Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Tiphunzilapo Ciani pa Zimene Jowana Anacita?

Kodi Tiphunzilapo Ciani pa Zimene Jowana Anacita?

ANTHU ambili amadziŵa kuti Yesu anali ndi atumwi 12. Koma sadziŵa kuti pakati pa ophunzila ake panalinso akazi ena amene anali kugwilizana naye kwambili. Jowana anali mmodzi wa akazi amenewo.—Mat. 27:55; Luka 8:3.

Kodi Jowana anathandiza bwanji pa utumiki wa Yesu? Nanga tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cake?

KODI JOWANA ANALI NDANI?

Jowana anali “mkazi wa Kuza, kapitawo wa Herode.” Kuza ayenela kuti anali kuyang’anila cuma ca mfumu Herode Antipa. Jowana anali mmodzi wa akazi ambili amene Yesu anacilitsa. Iye ndi akazi ena anali kuyendela pamodzi ndi Yesu ndiponso atumwi ake.—Luka 8:1-3.

Arabi Achiyuda anali kuphunzitsa kuti akazi safunika kuceza ndi amuna amene si acibale ao, ngakhale kuyenda nao pamodzi. Pa cifukwa cimeneci, amuna Aciyuda sanali kukonda kulankhula ndi akazi. Yesu ndi ophunzila ake sanatsatile miyambo imeneyi, m’malo mwake iye analola Jowana ndi akazi ena okhulupilila kuti aziyendela nao limodzi.

Jowana anali kugwilizanabe ndi Yesu komanso ophunzila ake mosasamala kanthu kuti anali kucitilidwa zacipongwe ndi acibale ake, anzake ndiponso atsogoleli acipembedzo. Onse amene anali kugwilizana ndi Yesu anafunika kusintha zinthu zina paumoyo wao wa tsiku ndi tsiku. Komabe, ponena za ophunzila amenewo, Yesu anati: “Mai anga ndi abale anga ndi awa amene amamvetsela mau a Mulungu ndi kuwacita.” (Luka 8:19-21; 18:28-30) N’zolimbikitsa kuona kuti Yesu amafuna kukhala pafupi ndi anthu amene amadzimana zinthu zina kuti am’tsatile.

ANALI KUTUMIKILA NDI CUMA CAKE

Jowana ndi amai ena ambili, anali kutumikila Yesu ndi atumwi “pogwilitsa nchito cuma cao.” (Luka 8:3) Wolemba mabuku wina anati: “Luka sananene kuti akaziwo ndiwo anali kuphika zakudya, kucapa zovala, kapena kusoka zovala zong’ambika. Mwina akaziwo anali kucita zimenezi . . . , koma si zimene Luka ananena.” Zioneka kuti akazi amenewa anali kugwilitsila nchito ndalama komanso katundu wao kuthandiza Yesu ndi ophunzila ake.

Yesu ndi atumwi ake sanali kugwila nchito kuti apeze ndalama zodzithandizila pa nchito yao yolalikila. Conco, n’kutheka kuti analibe kopeza ndalama zogulila zakudya ndi zinthu zina zofunikila anthu okwana 20 kapena kuposelapo. Ngakhale kuti anthu anali kuwalandila ndi kuwaceleza, Yesu ndi atumwi ake anali kunyamula “bokosi la ndalama.” Izi zionetsa kuti io sanali kungodalila thandizo la anthu. (Yoh. 12:6; 13:28, 29) Jowana ndi akazi ena ayenela kuti anali kupeleka zopeleka kuti ziziwathandiza.

Anthu ena otsutsa amanena kuti akazi aciyuda sanali kukhala ndi ndalama kapena zinthu zina zimene zingadziwabweletsela ndalama. Komabe, zioneka kuti akazi aciyuda anali kukhala ndi ndalama m’njila zotsatilazi: (1) akalandila colowa ca atate ao amene analibe ana aamuna, (2) akapatsidwa cinthu capamwamba cililiconse, (3) akapatsidwa ndalama ngati cikwati catha, (4) kucokela ku katundu umene amuna ao amene anamwalila anasiya, kapena (5) kucokela ku ndalama zimene io eni anali kupeza.

Otsatila a Yesu naonso anali kupeleka zimene angakwanitse. Zioneka kuti pakati pa otsatila a Yesu panalinso akazi olemela. Popeza kuti Jowana anali mkazi wa woyang’anila cuma ca Herode, anthu amanena kuti iye anali wolemela. Mwina iye ndiye anapeleka mkanjo wodula wopanda msoko umene Yesu anali kuvala. Wolemba wina ananena kuti: “Akazi a asodzi sakanatha kupeleka cinthu codula ngati cimeneco.”—Yoh. 19:23, 24.

Malemba sachula mwacindunji kuti Jowana anali kupeleka ndalama. Iye anacita zimene anakwanitsa ndipo zimenezi zikutiphunzitsa cinacake. Kupeleka zopeleka zocilikiza nchito ya Ufumu ndi cosankha cathu. Koma Mulungu amasangalala ngati timacita zimene tingathe mosangalala.—Mat. 6:33; Maliko 14:8; 2 Akor. 9:7.

PA IMFA YA YESU NDIPONSO PAMBUYO PAKE

Pamene Yesu anali kupacikidwa, panali Jowana ndi akazi ena “amene anali kuyenda naye limodzi ndi kumutumikila pamene anali ku Galileya. Panalinso amai ena ambili amene anabwela naye limodzi kucokela ku Yerusalemu.” (Maliko 15:41) Pamene thupi la Yesu linacotsedwa pa mtengo ndi kumapelekedwa kumanda, “amai amene anayenda limodzi ndi Yesu kucokela ku Galileya, anamutsatila kukaona manda acikumbutsowo ndi mmene mtembo wakewo anauikila. Atatelo anabwelela kukakonza zonunkhilitsa ndi mafuta onunkhila.” Pambuyo pa Sabata azimai anabwelela kumanda ndipo anapeza angelo amene anawauza za kuukitsidwa kwa Yesu. Malinga ndi kunena kwa Luka, azimai amenewa anali “Mariya Mmagadala, Jowana ndi Mariya mai wa Yakobo.”—Luka 23:55–24:10.

Jowana ndi akazi ena okhulupilila anacitila Yesu zimene anakwanitsa

N’kutheka kuti Jowana analinso pakati pa ophunzila a Yesu amene anasonkhana ku Yerusalemu pa Pentecosite mu 33 C.E. Anthu enanso amene ayenela kuti anali pakati pao anali amai ake a Yesu ndi abale ake. (Mac. 1:12-14) Popeza kuti mwamuna wa Jowana anali kapitawo wa Herode, zioneka kuti iye ndi amene anali kuuza Luka zinthu zacinsinsi zokhudza Herode Antipa. Cina, Luka ndiye yekha wolemba uthenga wabwino amene anamuchula mwacindunji kuti, Jowana.—Luka 8:3; 9:7-9; 23:8-12; 24:10.

Nkhani ya Jowana imatiphunzitsa zinthu zambili zofunika. Iye anatumikila Yesu mmene angathele. Ndipo ayenela kuti anasangalala kwambili kuona kuti zopeleka zake zikucilikiza Yesu, ndi ophunzila ake 12 komanso ena amene anali kupita kukalalikila limodzi ndi Yesu. Jowana anatumikila Yesu ndipo anali wokhulupilika kwa iye ngakhale pamavuto. Akazi Acikristu ayenela kutsatila khalidwe lake labwino limeneli.