuda anali kulamulila mu ufumu wa mafuko aŵili amenewa. Ansembe nawonso anali kukhala mu Yuda cifukwa anali kutumikila pa kacisi mu Yerusalemu. (2 Mbiri 11:13, 14; 34:30) Conco mpomveka kukamba kuti ndodo ya “Yuda” inaimila mafuko aŵili a ufumu wakumwela.
Kodi ndodo ziŵili zinaikiwa liti pamodzi? Zinaikiwa mu 537 B.C.E., pamene Aisiraeli anabwelela ku Yerusalemu kuti akamangenso kacisi. Oimila ufumu wa kumwela ndi oimila ufumu wa kumpoto anabwelela nawo limodzi kucoka kuukapolo. Kucokela panthawiyi ana a Isiraeli sanali ogaŵanikana. (Ezek. 37:21, 22) Apa Aisiraeli anayambanso kutumikila Yehova mogwilizana. Mneneli Yesaya ndi Yeremiya analoselapo za mgwilizano umenewu.—Yes. 11:12, 13; Yer. 31:1, 6, 31.
Ni mfundo yofunika iti yokhudza kulambila koona imene inachulidwa mu ulosi umenewu? Ni mfundo yakuti: Yehova adzacititsa kuti onse amene amamulambila akhale ‘amodzi.’ (Ezek. 37:18, 19) Kodi lonjezo limeneli lakwanilitsikadi masiku ano? Inde. Ulosiwu unayamba kukwanilitsika mu 1919 pamene Mulungu anayamba kugwilizanitsa anthu ake pang’ono-pang’ono. Apa, colinga ca Satana cofuna kuwagaŵanitsa cinalepheleka.
Panthawi imeneyo, anthu ambili a Mulungu anali kuyembekezela kuyenda kumwamba ndi kukakhala mafumu ndi ansembe pamodzi ndi Yesu. (Chiv. 20:6) Iwo anali monga ndodo ya Yuda. Koma mkupita kwa nthawi, anthu ambili amene anali kuyembezela kudzakhala padziko lapansi anayamba kudzigwilizanitsa ndi Ayuda auzimu. (Zek. 8:23) Iwo anali monga ndodo ya Yosefe ndipo analibe ciyembekezo codzalamulila ndi Khiristu.
Masiku ano, magulu onse aŵili amatumikila Yehova pamodzi, ndipo ali ndi Mfumu imodzi, Yesu Khiristu. Mu ulosi wa Ezekieli, Yesu anachulidwa kuti “Mtumiki wanga Davide.” (Ezek. 37:24, 25) Yesu anapemphelela ophunzila ake kuti ‘akhale amodzi, mmene iye alili ogwilizana ndi Atate ake.’ * (Yoh. 17:20, 21) Yesu analosela kuti kagulu kang’ono ka odzozedwa pamodzi ndi a “nkhosa zina” kadzakhala “gulu limodzi.” Ndipo onse adzatsatila “m’busa mmodzi.” (Yoh. 10:16) Monga mmene Yesu anafotokozela, anthu onse a Mulungu masiku ano ndi ogwilizana kaya ali ndi ciyembekezo cokakhala kumwamba kapena padziko lapansi.
^ par. 6 Pamene Yesu anali kukamba zimene zidzaonetsa kuti tili m’masiku otsiliza, anafotokozela ophunzila ake mafanizo angapo. Coyamba, anakamba za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” kagulu kang’ono ka abale odzozedwa amene anali kudzatsogolela anthu a Mulungu. (Mat. 24:45-47) Ndiyeno, anapeleka mafanizo okamba za odzozedwa onse. (Mat. 25:1-30) Potsilizila, anakambanso za ena amene adzacilikiza abale a Khiristu ndi kukhala ndi moyo pa dziko lapansi kwamuyaya. (Mat. 25:31-46) Mofananamo, kukwanilitsika koyamba kwa ulosi wa Ezekieli kumakhudza Akhiristu amene ali na ciyembekezo copita kumwamba. Koma ngakhale kuti mafuko 10 a Isiraeli saimila anthu amene adzakhala pa dziko, mgwilizano umene unafotokozedwa mu ulosiwu umatikumbutsa za mgwilizano umene ulipo pakati pa anthu amenewa ndi amene ali na ciyembekezo copita kumwamba.