Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Amishonale Akutumizidwa “Mpaka Kumalekezelo a Dziko Lapansi”

Amishonale Akutumizidwa “Mpaka Kumalekezelo a Dziko Lapansi”

JUNE 1, 2021

 Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Masiku ano, Mboni za Yehova zikugwila nchito imeneyi mokangalika. Komabe, m’madela ena a padziko lapansi, kuphatikizapo madela ena akulu-akulu, uthenga wabwino ukalibe kulalikidwa mokwanila. Ndipo m’maiko ena muli Mboni zocepa. (Mateyu 9:37, 38) Kodi tikucita zotani kuti tifikile anthu ambili mmene tingathele?

 Pothandiza kuti nchito imene Yesu analamula icitike, Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova, imatumiza amishonale a m’munda kumadela amene kuli alengezi a Ufumu ocepa padzikoli. Pano tikamba, pali amishonale a m’munda 3,090 padziko lonse lapansi. a Ambili analoŵa sukulu yophunzitsa Baibo, mwacitsanzo Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Amishonale amadzipeleka kucoka kwawo kupita kudziko lina. Cifukwa cakuti amishonale amenewa ni okhwima mwauzimu, anaphunzitsidwa bwino, ndipo amadziŵa zambili, athandiza kufalitsa uthenga wabwino komanso amapeleka citsanzo cabwino kwa atumiki acatsopano.

M’bale amene ni mmishonale akupatsa mwayi mlongo wopeleka ndemanga pa misonkhano ya mpingo.

Kuthandiza Amishonale Kuti Nawonso Azithandiza Ena

 Pa ofesi ya nthambi iliyonse, Ofesi Yosamalila Atumiki Ali M’munda ya dipatimenti ya utumiki mogwilizana na Komiti ya Nthambi, imasamalila amishonale pa zosoŵa zawo monga nyumba, thandizo la zacipatala, na kandalama kocepa kowathandiza pa zosoŵa za tsiku na tsiku. M’caka cautumiki ca 2020, Mboni za Yehova zinaseŵenzetsa ndalama zokwana madola 27 miliyoni a ku America posamalila amishonale. Cifukwa ca thandizo limeneli, amishonale amaika mtima wawo wonse na mphamvu zawo zonse pa nchito yolalikila komanso polimbikitsa mipingo yawo.

Amishonale amathandiza kulimbitsa mipingo

 Kodi amishonale a m’munda athandiza bwanji pa nchito yolalikila? M’bale Frank Madsen wa m’Komiti ya Nthambi ku Malawi anati: “Cifukwa cakuti amishonale ni olimba mtima komanso aluso, athandiza mipingo kuyamba kulalikila m’magawo ovuta, monga madela amene kuli nyumba za mipanda yokhala na mageti komanso kumene anthu amakamba zinenelo zina. Komanso khama lawo lophunzila zinenelo za kuno na cikhalidwe, limalimbikitsa ena. Cinanso, amalimbikitsa acinyamata kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Tiyamikila Yehova cifukwa cotipatsa amishonale.”

 M’bale wa m’Komiti ya Nthambi ya dziko lina anati: “Amishonale amapeleka umboni wakuti anthu a Yehova ni ogwilizana kulikonse padzikoli. Ngakhale anthu amene si Mboni amaona kuti sindife ogaŵikana cifukwa ca cikhalidwe cathu, koma kuti ziphunzitso za m’Baibo zatithandiza kukhala gulu la abale logwilizana.”

 Kodi amishonale a m’munda amawathandiza bwanji ofalitsa a m’mipingo yawo? M’bale Paulo, wa ku Timor-Leste, amayamikila kukhala na amishonale mu mpingo wawo. Iye anati: “Kuno kwathu n’kotentha kwambili. Ngakhale kuti amishonalewa anacokela ku dziko lozizila, saopa kulalikila cifukwa ca nyengo ya kuno. Nthawi zonse amapezeka pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki m’maŵa. Nthawi zambili nimawaona akupita ku maulendo obweleza masana dzuŵa lili phwee!, komanso madzulo. Iwo athandiza ambili kuphunzila coonadi, kuphatikizapo ine. Ni okangalika ndipo amaseŵenzetsa moyo wawo wonse potumikila Yehova, ndipo izi zimalimbikitsanso ofalitsa onse mu mpingo kutumikila Yehova na mtima wawo wonse.”

 Ketti, mpainiya wanthawi zonse ku Malawi anafotokoza mmene banja la amishonale linathandizila banja lake. Anati: “Pamene banja la amishonale linabwela mu mpingo mwathu, ndine nekha n’nali Mboni m’banja mwathu. Koma banjalo linanithandiza ndipo linayamba kugwilizana kwambili na banja lathu. Citsanzo cawo cabwino cinathandiza ana anga kuona kuti kutumikila Yehova kumathandiza munthu kukhala na umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa. Cifukwa colimbikitsidwa na amishonale amenewa, atsikana anga atatu tsopano akucita upainiya wanthawi zonse, ndipo mwamuna wanga anayamba kupezeka kumisonkhano.”

 Kodi ndalama zosamalila amishonale a m’munda zimacokela kuti? Zimacokela pa zopeleka za nchito ya padziko lonse. Zambili mwa zopeleka zimenezi zimapelekedwa kupitila pa donate.ps8318.com. Timayamikila kwambili zopeleka zanu zimene mumapeleka mowolowa manja.

a Amishonale amenewa amatumizidwa ku mipingo imene kuli alaliki a uthenga wabwino ocepa. Amishonale ena 1,001 ali mu utumiki woyendela madela.

Amishonale amathandiza polalikila uthenga wabwino m’madela amene kuli Mboni zocepa kwambili