Njilayo ‘Anali Kuidziŵa’
M’BALE Guy Hollis Pierce, amene anali membala wa Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova anamaliza moyo wake wa padziko lapansi pa Ciŵili, March 18, 2014. Iye anali ndi zaka 79 pamene ciyembekezo cake codzaukitsidwa kukhala mmodzi wa abale a Kristu kumwamba cinakwanilitsidwa.—Aheb. 2:10-12; 1 Pet. 3:18.
M’bale Guy Pierce anabadwa pa November 6, 1934 ku Auburn, m’dela la California, m’dziko la United States, ndipo anabatizidwa mu 1955. Iye anakwatilana ndi mkazi wake wokondedwa Penny mu 1977, ndipo anali ndi ana. Kusamalila banja kunamuthandiza kukhala wacikondi kwambili monga tate. Pofika mu 1982, iye ndi Penny anayamba upainiya, ndipo anatumikila monga woyang’anila dela ku United States kwa zaka 11 kuyambila mu 1986.
Mu 1997, M’bale ndi Mlongo Pierce anayamba kutumikila pa Beteli ya ku United States. M’baleyu anali kutumikila m’Dipatimenti ya Utumiki, ndipo mu 1998 anaikidwa kukhala wothandiza m’Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli ya Bungwe Lolamulila. Cilengezo cakuti M’bale Pierce waikidwa kukhala membala wa Bungwe Lolamulila cinapelekedwa pa October 2, 1999, pamsonkhano wa pachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. M’zaka zaposacedwapa, m’baleyu anatumikila m’makomiti osiyanasiyana monga Yoona za Atumiki a pa Beteli, Yoona za Nchito Yolemba Mabuku, Yoona za Nchito Yofalitsa Mabuku, ndi ya Ogwilizanitsa.
Anthu a m’maiko osiyanasiyana ndiponso a zikhalidwe zosiyanasiyana anali kukonda M’bale Pierce cifukwa cakuti anali wansangala ndipo anali kukonda kumwetulila. Komanso anthu anali kumukonda kwambili cifukwa ca cikondi ndi kudzicepetsa kwake. Anali kumukondanso cifukwa cotsatila malamulo ndi mfundo zolungama ndiponso cifukwa cokhulupilila kwambili Yehova. M’bale Guy Pierce anali kukhulupilila kuti malonjezo a Yehova nthawi zonse amakwanilitsidwa mofanana ndi mmene timakhulupilila kuti dzuŵa lidzatuluka maŵa. Motelo iye anali kufunitsitsa kulalikila mfundo ya coonadi imeneyi kwa anthu onse padziko lapansi.
M’bale Pierce anali wakhama kwambili potumikila Yehova cakuti anali kudzuka m’mamaŵa, ndipo nthawi zambili anali kugwila nchito mpaka usiku. M’baleyu anali kuyenda m’maiko osiyanasiyana padziko lonse lapansi n’colinga cokalimbikitsa abale ndi alongo ake akuuzimu. Iye anali kumasuka kuceza ndi aliyense pa Beteli ndiponso anthu ena amene anali kufuna kuceza naye, kupempha uphungu kapena thandizo lina lililonse. Ngakhale pambuyo pa zaka zambili, abale ndi alongo saiwala kuti m’bale Pierce anali kukonda kuceleza, anali waubwenzi, ndipo anali kukonda kulimbikitsa ena pogwilitsila nchito Malemba.
M’bale wathuyu ndiponso bwenzi lathu, anasiya mkazi, ana 6, adzukulu ndi adzukulutudzi. Analinso ndi ana ambilimbili a kuuzimu. M’bale Mark Sanderson, amenenso ali m’Bungwe Lolamulila, ndi amene anakamba nkhani ya malilo a M’bale Pierce, ku Beteli ya ku Brooklyn pa Ciŵelu, pa March 22, 2014. M’nkhaniyo, M’bale Sanderson anakambanso za ciyembekezo ca moyo wakumwamba cimene M’bale Pierce anali naco. Iye anaŵelenga mau a Yesu akuti: “M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambili okhalamo. . . . Ndikapita kukakukonzelani malo, ndidzabwelanso kudzakutengelani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko. Ndipo kumene ndikupitako, inu njila yake mukuidziŵa.”—Yoh. 14:2-4.
Kunena zoona tidzamusoŵa kwambili M’bale Pierce. Koma tikusangalala cifukwa cakuti anali kudziŵa “njila” yopitila ku malo kumene adzakhala kwamuyaya.