Mungapambane Polimbana Ndi Satana
“Khalani olimba m’cikhulupililo ndipo mulimbane naye [Satana].”—1 PET. 5:9.
1. (a) N’cifukwa ciani kulimbana ndi Satana n’kofunika kwambili masiku ano? (b) Timadziŵa bwanji kuti n’zotheka kupambana polimbana ndi Satana?
SATANA akucita nkhondo ndi odzozedwa ndiponso a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Popeza Mdyelekezi watsala ndi kanthawi kocepa, colinga cake n’cakuti ameze atumiki ambili a Yehova mmene angathele. (Ŵelengani Chivumbulutso 12:9, 12.) Kodi n’zotheka kupambana polimbana ndi Satana? Inde, n’zotheka. Baibulo limati: “Tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthawani.”—Yak. 4:7.
2, 3. (a) Kodi maganizo akuti Satana kulibe amamuthandiza bwanji kukwanilitsa zolinga zake? (b) Mumadziŵa bwanji kuti Satana aliko?
2 Anthu ambili amatsutsa mfundo yakuti Satana aliko. Iwo amanena kuti Satana ndi ziwanda ndi anthu ongopeka amene amapezeka m’mabuku a nthano, m’mafilimu oopsa ndi m’masewela a pa kompyuta. Anthu amenewo amaona kuti ndi kupanda nzelu kukhulupilila kuti kuli mizimu yoipa. Koma kodi muganiza kuti Satana ndi ziwanda zake amakhumudwa ndi zimene anthu amanena zoti iwo ndi ongopeka? Iyai. Ndipo sicikhala covuta kwa iye kucititsa khungu maganizo a anthu otelo. (2 Akor. ) Njila imodzi imene Satana amasoceletsela anthu ambili ndi kuwacititsa kukhulupilila kuti iye kulibe. 4:4
3 Ife atumiki a Yehova sitipusitsidwa mwa njila imeneyi. Timadziŵa kuti Mdyelekezi aliko cifukwa cakuti ndiye anakamba ndi Hava kudzela mwa njoka. (Gen. 3:1-5) Satana ananyoza Yehova ponena za Yobu. (Yobu 1:9-12) Ndipo ndi Satana yemweyo amene anayesa Yesu. (Mat. 4:1-10) Komanso Ufumu wa Mulungu utakhazikitsidwa mu 1914, Satana anapita “kukacita nkhondo” ndi otsalila odzozedwa. (Chiv. 12:17) Nkhondoyo ikali kupitilila cifukwa Satana akufunitsitsa kuononga cikhulupililo ca otsalila odzozedwa ndi a nkhosa zina. Kuti tipambane pankhondoyi, tifunika kulimbana naye ndi kukhala olimba m’cikhulupililo. M’nkhani ino, tikambilana makhalidwe atatu amene tiyenela kupewa kuti tipambane.
PEWANI KUNYADA
4. Kodi Satana waonetsa bwanji kuti ndi wonyada kwambili?
4 Satana ndi wodzikuza ndiponso wonyada kwambili. Umboni wa zimenezi ndi wakuti iye analimba mtima kutsutsa ulamulilo wa Yehova ndi kudzipanga mulungu wolimbana ndi Mlengi. Conco, cinthu cimodzi cimene tiyenela kucita kuti tilimbane ndi Satana ndi kupewa kunyada ndiponso kuyesetsa kukhala odzicepetsa. (Ŵelengani 1 Petulo 5:5.) Kodi kunyada n’kutani? Nanga kumasiyana bwanji ndi kunyadila?
5, 6. (a) Kodi kunyadila n’kulakwa? Fotokozani. (b) Kodi kunyada n’kutani? Nanga ndi zitsanzo ziti za m’Malemba zimene zionetsa kuti kunyada n’koipa?
5 Dikishonale ina inamasulila kunyadila kuti ndi: “Kukhala wokhutila cifukwa ca zimene mwacita, zimene muli nazo, kapena cifukwa ca zimene mnzanu wacita ndiponso zimene ali nazo.” Kucita zimenezo kulibe vuto lililonse. Mtumwi Paulo anauza Atesalonika kuti: “Ifeyo timakunyadilani ku mipingo ya Mulungu cifukwa ca kupilila kwanu ndi cikhulupililo canu pokumana ndi mazunzo ndi masautso onse amene mukulimbana nao.” (2 Ates. 1:4) Conco, kusangalala komanso kunyadila ndi zimene tacita kapena zimene ena acita n’kwabwino. Sitifunikila kucita manyazi cifukwa ca banja lathu, mtundu wathu, kapena dela limene tinakulilako.—Mac. 21:39.
6 Komabe, kunyada kungaononge ubwenzi wathu ndi anthu ena ndiponso ndi Yehova. Kunyada kungaticititse kudana ndi uphungu kapena kuukana mmalo movomela modzicepetsa. (Sal. 141:5) Kunyada kumatanthauza “kudziona wapamwamba kwambili” kapena “kukhala ndi mzimu wodzikuza cifukwa codziona kuti ndife apamwamba kuposa ena.” Yehova amadana ndi kunyada. (Ezek. 33:28; Amosi 6:8) Koma Satana amasangalala kwambili akaona anthu akuonetsa mzimu wonyada cifukwa iye ndi wonyada ndiponso wodzikuza. Satana ayenela kuti anasangalala kwambili pamene Nimurodi, Farao, ndi Abisalomu anacita zinthu modzikuza cifukwa ca kunyada. (Gen. 10:8, 9; Eks. 5:1, 2; 2 Sam. 15:4-6) Kunyada ndi kumene kunacititsanso kuti Kaini acimwe. Iye anapatsidwa uphungu mwacindunji ndi Mulungu, koma sanalabadile cifukwa ca kunyada. Modzikuza ananyalanyaza uphungu umene Yehova anamupatsa ndipo anapha m’bale wake.—Gen. 4:6-8.
7, 8. (a) Kodi kusankhana mitundu n’kutani? Ndipo n’cifukwa ciani kucita zimenezo ndi kunyada? (b) Fotokozani mmene kunyada kungasokonezele mtendele mumpingo.
7 Masiku ano, anthu amaonetsa mzimu wonyada m’njila zambili. Kunyada nthawi zina kumacititsa anthu kusankhana mitundu. Dikishonale ina inanena kuti kusankhana mitundu kumatanthauza “kusankha anthu kapena kudana nao cifukwa cakuti si a mtundu wathu.” Ndipo inanena kuti kumatanthauzanso “kukhulupilila
kuti anthu a mitundu ina ali ndi maluso ndiponso makhalidwe osiyana ndi ena, komanso kuti mitundu ina ndi yapamwamba kuposa ina.” Cifukwa cosankhana mitundu, anthu amacita ciwawa, nkhondo ndiponso amaphana mwacisawawa.8 Mumpingo simuyenela kukhala tsankho. Ngakhale n’conco, mikangano pakati pa Akhristu ikhoza kubuka cifukwa ca kunyada ndipo ingafike poipa kwambili. Ngakhale pakati pa Akhristu ena oyambilila panabuka mikangano. Ndiye cifukwa cake Yakobo anawafunsa kuti: “Kodi nkhondo zimene zikucitika pakati panu zikucokela kuti?” (Yak. 4:1) Kunena zoona, ngati tilekelela cidani ndiponso mzimu wodziona kukhala wapamwamba kukula m’mitima yathu tikhoza kumalankhula ndi kucita zinthu mosaganizila ena, ndipo tingawakhumudwitse. (Miy. 12:18) N’zoonekelatu kuti kunyada kumasokoneza mtendele mumpingo.
9. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kupewa kunyada ndi kusankhana mitundu? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
9 Ngati timakonda kudziona apamwamba kuposa ena, tiyenela kukumbukila kuti “Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.” (Miy. 16:5) Tiyenelanso kudzifufuza ndi kuona mmene timaonela anthu a mtundu wina, a dziko lina, kapena a cikhalidwe cina. Ngati timasankha anthu a mtundu wina kapena a dziko lina, ndiye kuti tikunyalanyaza mfundo yakuti “kucokela mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu.” (Mac. 17:26) Cifukwa ca ici, tonse ndife amodzi popeza tinacokela kwa kholo limodzi loyambilila, Adamu. Conco, ndi kupanda nzelu kuganiza kuti mtundu wina ndi wapamwamba kuposa wina. Maganizo otelo amasangalatsa Satana cifukwa iye amafuna kuti tisamakondane ndi kugwilizana. (Yoh. 13:35) Kuti tipambane polimbana ndi Satana, tifunika kupewelatu kunyada kwa mtundu uliwonse.—Miy. 16:18.
PEWANI KUKONDA CUMA NDI ZINTHU ZA M’DZIKO
10, 11. (a) N’cifukwa ciani n’zosavuta kuyamba kukonda kwambili zinthu za m’dziko? (b) Kodi Dema anaonetsa bwanji kuti anali kukonda zinthu za m’dziko?
10 Satana ndiye “wolamulila wa dzikoli” ndipo lili m’manja mwake. (Yoh. 12:31; 1 Yoh. 5:19) Motelo, zinthu zimene dzikoli limalimbikitsa sizigwilizana ndi mfundo za m’Baibulo. N’zoona kuti si zonse za m’dzikoli zomwe ndi zoipa. Komabe tisaiwale kuti Satana angagwilitsile nchito dzikoli kuti atisonkhezele kucita chimo kapena kuyamba kukonda zinthu za m’dzikoli ndi kusiya kulambila Yehova.—Ŵelengani 1 Yohane 2:15, 16.
11 Akhristu ena oyambilila anakhudzidwa ndi mzimu wokonda zinthu za m’dziko. Mwacitsanzo, Paulo analemba kuti: “Dema wandisiya cifukwa cokonda zinthu za m’nthawi ino.” (2 Tim. 4:10) Baibulo silichula mwacindunji zinthu za m’dziko zimene Dema anakonda zimene zinamucititsa kusiya Paulo. Mwina Dema anayamba kukonda kwambili zinthu zakuthupi kuposa zinthu zakuuzimu. Ngati zinali conco, Dema anataya mwai wamtengo wapatali wa kuuzimu, cifukwa cakuti dziko silikanamupatsa zinthu zabwino kuposa madalitso amene Yehova akanamupatsa cifukwa cokhala mnzake wa Paulo.—Miy. 10:22.
12. Kodi tingasoceletsedwe bwanji ndi “cinyengo camphamvu ca cuma”?
12 Zofanana ndi zimenezi zikhoza kuticitikila masiku ano. Pokhala Akhristu, timafunika kudzisamalila ndi kusamalilanso mabanja athu mwakuthupi. (1 Tim. 5:8) Yehova amafuna kuti tikhale ndi umoyo wabwino, ndipo timadziŵa zimenezi tikaganizila zinthu zabwino zimene iye anapatsa Adamu ndi Hava. (Gen. 2:9) Koma Satana angatisoceletse mwa kugwilitsila nchito “cinyengo camphamvu ca cuma.” (Mat. 13:22) Anthu ambili amaganiza kuti ndalama ndiponso zinthu zina zakuthupi zingawapatse cimwemwe. Koma kuganiza conco n’kudzinamiza cifukwa tikhoza kutaya cinthu ca mtengo wapatali cimene ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Yesu anacenjeza otsatila ake kuti: “Kapolo sangatumikile ambuye aŵili, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Ngati tikhala kapolo wa Cuma, tikhoza kusiya kutumikila Yehova, ndipo zimenezo n’zimene Satana amafuna. Tisalole ndalama kapena katundu kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuti tipambane polimbana ndi Satana, tiyenela kuona zinthu za kuthupi m’njila yoyenela.—Ŵelengani 1 Timoteyo 6:6-10.
PEWANI CIWELEWELE
13. Kodi dzikoli limalimbikitsa bwanji anthu kusalemekeza cikwati?
13 Msampha wina wa Satana ndi ciwelewele. Masiku ano, anthu ambili amaona kuti cikwati ndiponso kukhala wokhulupilika m’cikwati n’kwacikale ndipo n’kosatheka. Mwacitsanzo, mayi wina wochuka wa mafilimu anati: “N’zosatheka kukhala ndi mwamuna kapena mkazi mmodzi. Ndikukaikila ngati kuli munthu wokhulupilika m’banja kapena amene amafuna kutelo.” Ndiponso mwamuna wina wochuka wa mafilimu anati: “Ndikukayikila ngati tinalengedwa kuti tizikhala ndi mkazi kapena mwamuna mmodzi moyo wathu wonse.” Satana amasangalala akaona anthu ochuka akunyoza mphatso ya ukwati yocokela kwa Mulungu. Mdyelekezi safuna kuti anthu azilemekeza ukwati kapena kuti uziyenda bwino. Kuti tipambane polimbana ndi Satana, tifunika kuyesetsa kulemekeza mphatso ya ukwati yocokela kwa Mulungu.
14, 15. Kodi tingapewe bwanji ciwelewele?
14 Kaya tili m’banja kapena ai tifunika kupewelatu ciwelewele ca mtundu uliwonse. Kodi kucita zimenezi n’kopepuka? Ayi ndithu. Mwacitsanzo, ngati ndinu wacinyamata, mwina mumamva anzanu a kusukulu akudzitama kuti amagonana ndi anthu osiyanasiyana kapena kutumizilana zithunzi ndi mauthenga okhudza kugonana. M’madela ena, kucita zimenezi ndi mlandu wofanana ndi kufalitsa zithunzi za malisece za ana. Koma Baibulo limati: “Amene amacita dama amacimwila thupi lake.” (1 Akor. 6:18) Ciwelewele cacititsa kuti matenda opatsilana pogonana afalikile, ndipo matendawa abweletsa mavuto ambili kuphatikizapo imfa. Acinyamata ambili amene sali pa banja amadziimba mlandu cifukwa cosasunga unamwali wao. Mapulogilamu a pa TV ndi mafilimu angaticititse kuganiza kuti kuphwanya malamulo a Mulungu pankhani ya kugonana kulibe vuto. Koma zimenezo si zoona. Maganizo amenewo amacititsa anthu kukoledwa ndi “cinyengo camphamvu ca ucimo”—Aheb. 3:13.
15 Mungacite ciani ngati mumayesedwa kuti mucite ciwelewele? Musamadzidalile. (Aroma 7:22, 23) Pemphelani kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu. (Phil. 4:6, 7, 13) Muzipewa zinthu zimene zingacititse kuti mucite ciwelewele. (Miy. 22:3) Ndipo ngati mwayesedwa kuti mucite ciwelewele muzikana mwamsanga.—Gen. 39:12.
16. Kodi Yesu anayankha bwanji atayesedwa ndi Satana? Ndipo citsanzo cimeneco cikutiphunzitsa ciani?
16 Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tingapewele mayeselo. Iye sanapusitsidwe ndi malonjezo a Satana ndipo sanayambe waganizila ubwino ndi kuipa kwa malonjezowo. M’malomwake iye anayankha mwamsanga kuti: “Malemba Mateyu 4:4-10.) Yesu anali kudziŵa bwino mau a Mulungu. Ndiye cifukwa cake iye atakumana ndi ciyeso anayankha mwamsanga pogwilitsa nchito malemba. Kuti tipambane polimbana ndi Satana sitiyenela kugonja tikayesedwa kuti ticite ciwelewele.—1 Akor. 6:9, 10.
amati.” (ŴelenganiPILILANI KUTI MUPAMBANE
17, 18. (a) Ndi zida zina ziti zimene Satana amagwilitsila nchito? Nanga n’cifukwa ciani zimenezi siziyenela kutidabwitsa? (b) N’ciani cidzacitikila Satana? Ndipo zimenezo zimakulimbikitsani bwanji kupilila?
17 Kunyada, kukonda cuma, ndiponso ciwelewele ndi zida zimene Satana amagwilitsila nchito. Koma palinso zina zambili. Mwacitsanzo, Akhristu ena amatsutsidwa ndi anthu a m’banja lao, ena amavutitsidwa kusukulu, ndipo ena boma limawaletsa kulalikila. Mavuto amenewo sayenela kutidabwitsa. Yesu anacenjeza otsatila ake kuti: “Anthu onse adzadana nanu cifukwa ca dzina langa, koma yekhayo amene adzapilile mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”—Mat. 10:22.
18 Tingalimbane bwanji ndi Satana kuti tipambane? Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ngati inu mudzapilile, mudzapeza moyo.” (Luka 21:19) Cinthu ciliconse cimene munthu angacite sicingationonge kothelatu. Palibe amene angatilande ubwenzi wathu ndi Mulungu pokhapo ngati talola kuti zimenezi ziticitikile. (Aroma 8:38, 39) Atumiki a Yehova akamwalila sizitanthauza kuti Satana wapambana cifukwa Yehova adzaonetsetsa kuti onse aukitsidwa. (Yoh. 5:28, 29) Koma Satana alibe tsogolo labwino. Dongosolo loipali likadzaonongedwa, iye adzaponyedwa m’phompho ndipo adzakhala kumeneko kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:1-3) Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 1,000 ukadzatha, Satana “adzamasulidwa m’ndende yake” kwa kanthawi kocepa kuti ayese kusoceletsa anthu angwilo komaliza. Pambuyo pake, Mdyelekedzi adzaonongedwa kothelatu. (Chiv. 20:7-10) Satana alibe ciyembekezo ciliconse, koma ife tili ndi ciyembekezo ca tsogolo labwino. Conco, khalani olimba m’cikhulupililo ndipo mulimbane naye Satana. Inde, mungapambane polimbana ndi Satana.