Kodi Mboni za Yehova Ndi Anthu Otani?
Ndife gulu lapadziko lonse ndipo sitigwilizana ndi magulu aliwonse a zipembedzo. Ngakhale kuti likulu lathu lili ku United States, Mboni za Yehova zambili zimakhala m’maiko ena. Mboni zoposa 8 miliyoni m’maiko oposa 230 zimaphunzitsa anthu Baibulo. Timacita zimenezi pokwanilitsa mau a Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.”
Mosasamala kanthu za kumene timakhala, timamvela malamulo ndipo sitiloŵelela m’ndale za dziko. Timacita zimenezi cifukwa timamvela mau a Yesu akuti Akristu ‘sayenela kukhala mbali ya dziko.’ Conco sitiloŵelela m’ndale za dziko ndi m’zocitika zina zocilikiza nkhondo. (Yohane 15:19; 17:16) Pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, Mboni za Yehova zinaikidwa m’ndende, kuzunzidwa ndi kuphedwa cifukwa cokana kuloŵelela m’ndale za dziko. Bishopu wina wa ku Germany analemba kuti: “Iwo ayeneladi kunena kuti cipembedzo cao cokha n’cimene cinakanitsitsa kumenya nao nkhondo mu ulamulilo wa Hitler.”
“[Mboni za Yehova] zili ndi makhalidwe abwino kwambili. Timalakalaka kugwilitsila nchito anthu amenewa pa nkhani za ndale, koma sizingatheke. . . . Zimalemekeza maboma olamulila koma zimakhulupilila kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ukhoza kuthetsa mavuto onse a mtundu wa anthu.”—Anatelo Nová Svoboda, wofalitsa nkhani ku Czech Republic.
Ngakhale n’conco, sitidzipatula pa anzathu. Yesu anapemphelela ophunzila ake kuti: “Sindikupempha kuti muwacotse m’dziko, koma kuti muwayang’anile kuopela woipayo.” (Yohane 17:15) Mwina mumationa tikugwila nchito, tikupita kusukulu, ndi kugula zinthu m’dela limene timakhala.