Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ganizilani Za Mtundu Wa Munthu Amene Muyenela Kukhala

Ganizilani Za Mtundu Wa Munthu Amene Muyenela Kukhala

Ganizilani Za Mtundu Wa Munthu Amene Muyenela Kukhala

“Ganizilani za mtundu wa munthu amene muyenela kukhala. Muyenela kukhala anthu akhalidwe loyela ndipo muzicita nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu.”—2 PET. 3:11.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi muyenela kukhala anthu otani kuti mukhale ovomelezeka pamaso pa Mulungu?

Kodi Satana amasoceletsa motani anthu?

Kodi muyenela kucita ciani kuti muteteze ubwenzi wanu ndi Yehova?

1, 2. Kuti tikhale ovomelezedwa ndi Mulungu, kodi tiyenela kukhala anthu a mtundu wotani?

 ANTHU ambili amafuna kudziŵa mmene anthu ena amawaonela. Koma monga Akristu, timadela nkhawa kwambili ndi mmene Yehova amationela. Timatelo cifukwa cakuti iye ndi wamkulu mu cilengedwe conse, ndipo ndiye “kasupe wa moyo.”—Sal. 36:9.

2 Pogogomezela za mtundu wa ‘munthu amene tiyenela kukhala’ pamaso pa Yehova, mtumwi Petulo akutilimbikitsa kukhala anthu ‘akhalidwe loyela ndi kucita nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu.’ (Ŵelengani 2 Petulo 3:11.) Kuti tikhale anthu ovomelezeka pamaso pa Mulungu, ‘khalidwe’ lathu liyenela kukhala loyela, mwa zocita zathu, mwa maganizo, ndi mwa kuuzimu. Kuphatikiza pamenepo, tiyenela kucita ‘nchito zosonyeza kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu’ mosonkhezeledwa ndi cikondi cathu ndi ulemu wathu pa iye. Kuti tikhale pa unansi wabwino ndi Mulungu, tiyenelanso kusamala umunthu wathu wamkati. Popeza kuti Yehova ‘amasanthula mitima,’ iye amadziwa ngati khalidwe lathu ndi loyela ndiponso ngati ndife odzipeleka kwa iye yekha kapena ai.—1 Mbiri 29:17.

3. Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso otani okhudza unansi wathu ndi Mulungu?

3 Satana Mdyelekezi samafuna kuti tikhale anthu ovomelezedwa ndi Mulungu. Ndipo amacita zilizonse zimene angathe kuti atipangitse kuononga unansi wathu ndi Yehova. Kaŵili-kaŵili, Satana amagwilitsila nchito mabodza ndi cinyengo kuti atinyengelele kusiya kutumikila Mulungu. (Yoh. 8:44; 2 Akor. 11:13-15) Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Satana amasoceletsa motani anthu? Kodi ndiyenela kucita ciani kuti nditeteze unansi wanga ndi Yehova?’

KODI SATANA AMASOCELETSA MOTANI ANTHU?

4. Kodi Satana amafuna kuipitsa ciani kuti aononge unansi wathu ndi Mulungu? Nanga n’cifukwa ciani amatelo?

4 Wophunzila Yakobo analemba kuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cake. Ndiye cilakolako cikatenga pakati, cimabala chimo. Nalonso chimo likakwanilitsidwa, limabweletsa imfa.” (Yak. 1:14, 15) Kuti aononge unansi wathu ndi Mulungu, Satana amafuna kuipitsa mtima wathu umene ndi gwelo la zikhumbo zathu.

5, 6. (a) Kodi Satana amagwilitsila nchito ciani kuti atikope? (b) Kodi Satana amagwilitsila nchito zinthu zokopa zotani kuti aononge maganizo athu? Kodi wakhala akucita zimenezi kwa nthawi yaitali bwanji?

5 Kodi Satana amagwilitsila nchito ciani kuti aononge mtima wathu? Baibo imati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Zida zimene Satana amagwilitsila nchito zimaphatikizapo “zinthu za m’dziko.” (Ŵelengani 1 Yohane 2:15, 16.) Kwa zaka zambili, Mdyelekezi mwamacenjela wakonza dziko m’njila yakuti azisoceletsa nalo anthu. Popeza kuti tikukhala m’dziko limeneli, tiyenela kusamala ndi njila zake zamacenjela.—Yoh. 17:15.

6 Satana amayesa kuika maganizo oipa m’mitima yathu. Mtumwi Yohane anachula zinthu zokopa zitatu zimene Satana amagwilitsila nchito: (1) “cilako-lako ca thupi,”(2) “cilako-lako ca maso,” ndi (3) “kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” Satana anagwilitsila nchito zinthu zimenezi pamene anali kuyesa Yesu mu cipululu. Popeza kuti Satana wakhala akugwilitsila nchito misampha imeneyi kwa zaka zambili, iye masiku ano amaigwilitsila nchito mwaluso kwambili ndipo amasintha njila zake zimenezo mogwilizana ndi zimene aliyense amakonda. Tisanakambilane zimene tingacite kuti tidziteteze ku misampha ya Mdyelekezi imeneyi, tiyeni coyamba tikambilane mmene iye anagwilitsilila nchito misampha imeneyi kukopa Hava. Tikambilananso mmene analephelela kukopa Mwana wa Mulungu ndi misampha imodzi-modziyo.

“CILAKO-LAKO CA THUPI”

7. Kodi Satana anagwilitsila nchito bwanji “cilako-lako ca thupi” kuyesa Hava?

7 Anthu amafunikila kudya kuti akhale ndi moyo. Mlengi anakonza dziko lapansi kuti lizikwanitsa kupeleka zakudya zoculuka. Satana angagwilitsile nchito cikhumbo cathu cacibadwa cofuna kudya kuti atilepheletse kucita cifunilo ca Mulungu. Taonani mmene iye anacitila zimenezi kwa Hava. (Ŵelengani Genesis 3:1-6.) Satana anauza Hava kuti akhoza kudya zipatso za “mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa” ndipo sangafe. Anamuuzanso kuti tsiku limene adzadya cipatso ca mtengo umenewo, iye adzafanana ndi Mulungu. (Gen. 2:9) Mwa kutelo, Mdyelekezi anasonyeza kuti Hava sanafunikile kumvela Mulungu kuti apitilize kukhala ndi moyo. Limenelo linali bodza lamkunkhuniza. Pamene Hava anamva zimenezi, anafunikila kupanga cosankha: Kukana maganizo a Satana kapena kupitiliza kuganizila zimene Satanayo anamuuza. Kuganizila zimene Satana anamuuza kukanapangitsa kuti cikhumbo cake ca cipatso cimeneco cikule. Ngakhale kuti Hava anali ndi mwai wakudya zipatso za mitengo ina yonse ya m’mundamo, iye anasankha kuganizila pa zimene Satana anamuuza ponena za mtengo wa pakati pa munda ndipo “anathyola cipatso ca mtengowo n’kudya.” Conco, Satana anapangitsa Hava kuyamba kulaka-laka cinthu cimene cinali coletsedwa ndi Mlengi.

8. Kodi Satana anagwilitsila nchito bwanji “cilako-lako ca thupi” kuti akope Yesu? N’cifukwa ciani njila imeneyi inalepheleka?

8 Satana anagwilitsila nchito njila yacinyengo imodzi-modziyo pamene anayesa Yesu m’cipululu. Pambuyo pakuti Yesu wasala kudya kwa masiku 40 usana ndi usiku, Satana anapezelapo mwai womuyesa cifukwa cakuti Yesu anali ndi njala. Satana anauza Yesu kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.” (Luka 4:1-3) Yesu anafunika kupanga cosankha. Iye anafunika kusankha kugwilitsila nchito mphamvu zake zocita zozizwitsa kuti akhutilitse cikhumbo cake cofuna kudya kapena ai. Yesu anadziŵa kuti sanali kufunikila kugwilitsila nchito mphamvu zake mwadyela. Ngakhale kuti anali ndi njala, kusunga unansi wake ndi Yehova kunali kofunika kwambili kuposa kukhutilitsa cikhumbo cake cofuna kudya. Yesu anayankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi cakudya cokha koma ndi mau onse otuluka pakamwa pa Yehova.’”—Matt. 4:4; Luke 4:4.

“CILAKO-LAKO CA MASO”

9. Kodi mau akuti “cilakolako ca maso” amatanthauzanji? Kodi Satana anagwilitsila nchito bwanji njila imeneyi kuti asoceletse Hava?

9 Yohane anachulanso “cilako-lako ca maso” kukhala njila ina yacinyengo. Mau amenewa amasonyeza kuti munthu angayambe kukhumba cinthu cinacake akangociona. Satana anakopa Hava pogwilitsila nchito njila imeneyi pamene anamuuza kuti: “Maso anu adzatseguka ndithu.” Pamene Hava anayamba kuyang’anitsitsa cipatso coletsedwa, ndi pamene cinayamba kuoneka kukhala cokopa. Hava anaona kuti zipatso za mtengo umenewo zinali “zokhumbilika.”

10. Kodi Satana anagwilitsila nchito motani “cilako-lako ca maso” kuyesa Yesu? Nanga Yesu anayankha bwanji?

10 Nanga bwanji ponena za Yesu? Satana “anamuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kocepa. Ndiyeno Mdyelekezi anamuuza kuti: ‘Ndikupatsani ulamulilo pa maufumu onsewa ndi ulemelelo wao wonse.’” (Luka 4:5, 6) Sizinali zotheka kuti Yesu aone maufumu onse panthawi imodzi ndi maso eni-eni. Koma Satana anaganiza kuti akaonetsa Yesu maufumu amenewa mwa masomphenya, angathe kumukopa mosavuta. Mopanda manyazi, Satana ananena kuti: “Ngati inuyo mungandiwelamileko kamodzi kokha, ulamulilo wonsewu udzakhala wanu.” (Luka 4:7) Yesu anakanilatu kucita zimene Satana anali kufuna. Nthawi yomweyo Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’”—Luka 4:8.

“KUDZIONETSELA NDI ZIMENE MUNTHU ALI NAZO PA MOYO WAKE”

11. Kodi Hava anasoceletsedwa bwanji ndi Satana?

11 Pofotokoza zinthu za m’dziko, Yohane ananena za “kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” Panthawi imene Adamu ndi Hava anali anthu okha padziko, zinali zosatheka kuti io ‘adzionetsele ndi zimene anali nazo pa moyo wao’ kwa anthu ena. Koma io anasonyeza kuti anali onyada. Pamene anali kuyesa Hava, Satana anaonetsa kuti Mulungu anali kumana Hava cinacake cabwino. Mdyelekezi anauza Hava kuti tsiku limene adzadya “zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa,” iye ‘adzafanana ndi Mulungu. Adzadziŵa zabwino ndi zoipa.’ (Gen. 2:17; 3:5) Mwa kutelo, Satana anaonetsa kuti Hava akhoza kukhala ndi ufulu wodziimila payekha m’malo molamulilidwa ndi Yehova. Mwacionekele, kunyada ndi kumene kunapangitsa Hava kukhulupilila bodza limenelo. Anadya cipatso coletsedwa cifukwa cokhulupilila kuti sadzafa. Kumeneku kunali kupusa!

12. Kodi ndi njila ina iti imene Satana anagwilitsila nchito kuyesa Yesu? Kodi Yesu anayankha bwanji?

12 Mosiyana ndi Hava, Yesu anaonetsa kuti ndi wodzicepetsa kwambili. Satana anamuyesa m’njila ina, koma Yesu sanafune ngakhale pang’ono kucita zinthu zoyesa Mulungu. Kufuna kuyesa Mulungu kukanakhala kunyada. M’malo mwake, Yesu anayankha mwacindunji ndi momveka bwino kuti: “Pajatu Malemba amati, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’”—Ŵelengani Luka 4:9-12.

MMENE TINGATETEZELE UNANSI WATHU NDI YEHOVA

13, 14. Fotokozani mmene Satana amagwilitsilila nchito njila zina zacinyengo masiku ano.

13 Njila zacinyengo zimene Satana amagwilitsila nchito masiku ano, ndi zofanana ndi zimene anagwilitsila nchito kwa Hava ndi Yesu. Mdyelekezi amagwilitsila nchito “cilako-lako ca thupi” kuti alimbikitse makhalidwe a ciwelewele ndiponso kudya ndi kumwa kwambili. Iye amagwilitsila nchito “cilako-lako ca maso” kuti akope anthu amene ndi osasamala kuti azionelela zinthu zamalisece pa Intaneti. Satana amagwilitsilanso nchito msampha wodzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake’ kuti apangitse munthu kukhala wonyada, kufuna zinthu zambili za kuthupi, udindo, ndi kuchuka.

14 “Zinthu za m’dziko” zili ngati nyambo zimene msodzi amagwilitsila nchito. Nyambo zimakhala zokopa koma kutsogolo kwake kumakhala mbedza. Satana amagwilitsila nchito zinthu zimene anthu angaone kuti zilibe vuto kweni-kweni kuwapangitsa kuphwanya malamulo a Mulungu. Colinga cake ndi kufuna kutipangitsa kukhala ndi cikhumbo coipa ndi kuipitsa mitima yathu. Misampha ya Satana imeneyi ingatipangitse kuona kuti kupeza zofunika pa umoyo wathu ndi kukhala ndi umoyo wabwino n’zofunika kwambili kuposa kucita cifunilo ca Mulungu. Kodi tidzagonjetsedwa ndi njila zacinyengo zimenezi?

15. Kodi tingagonjetse motani ziyeso za Satana monga mmene Yesu anacitila?

15 Ngakhale kuti Hava anagonja ndi ziyeso za Satana, Yesu anagonjetsa ziyeso zimenezo. Nthawi ina iliyonse pamene iye anali kuyesedwa, anapeleka yankho la m’Malemba mwa kunena kuti: “Malemba amati.” Ngati timakonda kuphunzila Baibo mwakhama, tidzazolowela kwambili Malemba cakuti tikakumana ndi ciyeso, tidzatha kukumbukila mavesi amene angatithandize panthawi imeneyo. (Sal. 1:1, 2) Kukumbukila zitsanzo za m’Malemba za anthu amene anali okhulupilika kwa Mulungu, kungatithandize kutsatila zitsanzo zao. (Aroma 15:4) Kuopa Yehova m’njila yoyenelela, kukonda zimene iye amakonda ndi kuda zinthu zimene iye amadana nazo, kudzatiteteza.—Sal. 97:10.

16, 17. Kodi ‘luntha lathu la kuganiza’ lingakhudze bwanji zinthu zimene timacita?

16 Mtumwi Paulo akutilimbikitsa kugwilitsila nchito ‘luntha lathu la kuganiza’ kuti tikhale anthu oumbidwa ndi maganizo a Mulungu osati a dzikoli. (Aroma 12:1, 2) Paulo anagogomezela mfundo yakuti tiyenela kusamala kwambili ndi zinthu zimene timaganiza. Iye anati: “Tikugubuduza maganizo komanso cochinga ciliconse cotsutsana ndi kudziŵa Mulungu, ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvela Kristu.” (2 Akor. 10:5) Maganizo athu amakhudza kwambili zimene timacita. Conco, tiyenela ‘kupitiliza kuganizila’ zinthu zimene n’zolimbikitsa.—Afil. 4:8.

17 Ngati tifuna kukhala anthu oyela tiyenela kupewa maganizo oipa ndi zikhumbo zoipa. Tiyenela kukonda Yehova ndi ‘mtima woyela.’ (1 Tim. 1:5) Koma mtima ndi wonyenga, ndipo mosadziŵa “zinthu za m’dziko” zingaononge makhalidwe athu. (Yer. 17:9) Ndiye cifukwa cake tiyenela ‘kudziyesa kuti tione ngati tikali olimba m’cikhulupililo, ndi kupitiliza kudziyesa kuti tidziŵe kuti ndife anthu otani’ mwa kugwilitsila nchito zimene timaphunzila m’Baibo.—2 Akor. 13:5.

18, 19. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala ndi colinga cokhala mtundu wa munthu amene Yehova amafuna?

18 Cinthu cina cimene cingatithandize kukana “zinthu za m’dziko” ndi kukumbukila mau ouzilidwa a Yohane akuti: “Dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake, koma wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yoh. 2:17) Dongosolo la Satana lingaoneke monga kuti silidzatha. Koma lidzatha ndithu. Zinthu zilizonse zimene dziko la Satana lingapeleke n’zosakhalitsa. Kukumbukila mfundo imeneyi kungatithandize kupewa misampha ya Mdyelekezi.

19 Mtumwi Petulo akutilimbikitsa kuti tiyenela kukhala anthu amene Mulungu amafuna “poyembekezela ndi kukumbukila nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova, pamene kumwamba kudzapsa ndi moto n’kusungunuka, ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambili n’kusungunuka.” (2 Pet. 3:12) Nthawi imeneyo ifika posacedwapa, ndipo Yehova adzaononga mbali zonse za dziko la Satana. Koma pakali pano, Satana adzapitilizabe kugwilitsila nchito “zinthu za m’dziko” kuti atiyese monga mmene anacitila ndi Hava ndiponso Yesu. Sitiyenela kukhala monga Hava ndi kumangofuna kukhutilitsa zikhumbo zathu. Kucita zimenezo kungatanthauze kuti timaona Satana kukhala mulungu wathu. Tiyenela kukhala monga Yesu mwa kukana zokopa zonse za Satana mosasamala kanthu kuti zingaoneke zokopa motani. Tiyeni tonse tikhale ndi colinga cokhala mtundu wa munthu amene Yehova amafuna.

[Mafunso Ophunzilila]

[Cithunzi papeji 24]

“Cilako-lako ca thupi” ndi cimene cinapangitsa Hava kucimwa (Onani ndime 7)

[Cithunzi papeji 25]

Yesu sanalole cinthu cina ciliconse kumuceutsa pa utumiki wake (Onani ndime 8)

[Zithunzi papeji 26]

Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene muyenela kukumbukila pa zocitika izi? (Onani ndime 13 ndi 14)