Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Halfpoint Images/Moment via Getty Images

KHALANI MASO!

Mkulu Wina wa za Umoyo Wacenjeza za Mavuto Amene Acinyamata Amakumana Nawo pa Soshomidiya—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Mkulu Wina wa za Umoyo Wacenjeza za Mavuto Amene Acinyamata Amakumana Nawo pa Soshomidiya—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Pa May 23, 2023, mkulu wina wa za umoyo ku United States anacenjeza anthu kuti acinyamata ambili akukumana na mavuto cifukwa cogwilitsa nchito soshomidiya.

  •   “Ngakhale kuti soshomidiya ingakhale yothandiza kwa ana ena komanso acinyamata, pali maumboni oculuka oonetsa kuti ingawonongenso kwambili kaganizidwe kawo na thanzi lawo.”—Inatelo lipoti yakuti Social Media and Youth Mental Health: The U.S. Surgeon General’s Advisory, 2023.

 M’lipotilo anachulamo za kafukufuku amene aonetsa kuti vutoli lafika podetsa nkhawa.

  •   Acinyamata a zaka 12 mpaka 15 “amene amaseŵenzetsa soshomidiya kwa maola oposa atatu pa tsiku, amakhala pa ciwopsezo codwala matenda a maganizo kuwilikiza kaŵili, kuphatikizapo zizindikilo za kupanikizika maganizo na nkhawa.”

  •   Acinyamata a zaka 14, “amene amagwilitsa nchito kwambili soshomidiya, amalephela kugona, amavutitsidwa pa intaneti, sasangalala ni maonekedwe awo, amadzikayikila komanso amakhala na zizindikilo zambili za kupsinjika maganizo. Ndipo izi zimacitikila kwambili atsikana kuposa anyamata.”

 Kodi makolo angawateteze bwanji ana ana awo ku mavuto amenewa? Baibo imapeleka malangizo othandiza.

Zimene makolo angacite

 Citamponi kanthu. Monga makolo, onani ngati mwana wanu angamaiseŵenzetse soshomidiya kapena ayi, ndipo ganizilani kuopsa koiseŵenzetsa.

 Ngati mwamulola mwana wanu kuseŵenzetsa soshomidiya, ganizilani mavuto amene angakhalepo ni kumaona zimene mwana wanu amacita pa intaneti. Motani?

 Tetezani mwana wanu ku zinthu zovulaza. Phunzitsani mwana wanu kuzindikila zinthu zovulaza za pa intaneti na kuzipewa.

 Muikileni malile. Mwacitsanzo, khazikitsani malamulo a nthawi imene mwana wanu angaseŵenzetse soshomidiya komanso utali wake.

  •   Mfundo ya m’Baibo ‘Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela ni monga anthu anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.’—Aefeso 5:15, 16.

  •   Seŵenzetsani vidiyo ya tukadoli yakuti Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti pothandiza mwana mwanu kumvetsa cifukwa cake kumuikila malile n’kofunika.