Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO MUNGACITE CIANI KUTI MUPINDULE NA ZIMENE MUŴELENGA M’BAIBO?

Kodi Baibo Inganithandize Bwanji mu Umoyo Wanga?

Kodi Baibo Inganithandize Bwanji mu Umoyo Wanga?

Baibo si buku wamba. Ili na malangizo ocokela kwa Mlengi wathu. (2 Timoteyo 3:16) Uthenga wake ungatithandize ngako pa umoyo wathu. Ndipo Baibo imati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheberi 4:12) Baibo ingatithandize pa umoyo wathu m’njila ziŵili zikulu-kulu. Coyamba, imatipatsa malangizo amene angatithandize pa umoyo wathu wa tsiku na tsiku, ndipo caciŵili, imatithandiza kudziŵa Mulungu ndi malonjezo ake.—1 Timoteyo 4:8; Yakobo 4:8.

Ingakuthandizeni pa umoyo wanu tsopano. Baibo imathandiza ngakhale pa nkhani za umwini. Imapeleka malangizo othandiza pa nkhani izi:

  • Ubwenzi wathu na ena.—Aefeso 4:31, 32; 5:22, 25, 28, 33.

  • Thanzi lathu.—Salimo 37:8; Miyambo 17:22.

  • Makhalidwe athu.—1 Akorinto 6:9, 10.

  • Nchito na Ndalama.—Miyambo 10:4;28:19; Aefeso 4:28. *

Banja lina lacicepele ku Asia linayamikila ngako malangizo a m’Baibo. Mofanana ndi anthu ambili amene ndi atsopano m’cikwati, zinali kuwavuta kuti azigwilizana cifukwa ca kusiyana umunthu. Vuto lina linali lakuti sanali kukambitsana momasuka. Koma anayamba kutsatila zimene anaphunzila m’Baibo. Kodi panali zotsatilapo zabwanji? Mwamuna wa m’banjali, dzina lake Vicent anati: “Zimene n’naŵelenga m’Baibo zinanithandiza kucita zinthu mwacikondi polimbana ndi mavuto m’banja lathu. Cifukwa cotsatila malangizo a m’Baibo, lomba tili na umoyo wacimwemwe.” Mkazi wake, Annalou, anavomeleza ndipo anati: “Kuŵelenga zitsanzo za m’Baibo kwatithandiza. Lomba nimakhala wokondwela m’banja ndipo tili na zolinga zabwino pa umoyo.”

Kudziŵa Mulungu. Kuwonjezela pa zimene Vicent anakamba zokhudza banja lawo, iye anakambanso kuti: “Cifukwa ca kuŵelenga Baibo, manje nimaona kuti nili pafupi maningi na Yehova kuposa kale.” Zimene Vicent anakamba zionetsa mfundo yofunika yakuti, Baibo ingakuthandizeni kum’dziŵa bwino Mulungu. Ngati muŵelenga Baibo, mudzapindula na malangizo ocokela kwa Mulungu, ndiponso mudzamudziŵa monga mnzanu. Cinanso, mudzaona kuti iye amatiuza za tsogolo labwino, nthawi imene tidzakondwela na “moyo weni-weni” kapena kuti moyo wosatha. (1 Timoteyo 6:19) Palibe buku lina lililonse limene lingatiuze za tsogolo labwino ngati limeneli.

Ngati muyamba kuŵelenga Baibo ndi kupitiliza kutelo, inunso mudzakhala na umoyo wabwino ndiponso mudzamudziŵa Mulungu. Komabe, n’kutheka kuti pamene muiŵelenga mudzakhala na mafunso ambili. Ndipo ngati muli na funso, kumbukilani citsanzo cabwino ca nduna ina ya ku Itiyopiya imene inakhalako zaka 2,000 zapitazo. Iyo inali na mafunso ambili okhudza Baibo. Itafunsidwa ngati inali kumvetsetsa zimene inali kuŵelenga, inayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulila?” * Nduna imeneyi inalandila thandizo kucokela kwa wophunzila wa Yesu, dzina lake Filipo, amene anali mphunzitsi wofikapo wa Mau a Mulungu. (Machitidwe 8:30, 31, 34) Mofanana ndi nduna imeneyi, inunso ngati mufuna kudziŵa zambili zokhudza Baibo, tikupemphani kuti mutumize pempho lanu pa webusaiti ya www.ps8318.com kapena mulembele pa iliyonse ya maadresi amene ali m’magazini ino. Mungaonanenso na Mboni za Yehova kufupi na kwanu kapena kupita ku Nyumba ya Ufumu m’dela lanu. Bwanji osayamba kuŵelenga Baibo lelo ndi kulola kuti ikuthandizeni kukhala na umoyo wabwino?

Ngati nthawi zina mumakayikila kuti Baibo imakamba zoona, onani vidiyo yaifupi yakuti Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona? Mungaipeze mwa kucita skani QR khodi iyi kapena mungapite pa jw.org, ndi kulemba dzina la vidiyo imeneyi pa malo ofufuzila

^ par. 8 Kuti mupeze zitsanzo zina za malangizo othandiza a m’Baibo, onani pa webusaiti ya jw.org, pa cigawo cakuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA> KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO pa webusaiti ya Chichewa.

^ par. 11 Onaninso nkhani yakuti “Kodi N’kuphonya Cabe pa Kamvedwe?