Nyimbo 89
Yehova Akutipempha Mokoma Mtima Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”
(Miyambo 27:11)
1. Mwana wanga
Undipatse mtima wako
Adzionere yekha
Wonditonzayo.
Nditumikire uli
Wachinyamata,
Onse adziwe kuti
Umandikonda.
(KOLASI)
Mwana wanga wokondedwawe
Khalatu wanzeru chonde.
Usankhe kunditumikira,
Utero ndi mtima wonse.
2. Usangalale ndi
Kunditumikira,
Ngakhale ukapunthwa
Ndidzakudzutsa.
Wina aliyense
Angakulakwire,
Usadere nkhawa
Sindingakusiye.
(KOLASI)
Mwana wanga wokondedwawe
Khalatu wanzeru chonde.
Usankhe kunditumikira,
Utero ndi mtima wonse.
(Onaninso Deut. 6:5; Mlal. 11:9; Yes. 41:13.)