NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA May 2015

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzila kuyambila mlungu wa June 29 mpaka wa July 26, 2015.

MBILI YANGA

Kukumbukila Cikondi Canga ca Poyamba Kwandithandiza Kupilila

Ŵelengani mbili ya moyo wa Anthony Morris III, m’bale wa m’Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova.

Khalani Maso! Satana Akufuna Kukumezani

Makhalidwe atatu a Satana amaonetsa kuti iye ndi mdani wathu woopsa kwambili.

Mungapambane Polimbana Ndi Satana

Mungapewe bwanji misampha ya Satana monga kunyada, kukonda cuma ndi ciwelewele?

‘Anaona’ Malonjezo a Mulungu

Amuna ndi akazi okhulupilika akale anapeleka citsanzo cabwino cifukwa anali kuona madalitso amtsogolo.

Muzitsanzila Mulungu Amene Watilonjeza Moyo Wosatha

Kodi n’zotheka kumvetsa mavuto amene ena akukumana nao ngakhale kuti ife sitinakumanepo nao?

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Kodi Gogi wa Magogi wochulidwa m’buku la Ezekieli ndani?

ZA M'NKHOKWE YATHU

Nchito Inali Kuyenda Bwino M’kafiteliya Cifukwa ca Cikondi

Ngati munayamba kupezeka pamisonkhano yacigawo ya Mboni za Yehova ca m’ma 1990 kapena pambuyo pake, mudzacita cidwi kudziŵa za makonzedwe amene analiko kale.