Lalikilani Uthenga Wabwino Wokamba za Kukoma Mtima
“Kucitila umboni mokwanila za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”—MAC. 20:24.
1, 2. Kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kuyamikila kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?
MOONA mtima, mtumwi Paulo anakamba kuti: “Kukoma mtima kwake kwakukulu kumene [Mulungu] anandisonyeza sikunapite pacabe.” (Ŵelengani 1 Akorinto 15:9, 10.) Paulo anali kudziŵa kuti sanafunike kuonetsedwa cifundo cacikulu ca Mulungu cifukwa anali kuzunza Akhiristu.
2 Kumapeto kwa moyo wake, Paulo analembela Timoteyo kuti: “Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupilika, ndipo anandipatsa utumiki.” (1 Tim. 1:12-14) Ni utumiki uti umenewo? Tipeza yankho pa zimene Paulo anauza akulu a mpingo wa ku Efeso. Iye anati: “Moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ayi. Cimene ndikungofuna n’cakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu, komanso kuti ndimalize utumiki umene ndinalandila kwa Ambuye Yesu basi. Ndikungofuna kucitila umboni mokwanila za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”—Mac. 20:24.
3. Ni utumiki wapadela uti umene Paulo anapatsidwa? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
3 Ni “uthenga wabwino” uti umene Paulo anali kulalikila? Nanga uthengawo unaonetsa bwanji kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova? Paulo anauza Akhiristu a ku Efeso kuti: “Munamva kuti ndinaikidwa kukhala woyang’anila kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kuti ndikuthandizeni.” (Aef. 3:1, 2) Paulo analamulidwa kulalikila uthenga wabwino kwa anthu amene si Ayuda. Zimenezi zinacititsa kuti anthu a mitundu ina akhale mbali ya boma lolamulidwa ndi Mesiya. (Ŵelengani Aefeso 3:5-8.) Paulo anali kulalikila mwakwama, ndipo anasiya citsanzo cabwino kwa Akhiristu masiku ano. Anaonetsadi kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu “sikunapite pacabe.”
KODI KUKOMA MTIMA KWAKUKULU KWA MULUNGU KUMAKULIMBIKITSANI KUCITA CIANI?
4, 5. N’cifukwa ciani tikamba kuti “uthenga wabwino wa Ufumu” n’cimodzi-modzi ndi uthenga wabwino wa “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu”?
4 Anthu a Yehova m’nthawi ya mapeto ino, ali ndi udindo wolalikila “uthenga wabwino . . . wa Ufumu . . . padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Uthenga umene timalalikila umachedwanso “uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” Zili conco cifukwa madalitso onse amene tidzalandila mu Ufumu wa Mulungu, tidzawalandila cifukwa ca kukoma mtima kwa Yehova kumene anationetsa kupitila mwa Khiristu. (Aef. 1:3) Paulo anaonetsa kuti anali kuyamikila kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova mwa kulalikila mwakhama. Kodi timatengela citsanzo cake?—Ŵelengani Aroma 1:14-16.
5 M’nkhani yapita, tinaphunzila mmene ife anthu ocimwa timapindulila ndi kukoma mtima kwakukulu kumene Yehova amaonetsa m’njila zambili. Pa cifukwa cimeneci, tili ndi udindo wophunzitsa ena mmene Yehova akuonetsela cikondi cake ndi mmene iwo angapindulile. Ni mbali ziti za kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu zimene tiyenela kuuzako ena?
LALIKILANI UTHENGA WABWINO WOKAMBA ZA NSEMBE YA DIPO
6, 7. N’cifukwa ciani tingakambe kuti pamene tifotokozela anthu za dipo, ndiye kuti tilalikila uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?
6 Ambili masiku ano samvela cisoni akacimwa, conco samvetsetsa cifukwa cake ife anthu tifunikila dipo. Ngakhale zili conco, ambili sapeza cimwemwe ceni-ceni pa zimene amacita. Sadziŵa kuti chimo n’ciani, mmene imatikhudzila, ndi zimene tiyenela kucita kuti timasuke ku ukapolo wa ucimo. Amadziŵa izi akayamba kuphunzila Baibulo na Mboni za Yehova. Anthu oona mtima amayamikila akadziŵa kuti Yehova, cifukwa ca cikondi ndi kukoma mtima kwake kwakukulu, anatuma Mwana wake padziko lapansi kuti adzatimasule ku ucimo ndi imfa.—1 Yoh. 4:9, 10.
7 Pokamba za Mwana wokondedwa wa Yehova, Paulo anati: “Kudzela mwa iyeyu [Yesu] tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa macimo athu, malinga ndi cuma ca kukoma mtima kwake kwakukulu [kwa Yehova].” (Aef. 1:7) Ngati pali umboni waukulu umene Mulungu anapeleka woonetsa mmene amatikondela, ni nsembe ya dipo ya Khiristu. Nsembeyo imaonetsanso kukoma mtima kwake kwakukulu. Timakondwela kwambili kudziŵa kuti ngati tikhulupilila nsembe ya Yesu, Mulungu adzatikhululukila macimo athu, ndipo tidzakhala ndi cikumbumtima coyela. (Aheb. 9:14) Zoona, umenewu ni uthenga wabwino umene tiyenela kuuzako ena.
THANDIZANI ANTHU KUKHALA MABWENZI A MULUNGU
8. N’cifukwa ciani anthu ocimwa ayenela kugwilizana ndi Mulungu?
8 Tili ndi udindo wouzako anzathu kuti nawonso angakhale pa ubwenzi ndi Mlengi wathu. Ngati anthu sakhulupilila nsembe ya Yesu, Mulungu amawaona kuti ni adani ake. Yohane anati: “Iye wokhulupilila mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvela Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) Ndife okondwa kuti nsembe ya Khiristu imacititsa kuti zikhale zotheka kukhala mabwenzi a Mulungu. Paulo anati: “Inu amene kale munali otalikilana naye ndiponso adani ake cifukwa maganizo anu anali pa nchito zoipa, tsopano wagwilizana nanunso pogwilitsa nchito thupi lanyama la mwanayo kudzela mu imfa yake.”—Akol. 1:21, 22.
9, 10. (a) Ni udindo wa bwanji umene Khiristu anapatsa abale ake odzozedwa? (b) Kodi a “nkhosa zina” amawathandiza bwanji odzozedwa?
9 Khiristu wapatsa abale ake odzozedwa amene ali padziko lapansi “utumiki wokhazikitsanso mtendele.” Pofotokoza za utumiki umenewu, Paulo analembela Akhiristu odzozedwa a m’nthawi ya atumwi kuti: “Zinthu zonse n’zocokela kwa Mulungu, amene anatigwilizanitsa ndi iyeyo kudzela mwa Khiristu, ndipo anatipatsa utumiki wokhazikitsanso mtendele. Utumiki wake ndi woti tilengeze kuti Mulungu anali kugwilizanitsa dziko ndi iyeyo kudzela mwa Khristu, moti sanawaŵelengele anthuwo macimo awo, ndipo watipatsa ifeyo nchito yolengeza uthenga umenewu wokhazikitsanso mtendele. Cotelo ndife akazembe m’malo mwa Khristu, ngati kuti Mulungu akucondelela anthu kudzela mwa ife. Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti: ‘Gwilizananinso ndi Mulungu.’”—2 Akor. 5:18-20.
10 A “nkhosa zina” amaona kuti ni mwayi waukulu kuthandiza odzozedwa pa utumiki umenewu. (Yoh. 10:16) Naonso amatumikila Khiristu, ndipo akucita mbali yaikulu pa nchito yolalikila. Akuphunzitsa anthu coonadi ndi kuwathandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Iyi ni mbali yofunika kwambili pa nchito yolalikila uthenga wabwino wokamba za kukoma mtima kwa Mulungu.
THANDIZANI ANTHU KUDZIŴA KUTI MULUNGU AMAMVETSELA MAPEMPHELO
11, 12. N’cifukwa ciani anthu amakondwela akadziŵa kuti angapemphele kwa Yehova?
11 Anthu ambili amapemphela kuti amveleko cabe bwino, koma sakhulupilila kuti Mulungu amayankha mapemphelo awo. Iwo afunika kudziŵa kuti Yehova ni “Wakumva pemphelo.” Wamasalimo Davide analemba kuti: “Inu Wakumva pemphelo, anthu a mitundu yonse adzabwela kwa inu. Zolakwa zanga zandikulila. Inu mudzatikhululukila macimo athu.”—Sal. 65:2, 3.
12 Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ngati mutapempha ciliconse m’dzina langa, ine ndidzacicita.” (Yoh. 14:14) Izi zitanthauza kuti tingapemphe “ciliconse” cogwilizana ndi zofuna za Yehova. Nayenso Yohane anatitsimikizila kuti: “Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.” (1 Yoh. 5:14) Conco, tiyenela kuthandiza anthu kudziŵa kuti pemphelo silimatithandiza cabe kuti timveleko bwino, koma ni njila yabwino imene timafikila ku “mpando wacifumu wa kukoma mtima kwakukulu.” (Aheb. 4:16) Ngati tiphunzitsa anthu kupemphela m’njila yoyenela, kwa Munthu woyenela, ndi pa zinthu zoyenela, timawathandiza kukhala mabwenzi a Yehova, ndi kupeza thandizo akakumana ndi mavuto.—Sal. 4:1; 145:18.
KUKOMA MTIMA M’DZIKO LATSOPANO
13, 14. (a) Ni udindo wapadela uti umene odzozedwa adzakhala nawo kutsogolo? (b) Ni zinthu zabwino ziti zimene odzozedwa adzacitila anthu?
13 Yehova adzapitiliza kuonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu ngakhale pambuyo pa mapeto a dziko loipali. Pokamba za mwayi wapadela umene Mulungu wapatsa a 144,000 amene adzalamulila ndi Khiristu kumwamba, Paulo analemba kuti: “Mulungu, amene ndi wacifundo coculuka, mwacikondi cake cacikulu cimene anatikonda naco, anatikhalitsa amoyo pamodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa m’macimo, (pakuti inu mwapulumutsidwa cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu) ndipo anatikweza pamodzi, ndi kutikhazika pamodzi m’malo akumwamba mogwilizana ndi Khristu Yesu. Anacita zimenezi kuti mu nthawi zimene zikubwela padzasonyezedwe cuma copambana ca kukoma mtima kwake kwakukulu kumene anatisonyeza mogwilizana ndi Khristu Yesu.”—Aef. 2:4-7.
14 Sitingakwanitse kufotokoza zinthu zonse zosangalatsa zimene Yehova wakonzela Akhiristu odzozedwa amene adzalamulila ndi Khiristu kumwamba. (Luka 22:28-30; Afil. 3:20, 21; 1 Yoh. 3:2) Yehova ‘adzasonyeza cuma copambana ca kukoma mtima kwake kwakukulu’ makamaka kwa odzozedwa. Iwo ndiwo adzakhala “Yerusalemu watsopano,” mkwatibwi wa Khiristu. (Chiv. 3:12; 17:14; 21:2, 9, 10) Adzaseŵenza pamodzi ndi Yesu kuti ‘acilitse mitundu ya anthu.’ Adzathandiza anthu omvela kumasuka ku ukapolo wa ucimo ndi imfa kuti akhale angwilo.—Ŵelengani Chivumbulutso 22:1, 2, 17.
15, 16. Kodi Yehova adzaonetsa bwanji kukoma mtima kwake kwakukulu kwa “nkhosa zina” m’dziko latsopano?
15 Lemba la Aefeso 2:7 likamba kuti Mulungu adzaonetsa kukoma mtima kwakukulu “mu nthawi zimene zikubwela.” Sitikayikila kuti panthawi imeneyo aliyense, pa dziko lapansi adzaona “cuma copambana ca kukoma mtima kwake kwakukulu.” (Luka 18:29, 30) Njila ina yaikulu imene Yehova adzaonetsela kukoma mtima kwake kwakukulu padziko lapansi, ni mwa kuukitsa anthu “m’Manda.” (Yobu 14:13-15; Yoh. 5:28, 29) Amuna ndi akazi okhulupilika amene anafa Khiristu akalibe kupeleka moyo wake nsembe, kuphatikizapo a “nkhosa zina” amene amafa ali okhulupilika kwa Yehova m’masiku otsiliza ano, adzaukitsidwa kuti apitilize kutumikila Yehova.
16 Anthu mamiliyoni ambili amene anamwalila akalibe kudziŵa Mulungu nawonso adzaukitsidwa. Iwo adzapatsidwa mwayi wosankha kaya kulamulidwa ndi Yehova kapena iyayi. Yohane analemba kuti: “Ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimilila pamaso pa mpando wacifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweluzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwilizana ndi nchito zawo. Nyanja inapeleka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapeleka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweluzidwa malinga ndi nchito zake.” (Chiv. 20:12, 13) Anthu amene adzaukitsidwa adzaphunzila mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’Baibulo. Kuwonjezela apo, adzafunika kumvela malangizo atsopano olembedwa “m’mipukutu,” ofotokoza mmene Yehova afuna kuti iwo adzikhalila m’dziko latsopano. Ngakhale malangizo a tsopanowo ni njila ina imene Yehova adzaonetsela kukoma mtima kwake kwakukulu.
PITILIZANI KULALIKILA UTHENGA WABWINO
17. Kodi tiyenela kukumbukila ciani pamene tilalikila uthenga wabwino?
17 Mapeto ali pafupi kwambili. Conco, apa ndiye pamene tiyenela kulalikila kwambili uthenga wabwino. (Maliko 13:10) Kukamba zoona, uthenga wabwino umaonetsa kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. Tizikumbukila zimenezi nthawi zonse pamene tilalikila. Colinga cathu pamene tilalikila, ni kulemekeza Yehova. Tingacite zimenezi mwa kuuza anthu kuti madalitso onse amene tidzalandila m’dziko latsopano adzatheka cifukwa ca kukoma mtima kwa Yehova.
18, 19. Kodi timalemekeza bwanji Yehova cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu?
18 Polalikila, tidziwafotokozela anthu kuti Ufumu wa Khiristu ukayamba kulamulila pa dziko lapansi, anthu adzasangalala ndi zinthu zabwino cifukwa ca dipo, ndipo adzayamba kukhala angwilo pang’ono-pang’ono. Baibulo imati: “Cilengedweco cidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Izi zidzacitika cabe cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.
19 Tili na mwayi wouza anthu onse za madalitso okondweletsa amene ali pa Chivumbulutso 21:4, 5 akuti: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Ndipo Yehova amene ali pampando wacifumu anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” Anakambanso kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalilika ndi oona.” Kukamba zoona, pamene tilalikila uthenga wabwino umenewu kwa ena, timalemekeza Yehova cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu.