NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA June 2015

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzila kuyambila mlungu wa July 27 mpaka August 30, 2015.

Kristu Ndiye Mphamvu ya Mulungu

Zozizwitsa za Yesu sizinapindulitse Aisraeli akale okha, koma zimasonyezanso zimene Yesu adzacitila anthu posacedwapa.

Anali Kukonda Anthu

Kodi zozizwitsa zimene Yesu anacita zimaonetsa kuti iye ndi munthu wotani?

Tingathe Kupewa Ciwelewele

Baibulo limachula njila zitatu zimene zingatithandize kupewa ciwelewele.

“Ngati Kingsley Wakwanitsa, Inenso Ndingakwanitse”

Kingsley, amene anali ku Sri Lanka, anapilila mavuto aakulu kuti akwanitse kukamba nkhani yake imene inatenga mphindi zocepa.

Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 1

N’cifukwa ciani Yesu anayamba pemphelo limeneli ndi mau akuti “Atate Wathu” osati akuti “Atate Wanga”?

Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 2

Pamene tipempha Mulungu kuti atipatse cakudya cathu calelo, ndiye kuti tikupempha zambili osati cabe cakudya cakuthupi.

“Mukufunika Kupilila”

Pali mfundo zinai zocokela kwa Yehova zimene zingatithandize kupilila tikakumana ndi mayeselo kapena mavuto.

Kodi Mukumbukila?

Kodi mwaŵelenga magazini a Nsanja ya Mlonda aposacedwapa? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa.