KHALANI MASO!
Caka ca 2023 Cacititsa Anthu Ambili Kukhala na Nkhawa—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?
Zocitika za padziko lonse mu 2023 zapeleka umboni wosatsutsika wakuti tikukhala m’nthawi imene Baibo imacha “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1) Onani kuti zimene zikucitika padziko lonse n’zimenenso Baibo inakambilatu kuti zidzacitika m’nthawi yathu ino.
Baibo inakambilatu zocitika za padziko lonse
“Nkhondo ndi malipoti a nkhondo.”—Mateyu 24:6.
“Zaciwawa zikuwonjezeka m’malo ambili padziko lapansi.” a
Onani nkhani yakuti “Kodi Ndani Adzapulumutsa Anthu?” na yakuti “Ndalama Zopitilila $2 Tililiyoni Zawonongedwa pa Zida Zankhondo.”
“Zivomelezi mʼmalo osiyanasiyana.”—Maliko 13:8.
“Kucokela ku ciyambi ca caka ca 2023, padziko lonse pacitika zivomezi zamphamvu kwambili zokwana 13. Ici ni caka cimene kwacitika zivomezi zambili zamphamvu zedi.” b
Onani nkhani yakuti “Zivomezi Zamphamvu Zisakaza ku Turkey na ku Syria.”
“Zinthu zoopsa.”—Luka 21:11.
Dziko lapansi likutentha kwambili, moti tsopano likutentha koopsa kuposa kale lonse.—António Guterres, Kalembela Wamkulu wa Bungwe la Untied Nations. c
Onani nkhani yakuti “Kutentha Koopsa pa Dziko Lonse mu 2023.”
“Njala.”—Mateyu 24:7.
“Caka ca 2023 cakhala covuta kwambili kwa anthu amene amavutikila kupeza cakudya ca banja lawo.” d
Onani nkhani yakuti “Njala Padziko Lonse Yawonjezeka Cifukwa ca Nkhondo Komanso Kusintha kwa Nyengo.”
“Nthawi yapadela komanso yovuta.”—2 Timoteyo 3:1.
“Padziko lonse, munthu mmodzi pa anthu 8 alionse akudwala matenda a maganizo.” e
Onani nkhani yakuti “Ciŵelengelo ca Acinyamata Odwala Matenda a Maganizo Cikuculuka.”
Kodi tiyembekezela zotani mu 2024?
Palibe amene adziŵa zimene zidzacitika mu 2024. Koma zocitika za padzikoli zionetsa kuti posacedwa Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma lakumwamba, udzaloŵa m’malo maboma onse a anthu ndipo udzacotsapo zonse zimene zimayambitsa mavuto na nkhawa.—Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:4.
Koma pamene tikuyembekezela nthawiyo, tiyenela kudalila Mulungu kuti azitithandiza tikakhala na nkhawa. Baibo imati:
“Ndikamacita mantha, ndimadalila inu.”—Salimo 56:3.
Kodi tingaonetse bwanji kuti timamudalila Mulungu? Tikupemphani kuti muphunzile zambili za lonjezo la m’Baibo la tsogolo lopanda mavuto. Yambani maphunzilo a Baibo okambilana aulele kuti muone mmene malonjezo a m’Baibo angakuthandizileni limodzi na banja lanu.
a Foreign Affairs, “A World at War: What Is Behind the Global Explosion of Violent Conflict?” by Emma Beals and Peter Salisbury, October 30, 2023.
b Earthquake News, “Year 2023: Number of Major Earthquakes on Course for Record,” May, 2023.
c United Nations, “Secretary-General’s Opening Remarks at Press Conference on Climate,” July 27, 2023.
d World Food Programme, “A Global Food Crisis.”
e World Health Organization, “World Mental Health Day 2023,” October 10, 2023.