Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Acinyamata​—Kodi Mungakonzekele Bwanji Ubatizo?

Acinyamata​—Kodi Mungakonzekele Bwanji Ubatizo?

“Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga.”​—SALIMO 40:8.

NYIMBO: 51, 58

1, 2. (a) N’cifukwa ciani ubatizo ndi cosankha cacikulu? (b) Kodi munthu ayenela kutsimikiza za ciani asanabatizidwe? Nanga n’cifukwa ciani?

KODI ndinu wacinyamata ndipo mufuna kubatizidwa? Ngati n’conco, ubatizo ndiye cinthu cofunika kwambili cimene mungacite. Monga mmene tinakambila m’nkhani yapita, ubatizo ndi cosankha cacikulu. Umaonetsa kuti mwadzipeleka kwa Yehova, kutanthauza kuti mwamulonjeza kuti mudzamutumikila kwamuyaya. Umaonetsanso kuti kucita cifunilo cake ndiye cinthu cofunika kwambili pa umoyo wanu. Lonjezo limeneli ndi nkhani yaikulu. Cotelo, muyenela kubatizidwa kokha ngati mwafikapo mwakuuzimu, mwamvetsetsa zimene kudzipeleka kwa Mulungu kumatanthauza, ndiponso mwasankha nokha kucita zimenezo.

2 Komabe, mwina muona kuti sindinu okonzeka kubatizidwa. Kapena muona kuti ndinu okonzeka, koma makolo anu akuuzani kuti muyembekeze coyamba kuti mukuleko ndi kudziŵa zambili. Ngati ndi conco, kodi muyenela kucita ciani? Musafooke. M’malomwake, panthawi imeneyi, yesetsani kupita patsogolo mwakuuzimu kuti muyenelele ubatizo. Kuti zimenezi zitheke, mungadziikile zolinga pa mbali zitatu izi: (1) pa zikhulupililo zanu, (2) pa zocita zanu, ndi (3) pa mbali ya kukhala woyamikila.

ZIKHULUPILILO ZANU

3, 4. Kodi acinyamata angaphunzile ciani pa citsanzo ca Timoteyo?

3 Ganizilani mmene mungayankhile mafunso awa: N’cifukwa ciani ndimakhulupilila kuti kuli Mulungu? N’cifukwa ciani ndimakhulupilila kuti Baibulo ndi locokeladi kwa Mulungu? Nanga n’cifukwa ciani ndimamvela malamulo a Mulungu m’malo motengela makhalidwe oipa a m’dzikoli? Mafunso amenewa angakuthandizeni kutsatila malangizo a Paulo akuti: “Muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.” (Aroma 12:⁠2) N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?

Timoteyo anakonda coonadi cifukwa cakuti anaganizila zimene anaphunzila ndipo anakhutila nazo

4 Kutsatila citsanzo ca Timoteyo kungakuthandizeni. Iye anali kuwadziŵa bwino Malemba cifukwa cakuti amai ake ndi ambuye ake aakazi anam’phunzitsa Malemba. Komabe, Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pitiliza kutsatila zimene unaphunzila ndi zimene unakhulupilila pambuyo pokhutila nazo.” (2 Timoteyo 3:​14, 15) Pa lembali, liu lakuti ‘kukhutila’ likutanthauza “kukhala wotsimikiza kuti cina cake ndi coonadi.” Cotelo, Timoteyo anafunika kukhala wotsimikiza kuti coonadi cimapezeka m’Malemba. Iye anakonda coonadi osati cifukwa cakuti amai ake ndi ambuye ake anamuphunzitsa coonadi. Koma cifukwa cakuti anaganizila zimene anaphunzila ndipo anakhutila nazo.​—Ŵelengani Aroma 12:⁠1.

5, 6. N’cifukwa ciani mufunika kuphunzila kugwilitsila nchito “luntha la kuganiza” mukali acinyamata?

5 Nanga bwanji za inu? Mwina munayamba n’kale kuphunzila coonadi. Ngati n’conco, pezani nthawi yosinkhasinkha cifukwa cake mumakhulupilila zimene munaphunzila. Kucita zimenezo kudzakuthandizani kulimbitsa cikhulupililo canu ndi kupewa kupanga zosankha zoipa cifukwa cosonkhezeledwa ndi anzanu, kutengela maganizo a dziko, kapena cifukwa cofuna kudzisangalatsa.

6 Ngati mwaphunzila kugwilitsila nchito “luntha la kuganiza” mukali acinyamata, mudzakwanitsa kuyankha mafunso amene anzanu angakufunseni, monga akuti: ‘Umadziŵa bwanji kuti kuli Mulungu? Ngati Mulungu amatikonda, n’cifukwa ciani amalola zinthu zoipa kucitika? Umadziŵa bwanji kuti Mulungu alibe ciyambi?’ Ngati ndinu okonzeka, mafunso amenewa sadzakucititsani kukaikila zikhulupililo zanu, koma adzakulimbikitsani kuphunzila Baibulo mwakhama.

7-9. Fotokozani mmene nkhani zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Ciani?” za pa webusaiti yathu zingakuthandizileni kulimbitsa cikhulupililo.

7 Kucita phunzilo laumwini mwakhama kungakuthandizeni kuyankha mafunso, kuthetsa zikaikilo zimene mungakhale nazo, ndi kulimbitsa cikhulupililo canu. (Machitidwe 17:11) Tili ndi zofalitsa zambili zimene zingakuthandizeni kucita zimenezo. Ambili athandizidwa cifukwa cophunzila bulosha lacingelezi lakuti, The Origin of Life​—Five Questions Worth Asking, ndi buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Komanso, acinyamata ambili apindula ndi nkhani zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Ciani?” zimene zili pa webusaiti yathu ya jw.org. Kuti mupeze nkhanizi, pitani pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA. Nkhani iliyonse pa mbali imeneyi inakonzedwa kuti ikuthandizeni kulimbitsa cikhulupililo canu pa mfundo inayake ya m’Baibulo.

8 Popeza mumaphunzila Baibulo, mayankho ena a mafunso amene ali m’nkhani zimenezi mukuwadziŵa. Koma kodi ndinu okhutila ndi mayankho anu? Nkhanizo zidzakuthandizani kuganizila Malemba osiyanasiyana mosamala ndi kukulimbikitsani kulemba cifukwa cake mumakhulupilila zimenezo. Kucita zimenezo kudzakuthandizani kudziŵa mmene mungafotokozele ena zimene mumakhulupilila. Ngati muli ndi mwai woŵelenga nkhani zakuti “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Ciani?” pa webusaiti yathu, mungazigwilitsile nchito pa phunzilo lanu laumwini kuti mulimbitse cikhulupililo canu.

9 Muyenela kukhutila kuti mwapeza coonadi. Zimenezi zidzakuthandizani kukonzekela ubatizo. Mlongo wina wacitsikana anati: “Ndikalibe kuganiza zobatizidwa, ndinaphunzila Baibulo ndipo ndinakhulupilila kuti ici ndiye cipembedzo coona. Ndipo tsiku ndi tsiku, cikhulupililo canga cinali kulimbilalimbila.”

ZOCITA ZANU

10. N’cifukwa ciani Mkristu wobatizidwa ayenela kukhala ndi makhalidwe oonetsa kuti ali ndi cikhulupililo?

10 Baibulo limati: “Cikhulupililo pacokha, ngati cilibe nchito zake, ndi cakufa.” (Yakobo 2:17) Zocita zanu n’zimene zimaonetsa kuti muli ndi cikhulupililo colimba. Ngati muli ndi cikhulupililo colimba, mudzakhala ndi ‘makhalidwe oyela ndi kucita nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu.’​—Ŵelengani 2 Petulo 3:⁠11.

11. Kodi ‘makhalidwe oyela’ n’ciani?

11 Kodi ‘makhalidwe oyela’ n’ciani? Munthu amene ali ndi khalidwe loyela, amapewa zinthu zoipa. Mwacitsanzo, ganizilani za miyezi 6 yapitayi. Pamene munayesedwa kuti mucite zinthu zoipa, kodi munakwanitsa kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela? (Aheberi 5:14) Kodi mukukumbukila nthawi inayake pamene simunagonje pa ciyeso kapena pamene munakana kutengela zocita za anzanu? Kodi ndinu citsanzo cabwino ku sukulu? Kodi mumakhalabe okhulupilika kwa Yehova, kapena mumacita zinthu zomwe anzanu amacita kuti asakusekeni? (1 Petulo 4:​3, 4) Tonse ndife opanda ungwilo. Nthawi zina, ngakhale anthu amene atumikila Yehova kwa nthawi yaitali amamva manyazi, ndipo zimakhala zovuta kuti aphunzitse ena. Koma munthu amene wadzipeleka kwa Mulungu amanyadila kukhala wa Mboni za Yehova, ndipo amaonetsa zimenezi mwa kukhala ndi khalidwe loyela.

12. Kodi “nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu” zimaphatikizapo ciani? Ndipo inuyo mumaziona bwanji?

12 Kodi “nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu” n’ciani? Nchito zimenezi zimaphatikizapo zimene mumacita pampingo, monga kupita kumisonkhano ndi kulalikila. Komanso zimaphatikizapo zinthu zina zimene mumacita monga kupemphela panokha kwa Yehova ndi kucita phunzilo laumwini. Munthu amene wadzipeleka kwa Yehova saona kuti kucita zinthu zimenezi n’kolemetsa. Iye amamva monga mmene Mfumu Davide anamvelela pamene anakamba kuti: “Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga, ndipo cilamulo canu cili mumtima mwanga.”​—Salimo 40:⁠8.

Mukamapemphela, kodi mumachula mwacindunji zimene mukufuna?

13, 14. N’ciani cingakuthandizeni kucita “nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu”? Nanga acinyamata ena apindula bwanji ndi mbali imeneyi?

13 Pofuna kukuthandizani kupanga zolinga, pa tsamba 308 ndi 309 m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, pali mbali imene mungalembepo mayankho a mafunso amene alipo. Pamenepo, pali mafunso monga akuti: “Mukamapemphela, kodi mumachula mwacindunji zimene mukufuna? Nanga mapemphelo anuwo amasonyeza kuti mumakondadi Yehova?” “Kodi mumacita zinthu zotani paphunzilo lanu laumwini?” “Kodi mumaloŵa mu utumiki ngakhale ngati makolo anu sanaloŵe?” Mbali imeneyo ilinso ndi malo amene mungalembepo zolinga zimene mufuna kukwanilitsa pa nkhani ya pemphelo, phunzilo laumwini, ndi polalikila.

14 Acinyamata ambili amene afuna kubatizidwa aona kuti mbali imeneyi ndi yothandiza kwambili. Mlongo wina wacitsikana, dzina lake Tilda anati: “Ndinalemba zolinga zanga pa masamba amenewo. Ndinayamba kukwanilitsa zolinga zimenezo cimodzi ndi cimodzi, ndipo patapita caka cimodzi ndinakhala woyenelela kubatizidwa.” M’bale wina wacinyamata dzina lake Patrick anacita zofanana ndi zimenezi. Iye anati “Ndinali kudziŵa zolinga zanga, koma kuzilemba kunandithandiza kuti ndiyesetse kuzikwanilitsa.”

Kodi mungapitilize kutumikila Yehova ngakhale makolo anu atasiya kum’tumikila? (Onani ndime 15)

15. N’cifukwa ciani muyenela kudzipeleka mwa kufuna kwanu?

15 Limodzi mwa mafunso amene ali pamasamba amenewo ndi lakuti: “Kodi mungapitilize kutumikila Yehova ngakhale makolo anu ndiponso anzanu atasiya kumutumikila?” Mukadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa, ndiye kuti inuyo panokha mwapanga ubwenzi ndi Mulungu. Conco, muyenela kutumikila Yehova mwa kufuna kwanu osati cabe cifukwa cotengela makolo anu kapena munthu wina. Makhalidwe anu oyela ndi nchito zanu zosonyeza kudzipeleka kwanu kwa Mulungu, ziyenela kuonetsa kuti mumakhulupilila kuti mwapeza coonadi komanso mukufuna kutsatila mfundo za Mulungu. Mukacita zimenezo, mudzakhala woyenela kubatizidwa.

KHALANI WOYAMIKILA

16, 17. (a) N’ciani ciyenela kulimbikitsa munthu kukhala Mkristu? (b) Ndi fanizo liti limene lionetsa kuti tifunika kuyamikila dipo?

16 Tsiku lina, munthu wina amene anali kudziŵa bwino Cilamulo ca Mose, anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:​35-37) Pamenepa, Yesu anasonyeza kuti munthu ayenela kubatizidwa ndi kukhala Mkristu cifukwa cokonda Yehova. Cinthu cimodzi cimene cingakuthandizeni kukonda kwambili Yehova, ndi kuganizila mozama za dipo, limene ndi mphatso ya mtengo wapatali imene Mulungu anapatsa anthu. (Ŵelengani 2 Akorinto 5:​14, 15; 1 Yohane 4:​9, 19.) Mukacita zimenezo, mudzalimbikitsidwa kucita zinthu zoonetsa kuti mumayamikila mphatso yapadela imeneyo.

17 Kuti mumvetsetse cifukwa cake muyenela kuyamikila kwambili dipo, ganizilani izi: Tiyelekeze kuti muli m’madzi ndipo mwayamba kumila, kenako munthu wina wabwela kudzakupulumutsani. Kodi mungangocoka pa malowo ndi kupita kunyumba kukasintha zovala, ndi kuiŵalako za munthu amene wakupulumutsani? Ai ndithu. Nthawi zonse, mudzakhala woyamikila kwa munthu ameneyo cifukwa cakuti anakupulumutsani. Mofanana ndi zimenezi, tiyenela kuyamikila kwambili Yehova ndi Yesu cifukwa ca dipo. Tili ndi moyo cifukwa ca io, ndipo anatipulumutsa ku ucimo ndi imfa. Cifukwa cakuti amatikonda, tili ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo kwamuyaya m’Paladaiso pano pa dziko lapansi.

18, 19. (a) N’cifukwa ciani simuyenela kuopa kudzipeleka kwa Yehova? (b) Kodi kutumikila Yehova kungakupindulitseni bwanji?

18 Kodi mumayamikila zimene Yehova anakucitilani? Ngati mwayankha kuti inde, mungacite bwino kudzipeleka ndi kubatizidwa. Mukadzipeleka kwa Mulungu, ndiye kuti mwalonjeza kuti mudzacita cifunilo cake kwamuyaya. Kodi muyenela kuopa kupanga lonjelo limeneli? Ai. Yehova amakufunilani zabwino, ndipo adzapeleka mphoto kwa amene amacita cifunilo cake. (Aheberi 11:⁠6) Mukadzipeleka kwa Mulungu ndi kubatizidwa, zinthu zidzakuyendelani bwino. M’bale wina wa zaka 24 amene anabatizidwa ali wacicepele, anati: “Ndikanatha kuyembekezela kuti ndikuleko mpaka nditamvetsa zinthu mozama. Koma ndikuona kuti kudzipeleka kwa Yehova ndikali wamng’ono kunandithandiza kuti ndisayambe kufunafuna zinthu za m’dzikoli.”

Satana ndi wodzikonda ndipo sasamala za inu

19 Yehova amakufunilani zabwino. Koma Satana ndi wodzikonda ndipo sasamala za inu. Iye sangakupatseni cinthu ciliconse cabwino mukam’tsatila cifukwa alibe cabwino. Alibe uthenga wabwino, ndiponso alibe ciyembekezo ciliconse. Angakucititseni kuti mudzaonongedwe, cifukwa iye akuyembekezela cionongeko.​—Chivumbulutso 20:⁠10.

20. Kodi wacinyamata angacite ciani kuti akhale wokonzeka kudzipeleka ndi kubatizidwa? (Onani bokosi lakuti “Zimene Zingakuthandizeni Kupita Patsogolo.”)

20 Kudzipeleka kwa Yehova ndi cosankha cabwino kwambili cimene munthu angapange. Kodi mwakonzekela kucita zimenezo? Ngati n’telo, musaope kupanga lonjezo limenelo. Koma ngati muona kuti sindinu okonzeka, gwilitsilani nchito malangizo amene ali m’nkhani ino kuti mupite patsogolo. Paulo anauza abale a ku Filipi kuti apitilize kupita patsogolo. (Afilipi 3:16) Mukamvela malangizo amenewo, mudzayamba kulakalaka kudzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa.