Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Nkhani ya Munda wa Edeni Imakukhudzani Bwanji?

Kodi Nkhani ya Munda wa Edeni Imakukhudzani Bwanji?

Kodi Nkhani ya Munda wa Edeni Imakukhudzani Bwanji?

IMODZI mwa mfundo zodabwitsa zimene akatswili ena amanena zokhudza munda wa Edeni ni yakuti, nkhani zina za m’Baibo sizisonyeza kuti kunalidi munda wa Edeni. Mwacitsanzo, Pulofesa wina wa Maphunzilo Azacipembedzo dzina lake Paul Morris analemba kuti: “Kupatula m’buku la Genesis, palibe paliponse m’Baibo pamene amanena mwacindunji za munda wa Edeni.” Anthu ena omwe amati ni odziŵa zinthu angagwilizane na maganizo amenewa koma zimenezi ni zosagwilizana na mmene zinthu zililidi.

M’Baibo muli nkhani zambili zosonyeza kuti kunalidi munda wa Edeni ndiponso kunali Adamu, Hava na njoka. a Koma zimene akatswili ocepa amaphunzilo amanena potsutsa nkhani yokhudza munda wa Edeni ni nkhani yaikulu. Atsogoleli acipembedzo ndiponso anthu otsutsa Baibo akamatsutsa nkhani ya m’buku la Genesis yonena za munda wa Edeni, ndiye kuti kwenikweni akutsutsa Baibo lonse. N’cifukwa ciani tikutelo?

Kumvetsa bwino zimene zinacitika m’munda wa Edeni n’kofunika kwambili kuti timvetsenso bwino nkhani zina za m’Baibo. Mwacitsanzo, Mawu a Mulungu analembedwa kuti atithandize kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambili onena za zimene zimacitikila anthu. Nthawi zambili mayankho amene Baibo imapeleka pa mafunso amenewa, amakhala okhudzana na zimene zinacitika m’munda wa Edeni. Taonani zitsanzo izi.

Kodi n’cifukwa ciani anthufe timakalamba ndiponso kumwalila? Adamu na Hava akanamvela Yehova akanakhala na moyo kwamuyaya, ndipo imfa ikanabwela pokhapokha ngati sanamvele. Conco kuyambila pa tsiku limene iwo anapanduka, anakhala na moyo woti nthawi ina iliyonse adzafa. (Genesis 2:16, 17; 3:19) Iwo sanalinso angwilo ngati poyamba ndipo anapatsila ana awo kupanda ungwiloko. N’cifukwa cake Baibo imanena kuti: ‘Ucimo unalowa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.’—Aroma 5:12.

N’cifukwa ciani Mulungu amalola kuti zinthu zoipa zizicitika? M’munda wa Edeni, Satana ananena kuti Mulungu ni wabodza ndipo amabisila zolengedwa zake zinthu zabwino. (Genesis 3:3-5) Conco iye anatsutsa ulamulilo wa Yehova. Adamu na Hava anasankha kumvela Satana, conco nawonso anakana ulamulilo wa Yehova. Mwakucita zimenezi anasonyeza kuti munthu atha kusankha yekha zabwino ni zoipa popanda kutsogoleledwa na Mulungu. Mwa cilungamo cake na nzelu zake zangwilo, Yehova anadziŵa kuti pali njila imodzi yokha imene angathetsele nkhaniyi moyenela. Njila imeneyo ni kulola kuti papite nthawi anthu akudzilamulila okha ngati mmene iwo anafunila. Zotsatila zake n’zakuti padziko lapansili pakhala pakucitika zoipa zambili ndipo zina mwa zimenezi akucititsa ni Satana. Zimenezi zacititsa kuti anthu azindikile mfundo yoona ndiponso yofunika yakuti: Anthu sangathe kudzilamulila okha popanda Mulungu.—Yeremiya 10:23.

Kodi colinga ca Mulungu polenga dzikoli ni ciani? a ngati munda wa Edeni. Iye analamula Adamu na Hava kuti abeleke ana ni kudzaza dziko lapansi ndipo ‘aliyang’anile’ n’colinga coti dziko lonse lapansi likhale lokongola mofanana na munda wa Edeni. (Genesis 1:28) Conco colinga ca Mulungu polenga dzikoli cinali coti likhale paradaiso, ndipo ana a Adamu na Hava angwilo azikhala mmenemo mogwilizana. Mbali yaikulu ya Baibo imafotokoza mmene Mulungu adzakwanilitsila colinga cake coyambilila cimeneci.

Kodi n’cifukwa ciani Yesu Khristu anabwela padziko lapansi? Kupanduka kwa Adamu na Hava m’munda wa Edeni kunacititsa kuti iwo afe komanso kuti ana awo azifa. Komabe cifukwa ca cikondi, Mulungu anapeleka ciyembekezo coti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Iye anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzapeleke cimene Baibo imati, dipo. (Mateyu 20:28) Kodi zimenezi zikutanthauza ciani? Yesu anali “Adamu womalizila,” ndipo anacita zimene Adamu analephela kucita. Yesu anakhalabe munthu wangwilo cifukwa anapitilizabe kumvela Yehova. Kenako mofunitsitsa anapeleka moyo wake monga nsembe kapena kuti dipo ndipo zimenezi zinacititsa kuti anthu onse okhulupilika azikhululukidwa macimo ndiponso kuti m’tsogolo adzakhale na moyo wofanana na umene Adamu na Hava anali nawo mu Edeni asanacimwe. (1 Akorinto 15:22, 45; Yohane 3:16) Mwa kucita zimenezi, Yesu anatitsimikizila kuti colinga ca Yehova cokonzanso dziko lapansi kuti likhale paradaiso, ngati mmene zinalili mu Edeni, cidzacitikadi. b

Colinga ca Mulungu cimeneci cidzacitikadi ndipo sikuti ni zinthu zongoyelekezela cabe. Munda wa Edeni anali malo enieni padzikoli ndipo m’mundamo munali nyama ndiponso anthu. Mofanana na zimenezi, zimene Mulungu walonjeza ni zenizeni ndipo posacedwapa zidzakwanilitsidwa. Kodi inuyo mudzakhalapo pa nthawi imeneyi? Kuti zimenezi zitheke, zikudalila inuyo. Mulungu akufuna kuti aliyense amene angasinthe, ngakhale amene anali wocimwa kwambili, adzakhalepo pa nthawi imeneyo.—1 Timoteyo 2:3, 4.

Yesu atatsala pang’ono kufa, analankhula na munthu amene anali wocimwa kwambili. Munthu ameneyu anali cigawenga ndipo anali kudziŵa kuti anali kuyeneladi kuphedwa. Koma anakhulupilila kuti Yesu ni amene angamutonthoze ndiponso kum’patsa ciyembekezo. Kodi pamenepa Yesu anatani? Anamuuza kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Yesu akufuna kudzaonanso munthu ameneyu ataukitsidwa ndiponso kupatsidwa mwayi wokhala na moyo wosatha m’paradaiso wofanana na munda wa Edeni, ngakhale kuti munthuyu poyamba anali cigawenga. Ndiye kodi si zoona kuti Yesu amafunanso kuti inuyo mudzakhale m’paradaiso? N’zosakayikitsa kuti amafuna zimenezi ndipo Atate ake amafunanso zimenezi. Ngati mukufuna kuti mudzakhale m’paradaiso ameneyu, yesetsani kuphunzila za Mulungu amene analenga munda wa Edeni.

[Mau apansi]

a Mwacitsanzo onani malemba awa: Genesis 13:10; Deuteronomo 32:8; 2 Samueli 7:14; 1 Mbiri 1:1; Yesaya 51:3; Ezekieli 28:13; 31:8, 9; Luka 3:38; Aroma 5:12-14; 1 Akorinto 15:22, 45; 2 Akorinto 11:3; 1 Timoteyo 2:13, 14; Yuda 14; Chivumbulutso 12:9.

b Kuti mudziŵe zambili zokhudza nsembe ya dipo ya Khristu, ŵelengani mutu 5 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni lofalitsidwa na Mboni za Yehova.

[Bokosi]

ULOSI UMENE UMASONYEZA KUTI NKHANI ZONSE ZA M’BAIBO NI ZOGWILIZANA

“Ndidzaika cidani pakati pa iwe [njoka] ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza cidendene.”—Genesis 3:15.

Umenewu ni ulosi woyamba m’Baibo ndipo Mulungu ni amene analosela zimenezi m’munda wa Edeni. Kodi mkazi, mbewu ya mkazi, njoka ndiponso mbewu ya njoka zimene zachulidwa mu ulosi umenewu zikuimila ndani? Nanga “cidani” cimene anacinenaco ni cotani?

NJOKA

Satana Mdyerekezi.—Chivumbulutso 12:9.

MKAZI

Gulu la Yehova la zolengedwa zakumwamba. (Agalatiya 4:26, 27) Yesaya analosela kuti “mkazi” ameneyu adzabeleka ana amene m’tsogolo adzakhale mtundu waukulu wauzimu.—Yesaya 54:1; 66:8.

MBEWU YA NJOKA

Anthu amene asankha kucita cifunilo ca Satana.—Yohane 8:44.

MBEWU YA MKAZI

Yesu Khristu ndiye mbewu yoyambilila ya mkazi ndipo anacokela m’mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. Koma enanso amene ali m’gulu la “mbewu” imeneyi ni abale auzimu a Khristu omwe adzalamulile naye kumwamba. Akhristu odzozedwa amenewa ni amene amapanga mtundu wauzimu wochedwa “Isiraeli wa Mulungu.”—Agalatiya 3:16, 29; 6:16; Genesis 22:18.

KUVULAZA CIDENDENE

Ululu umene Mesiya anamva kwa kanthawi. Satana anakwanitsa kupha Yesu pamene Yesuyo anali padziko lapansi. Koma Yesu anaukitsidwa.

KUPHWANYA MUTU

Kupha Satana. Yesu adzawononga Satana ndipo sadzakhalakonso. Koma ngakhale asanacite zimenezi, Yesu adzathetsa zoipa zonse zimene Satana anayambitsa mu Edeni.—1 Yohane 3:8; Chivumbulutso 20:10.

[Cithunzi]

Adamu na Hava anavutika kwambili cifukwa cakuti anacimwa