NSANJA YA MLONDA Na. 1 2017 | Mungacite Ciani Kuti Mupindule na Zimene Muŵelenga m’Baibo?
MUGANIZA BWANJI?
Kodi Baibo ni yothandiza masiku ano kapena si yothandiza? Baibo imayankha yokha kuti: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16, 17.
Nsanja ya Mlonda iyi ifotokoza ena mwa malangizo othandiza opezeka m’Baibo, ndipo ikambanso zimene mungacite kuti mupindule na zimene mumaŵelenga m’Baibo.
NKHANI YA PACIKUTO
N’cifukwa Ciani Mufunika Kuŵelenga Baibo?
Kodi anthu ambili apindula bwanji na kuŵelenga Baibo?
NKHANI YA PACIKUTO
Mungayambe Bwanji Kuŵelenga Baibo?
Mfundo zisanu zimene zingapangitse kuti kuŵelenga Baibo kukhale kosavuta ndi kokondweletsa.
NKHANI YA PACIKUTO
Mungacite Ciani Kuti Kuŵelenga Baibo Kuzikukondweletsani?
Mabaibo, zipangizo zamakono, zida, na njila zosiyana-siyana zoŵelengela Baibo, zingathandize kuti kuŵelenga Baibo kukhale kokondweletsa.
NKHANI YA PACIKUTO
Kodi Baibo Inganithandize Bwanji mu Umoyo Wanga?
Buku lakale limeneli lili na malangizo othandiza kwambili.
BAIBO IMASINTHA ANTHU
N’nali Kuopa Imfa
Nthawi ina Yvonne Quarrie anadzifunsa kuti, “N’cifukwa ciani nili na moyo?” Yankho limene anapeza linamucititsa kusintha umoyo wake.
TENGELANI CIKHULUPILILO CAWO
‘Mulungu Anakondwela Naye’
Kodi musamalila banja kapena mukumana na mavuto cifukwa cocita zinthu zabwino? Ngati n’conco, ndiye kuti muphunzila zambili pa cikhulupililo ca Inoki.
Kodi N’kuphonya Cabe pa Kamvedwe?
Uthenga wa m’Baibo ni wofunika ngako ndipo tifunika kuumvetsetsa. Mungacite ciani kuti muumvetsetse?
Kodi Baibo Imakamba Ciani?
Baibo imakamba zimene zipangitsa mavuto komanso mmene mavutowo adzathela.