Kodi Mungacite Ciyani Ngati Mumasoŵa Woceza Naye?
“Pafupifupi hafu ya acikulile ku America amasoŵa oceza nawo, ndipo izi zimacitikila kwambili acinyamata.”—Linatelo buku lakuti Our Epidemic of Loneliness and Isolation: The U.S. Surgeon General’s Advisory on the Healing Effects of Social Connection and Community, 2023.
Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linalengeza kuti lakhazikitsa nthambi yatsopano yochedwa Commission on Social Connection, imene colinga cake ni kugwebana na vuto la kusungulumwa, limene lakhala mlili wofunika kuthetsedwa mwamsanga. Colinga cina ca nthambiyi ni kulimbikitsa ubwenzi pakati pa anthu, komanso kupeza mwamsanga njila zothetsela vuto la kusungulumwa m’maiko onse, olemela na osauka omwe.—Lipoti la Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse, la pa November 15, 2023.
Baibo imapeleka malangizo otithandiza kukhala paubwenzi wabwino na anthu ena.
Mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni
Cepetsani zocita zimene zingapangitse kuti muzidzipatula. Zocita zimenezi ziphatikizapo kuseŵenzetsa kwambili soshomidiya. M’malomwake, muziyesetsa kupeza nthawi yoceza na anthu ena pamasom’pamaso. Mukatelo, mudzapeza mabwenzi enieni.
Mfundo ya m’Baibo: “Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.
Pezani mipata yothandiza ena. Tikamacitila ena zabwino, ubwenzi wathu na iwo umalimba ndipo timapeza cimwemwe.
Mfundo ya m’Baibo: “Kupatsa kumaticititsa kukhala osangalala kwambili kuposa kulandila.”—Machitidwe 20:35.
Fufuzani pa webusaiti yathu kuti mupeze mfundo zina za m’Baibo zimene zingakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi na ena.